Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 3:1-26

 3  Pambuyo pa zimenezi m’pamene Yobu anatsegula pakamwa pake n’kuyamba kutemberera tsiku limene anabadwa.+  Tsopano Yobu anati:   “Liwonongeke tsiku limene ndinabadwa,+ Ndiponso usiku umene wina ananena kuti, ‘Mwamuna wamphamvu wapangika m’mimba.’   Tsiku limenelo likhale mdima. Mulungu asaliganizirenso ali kumwamba, Ndipo kuwala kusalifikire.   Mdima wandiweyani ulitenge. Mtambo wa mvula uliphimbe. Zinthu zimene zimadetsa tsiku ziliopseze.+   Usiku umenewo utengedwe ndi mdima.+ Usasangalale pakati pa masiku a pachaka, Pachiwerengero cha miyezi, usalowe nawo.   Ndithu usiku umenewo ukhale wosabereka. Mfuu yachisangalalo isamveke usikuwo.+   Otemberera masiku alitemberere tsikulo, Iwo amene ali okonzeka kudzutsa ng’ona.*+   Nyenyezi za m’chisisira cha m’mawa mwake zizime. Lidikire kuwala koma lisakuone, Ndipo lisaone kuwala kwa m’bandakucha. 10  Chifukwa silinatseke zitseko za mimba ya mayi anga,+ Kuti ndisaone mavuto. 11  Bwanji sindinafere m’chiberekero?+ Bwanji sindinamwalire nditangotuluka m’mimba? 12  N’chifukwa chiyani mawondo anakumana nane, Ndipo mabere+ ndinakumana nawo chifukwa chiyani kuti ndiyamwe? 13  Panopa bwenzi nditagona kuti ndisasokonezedwe,+ Bwenzi ndili m’tulo pa nthawiyo, ndipo bwenzi pano ndikupuma+ 14  Limodzi ndi mafumu ndi aphungu a padziko lapansi,+ Amene anadzimangira malo omwe tsopano ali bwinja.+ 15  Kapena ndi akalonga amene ali ndi golide, Amene amadzaza nyumba zawo ndi siliva. 16  Kapena ngati pakati pomwe papita pachabe mosadziwa,+ bwenzi ine kulibe, Mofanana ndi ana amene sanaone kuwala.+ 17  Kumandako oipa asiya kusautsika,+ Ndipo kumeneko anthu omwe mphamvu zawo zatha, akupuma.+ 18  Akaidi onse pamodzi ali pa mtendere. Iwo samvanso mawu a munthu wowakusira ku ntchito.+ 19  Aang’ono ndi aakulu amakhala chimodzimodzi kumeneko,+ Ndipo kapolo amamasuka kwa mbuye wake. 20  N’chifukwa chiyani Mulungu amapereka kuwala kwa munthu amene ali ndi mavuto, Ndiponso moyo kwa opwetekedwa mtima?+ 21  N’chifukwa chiyani anthu ena amadikirira imfa, koma siwabwerera,+ Ngakhale amakumba pansi poifunafuna, kuposa mmene amakumbira chuma chobisika? 22  Amenewa amasangalala kwadzaoneni, Amakondwera akapeza manda. 23  N’chifukwa chiyani Mulungu amapereka kuwala kwa mwamuna wamphamvu amene njira yake yabisika,+ Amene Mulungu akum’pingapinga?+ 24  Pakuti chakudya changa chimabwera limodzi ndi kuusa moyo,*+ Ndipo ngati madzi, kubuula kwanga kumakhuthuka.+ 25  Chinthu chochititsa mantha chimene ndinali kuchita nacho mantha, chandibwerera, Ndipo chimene ndinali kuchiopa chabwera kwa ine.+ 26  Sindinali wopanda nkhawa kapena wopanda mavuto, Komanso sindinali pa mtendere, komabe zosautsa mtima zandibwerera.”

Mawu a M'munsi

M’Chiheberi, “Leviyatani.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.