Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 26:1-14

26  Tsopano Yobu anayankha kuti:   “Koma ndiyetu wathandiza munthu wopanda mphamvu! Ukuona ngati wapulumutsa dzanja lopanda nyonga,+   Walangiza munthu wopanda nzeru.+ Komanso ukuona ngati anthu ochuluka wawadziwitsa nzeru zopindulitsa.   Kodi wauza ndani mawu ako, Ndipo zimene ukunenazi zachokera kuti?   Akufa amangokhalira kunjenjemera Pansi pa nyanja ndi pansi pa zimene zili m’nyanjamo.+   Manda ndi ovundukuka pamaso pake,+ Ndipo malo a chiwonongeko n’ngosavundikira.   Iye anatambasula kumpoto pamwamba pa malo opanda kanthu,+ Ndipo anakoloweka dziko lapansi m’malere.   Iye anakulunga madzi m’mitambo yake,+ Moti mitamboyo sing’ambika pansi pa madziwo.   Anaphimba mpando wake wachifumu, Poukuta ndi mtambo wake.+ 10  Anaika malire ozungulira pamwamba pa madzi,+ Kumene kuwala kumakathera mu mdima. 11  Zipilala za kumwamba zimagwedezeka, Ndipo zimadabwa chifukwa cha kudzudzula kwake. 12  Ndi mphamvu zake wavundula nyanja,+ Ndipo ndi kuzindikira kwake wathyolathyola+ wachiwawa.*+ 13  Ndi mphepo yake wapukuta kumwamba,+ Ndipo dzanja lake labaya* njoka yokwawa.+ 14  Komatu zimenezi ndi kambali kakang’ono chabe ka zochita zake,+ Ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake. Koma kodi mabingu ake amphamvu, angawamvetse ndani?”+

Mawu a M'munsi

Mwina “wachiwawa” ameneyu ndi chilombo cha m’nyanja.
Ena amati “kulasa.”