Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 30:1-31

30  “Tsopano anthu amene ndi ana aang’ono poyerekeza ndi ine,+ Akundiseka.+ Anthu amene abambo awo sindikanalola Kuwaika pamodzi ndi agalu oweta nkhosa zanga.   Ngakhale mphamvu za manja awo zinali zopanda ntchito kwa ine. Ndiponso nyonga zawo zatha.+   Chifukwa cha njala ndiponso kusowa, iwo ali ngati akufa. Amatafuna dera lopanda madzi,+ Limene dzulo kunali mphepo yamkuntho ndi chiwonongeko.   Iwo anali kubudula chitsamba cha mchere m’tchire, Ndipo mizu ya timitengo ndiyo inali chakudya chawo.   Ankathamangitsidwa m’mudzi.+ Anthu ankawakuwiza ngati mbala.   Iwo amakhala m’malo otsetsereka a m’zigwa,* M’maenje a m’nthaka ndi m’matanthwe.   Amalira mokuwa ali pakati pa zitsamba, Amaunjikana pansi pa zitsamba zaminga.   Ana a munthu wopusa,+ komanso ana a munthu wopanda dzina. Iwo akwapulidwa n’kuthamangitsidwa  m’dziko.   Tsopano ine ndakhala mutu wa nyimbo yawo,+ Ndipo kwa iwo ndine chinthu choseketsa.+ 10  Akunyansidwa nane, ndipo akukhala patali ndi ine.+ Sakuzengereza kundilavulira kumaso.+ 11  Pakuti iye anakhwefula chingwe cha uta wanga n’kunditsitsa, Ndipo zingwe za pakamwa pa hatchi,* iwo anazisiya zomasula chifukwa cha ine. 12  Iwo aimirira kudzanja langa lamanja ngati kagulu ka anthu oipa. Amasula mapazi anga, Koma andiikira zopinga zovulaza kwambiri.+ 13  Iwo awononga njira zanga. Anangondibweretsera mavuto,+ Popanda aliyense wowathandiza. 14  Amabwera ngati akudutsa pampata waukulu, Amakokoloka ndi madzi a mvula yamkuntho. 15  Zoopsa zadzidzidzi zandibwerera. Ulemerero wanga wachoka ngati kuti wauluzika ndi mphepo, Ndipo chipulumutso changa chapita ngati mtambo. 16  Tsopano moyo wanga ukukhuthuka mwa ine.+ Masiku a masautso+ ali pa ine. 17  Usiku mafupa anga+ amabooledwa n’kugwa pansi. Zowawa zonditafuna sizipuma.+ 18  Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu, chovala* changa chimasintha, Ndipo chimandithina ngati kolala yothina. 19  Iye wanditsitsa mpaka m’dothi, Moti ndikukhala ngati fumbi ndi phulusa. 20  Ndimafuulira kwa inu kuti mundithandize, koma simundiyankha.+ Choncho ndaimirira kuti mundimvere. 21  Mwasintha n’kukhala wankhanza kwa ine.+ Ndi mphamvu yonse ya dzanja lanu, mwandisungira chidani. 22  Mwandiuluza ndi mphepo, mwandinyamula nayo. Kenako mwandisungunula ndi mkokomo wake. 23  Pakuti ndikudziwa bwino kuti mudzandibwezera ku imfa,+ Kunyumba yosonkhanako aliyense wamoyo. 24  Koma palibe amene amatambasula dzanja lake polimbana ndi mulu wa zinthu zowonongeka.+ Komanso pa kuwonongeka kwa munthu, palibe amene amapempha thandizo la zinthu zimenezo. 25  Ndithu, ndalirira munthu amene zinthu sizikumuyendera bwino.+ Moyo wanga walirira munthu wosauka.+ 26  Ngakhale kuti ndinkadikirira zabwino, zoipa n’zimene zinabwera.+ Ndinkadikirira kuwala, koma kunabwera mdima. 27  Matumbo anga anawira ndipo sanakhale chete. Masiku a masautso anandipeza. 28  Ndinayendayenda mwachisoni+ pamene kunalibe kuwala. Ndinaimirira mumpingo, ndipo ndinkangofuula popempha thandizo. 29  Ndinakhala m’bale wake wa mimbulu, Ndi mnzawo wa ana aakazi a nthiwatiwa.+ 30  Khungu langa linakhala lakuda+ ndipo linayoyoka pathupi panga. Mafupa anga anatentha chifukwa chouma. 31  Zeze wanga anangokhala wolirirapo, Ndipo chitoliro changa chinangokhala choimbapo mawu a anthu olira.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Ena amati “hosi,” kapena “kavalo.”
N’kutheka kuti akutanthauza “khungu.”