Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 29:1-25

29  Yobu anayambanso kulankhula mwandakatulo kuti:   “Ndikulakalaka ndikanakhala ngati mmene ndinalili m’miyezi yakale,+ Ngati mmene ndinalili m’masiku amene Mulungu anali kundiyang’anira,+   Pamene anachititsa nyale yake kuwala pamutu panga, Pamene ndinkayenda mu mdima iye akundiunikira ndi kuwala kwake.+   Ngati mmene ndinalili m’masiku amene ndinali mnyamata,+ Pamene Mulungu anali bwenzi langa lapamtima, ndipo anali pahema wanga,+   Pamene Wamphamvuyonse anali nane, Pamene antchito anga onse anandizungulira,   Pamene ndinkasambitsa mapazi anga m’mafuta a mkaka, Ndiponso pamene miyala inkanditulutsira mitsinje ya mafuta.+   Ndikapita kuchipata cha mzinda,+ Ndinkakonzako malo anga okhala pabwalo la mzinda.+   Anyamata akandiona, ankabisala. Ngakhale okalamba ankanyamuka n’kuima chilili.+   Akalonga ankabweza mawu, Ndipo ankagwira pakamwa.+ 10  Mawu a atsogoleri ankabisika, Ndipo lilime lawo linkamamatira m’kamwa mwawo.+ 11  Khutu likamva, linkanena kuti ndine wodala, Ndipo diso likaona, linkandichitira umboni. 12  Pakuti ndinkapulumutsa wosautsika wopempha thandizo,+ Ndiponso mwana wamasiye* ndi aliyense amene analibe womuthandiza.+ 13  Madalitso+ a munthu amene watsala pang’ono kuwonongedwa ankabwera kwa ine, Ndipo ndinkasangalatsa mtima wa mkazi wamasiye.+ 14  Ndinkavala chilungamo, ndipo icho chinkandiveka.+ Chilungamo changa chinali ngati malaya akunja odula manja, ndi nduwira.* 15  Ndinali ngati maso kwa wakhungu,+ Ndipo ndinali mapazi kwa wolumala. 16  Ndinali bambo weniweni kwa osauka,+ Ndipo mlandu wa munthu amene sindinali kumudziwa ndinkaufufuza.+ 17  Ndinkaphwanya nsagwada za wochita zoipa,+ Ndipo wogwidwa, ndinkamulanditsa kukamwa kwa wochita zoipayo. 18  Ndinkati, ‘Ndidzafera m’chisa changa,+ Ndidzachulukitsa masiku anga ngati mchenga.+ 19  Muzu wanga ndi wotseguka kuti uyamwe madzi,+ Ndipo mame akhala usiku wonse panthambi yanga. 20  Ulemerero wanga ndili nawobe, Ndipo uta umene uli m’manja mwanga uziponya mivi mobwerezabwereza.’ 21  Anthu ankandimvera ndipo ankandidikirira. Ankakhala phee kuti amve malangizo anga.+ 22  Ndikamaliza kulankhula, iwo sankalankhulanso. Ndipo mawu anga ankadonthera pa iwo.+ 23  Iwo ankandidikirira ngati akudikira mvula,+ Ndipo ankayasama kuti m’kamwa mwawo mugwere mvula yomalizira.+ 24  Ndinkawamwetulira, koma iwo sankakhulupirira, Ndipo kuwala kwa pankhope+ panga sankakuzimitsa. 25  Ndinkawasankhira njira, ndipo ndinkakhala pansi patsogolo pawo. Ndinali ngati mfumu pakati pa asilikali ake,+ Ndiponso ngati wotonthoza olira.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”
“Nduwira” ndi chovala chansalu chakumutu chimene amachimanga ngati duku.