Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 28:1-28

28  “Zoonadi, siliva ali ndi malo amene amapezekako, Ndiponso kuli malo a golide yemwe amayengedwa.+   Chitsulo chimatengedwa m’fumbi,+ Ndipo mkuwa umakhuthulidwa kuchokera m’miyala.   Anthu aika malire a mdima, Ndipo amafufuza miyala mpaka pamapeto,+ Mu mdima wandiweyani.   Amakumba mgodi kutali ndi kumene anthu amakhala monga alendo,+ Kumalo oiwalika, kutali ndi phazi. Anthu ena amatsikira pansi n’kumagwira ntchito cholendewera.   Padziko lapansi pamamera chakudya,+ Koma pansi pake pasandulizidwa ngati kuti pasakazidwa ndi moto.   M’miyala yake mumapezeka miyala ya safiro,+ Ndipo dzikolo lili ndi fumbi la golide.   Imeneyi ndi njira imene mbalame yodya nyama+ sikuidziwa, Ndipo diso la mphamba+ silinaionepo.   Zilombo zamphamvu zakutchire sizinapondepondemo, Mkango wamphamvu sunayendeyendemo.   Anthu amatenga mwala wolimba, Amagwetsa mapiri kuyambira pansi penipeni. 10  M’miyala amakumbamo ngalande zodzaza ndi madzi,+ Ndipo maso awo aona zinthu zonse zamtengo wapatali. 11  Kumalo kumene kumayambira mitsinje, amakumbako madamu.+ Ndipo chinthu chobisika amachibweretsa poyera. 12  Koma kodi nzeru zingapezeke kuti?+ Ndipo kumvetsa zinthu, malo ake ali kuti? 13  Munthu sadziwa mtengo wake,+ Ndipo nzeru sizipezeka m’dziko la amoyo. 14  Madzi akuya anena kuti, ‘Sizili mwa ine.’ Nayonso nyanja yanena kuti, ‘Sizili ndi ine.’+ 15  Golide woyenga bwino sangaperekedwe mosinthana nazo,+ Ndipo sangayeze siliva monga mtengo wake. 16  Sangazigule ndi golide wa ku Ofiri,+ Kapena mwala wosowa wa onekisi ndi wa safiro. 17  Golide ndi galasi sizingayerekezedwe ndi nzeru, Ndipo sangazisinthanitse ndi chiwiya chilichonse cha golide woyengeka bwino. 18  Mwala wamtengo wapatali wa korali+ ndi wa kulusitalo sizingayerekezedwe n’komwe ndi nzeruzo. Ndipo thumba lodzaza ndi nzeru ndi lamtengo wapatali kuposa thumba lodzaza ndi ngale.+ 19  Sizingayerekezedwe ndi miyala ya topazi+ ya ku Kusi, Ngakhale golide woyenga bwino sangagulire nzeru. 20  Koma kodi nzeru zimachokera kuti?+ Ndipo kumvetsa zinthu malo ake ali kuti? 21  Zabisika ngakhale kumaso kwa munthu aliyense wamoyo,+ Ndipo n’zobisika kwa zolengedwa zouluka m’mlengalenga. 22  Chiwonongeko ndi imfa zanena kuti, ‘Ndi makutu athu, tamva nkhani zokhudza nzeruzo.’ 23  Mulungu ndi amene amamvetsa njira zake,+ Ndipo iye ndiye amadziwa malo ake. 24  Pakuti iye amayang’ana kumapeto kwenikweni kwa dziko lapansi.+ Amaona pansi ponse pa thambo, 25  Kuti mphepo aipatse mphamvu.+ Ndipo iye amagawa madzi ndi choyezera.+ 26  Pamene ankapangira mvula lamulo,+ Ndiponso pamene ankapangira njira mtambo wa mvula ya mabingu, 27  M’pamene anaona nzeru n’kuyamba kulankhula zinthu zokhudza nzeruzo. Iye anazikonza n’kuzifufuza bwinobwino. 28  Ndiyeno anauza munthu kuti, ‘Tamvera, kuopa Yehova ndiko nzeru,+ Ndipo kupatuka pa choipa ndiko kumvetsa zinthu.’”+

Mawu a M'munsi