Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 27:1-23

27  Tsopano Yobu anayambanso kulankhula mwandakatulo+ kuti:   “Pali Mulungu wamoyo amene wandimana chilungamo,+Ndiponso pali Wamphamvuyonse wamoyo amene wachititsa moyo wanga kupweteka,   Pamene mpweya wanga udakali wonse mwa ine,Ndiponso pamene mzimu wa Mulungu udakali m’mphuno mwanga,   Milomo yanga sidzalankhula zopanda chilungamo,Ndipo lilime langa silidzalankhula zachinyengo.   Inetu sindingayerekeze n’komwe kunena kuti amuna inu ndinu olungama.Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.+   Ndagwira chilungamo changa ndipo sindichitaya.+Mtima wanga sudzandinyoza masiku anga onse.+   Mdani wanga akhale munthu woipa m’zonse,Ndipo wondiukira akhaledi wochita zoipa.   Kodi chiyembekezo cha wampatuko n’chiyani Mulungu akachotsa moyo wake,+Akamulanda moyo wake?+   Kodi Mulungu angamumvere kulira kwakeZowawa zikamugwera?+ 10  Kodi iye angasangalale ndi Wamphamvuyonse?Kodi angapemphere kwa Mulungu nthawi zonse? 11  Ndikuphunzitsani ndi thandizo la Mulungu amuna inu.Sindibisa maganizo a Wamphamvuyonse.+ 12  Nonsenutu mwaona masomphenya.Nanga n’chifukwa chiyani mukuoneka kuti ndinu opanda nzeru?+ 13  Gawo la munthu woipa lochokera kwa Mulungu,+Zomwe adzalandire kwa Wamphamvuyonse monga cholowa cha ozunza anzawo, ndi izi: 14  Ana ake akachuluka, amachulukira lupanga.Mbadwa zake sizidzakhala ndi chakudya chokwanira. 15  Opulumuka ake adzaikidwa m’manda pa nthawi ya mliri wakupha,Ndipo akazi awo amasiye sadzalira.+ 16  Iye akaunjika siliva ngati fumbi,Ndipo akakonza zovala zake ngati dothi, 17  Ngakhale akonze zovalazo, wolungama ndi amene adzazivale.+Ndipo silivayo, wosalakwa ndi amene adzam’tenge. 18  Iye wamanga nyumba yake ngati kadziwotche,Ndiponso ngati chisimba*+ chimene mlonda wamanga. 19  Adzagona ali wolemera, koma palibe chimene chidzasonkhanitsidwe.Adzatsegula maso ake, koma sipadzakhala kalikonse.+ 20  Zoopsa zadzidzidzi zidzam’tenga ngati madzi.+Usiku chimphepo chamkuntho chidzamuba ndithu. 21  Mphepo ya kum’mawa idzamunyamula n’kumusowetsa,+Ndipo idzamuchotsa pamalo pake.+ 22  Idzamukuntha, ndipo sidzamumvera chisoni.+Adzayesera kuthawa mphamvu ya mphepoyo koma sadzatha.+ 23  Anthu adzamuwombera m’manja monyoza.Ndipo adzamuimbira mluzu ali pamalo pake.

Mawu a M'munsi

Ena amati “khumbi,” kapena “chitala.”