Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 23:1-17

23  Tsopano Yobu anayankha kuti:   “Ngakhale lero, sindikusangalala ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanga. Chotero ndikudandaula.+ Dzanja langa likulemera chifukwa chakuti ndikuusa moyo.   Ndikanadziwa kumene ndingamupeze,+ Bwenzi nditapita kumalo kumene iye amakhala nthawi zonse.+   Bwenzi nditapita pamaso pake ndi nkhani yoti aweruze. M’kamwa mwanga bwenzi nditadzazamo mfundo zodziikira kumbuyo.   Bwenzi nditadziwa mawu amene amanena pondiyankha, Ndipo bwenzi nditaganizira zimene amandiuza.+   Kodi bwenzi iye atalimbana nane ndi mphamvu zambiri? Ayi ndithu! Iye akanandimvera.+   Kumeneko, wowongoka mtima adzathetsa nkhani zake ndi iye, Ndipo ine ndikanapulumuka kwa woweruza wanga mpaka kalekale.   Ndikapita kum’mawa, iye kulibe. Ndikabwerako, sindimuona.+   Ndimapita kumanzere kumene iye akugwira ntchito, koma sindimuona. Amatembenukira kudzanja lamanja, koma ine osamuona, 10  Pakuti iye amadziwa bwino njira imene ine ndimadutsa.+ Akamaliza kundiyesa, ndidzakhala ngati golide.+ 11  Mapazi anga amatsata mayendedwe ake. Ndasunga njira yake, ndipo sindipatukapo.+ 12  Sindisiya malamulo otuluka pakamwa pake.+ Ndasunga mosamala mawu a pakamwa pake+ kuposa zimene akufuna kuti ndichite. 13  Iye ali ndi maganizo amodzi, ndani angam’tsutse?+ Zimene moyo wake umalakalaka amazichita.+ 14  Iye adzachita zonse zimene wandikonzera,+ Ndipo zinthu zoterezi n’zambiri kwa iye. 15  N’chifukwa chake ndikusokonezeka chifukwa cha iye. Ndikaganizira za iye, ndikumachita mantha.+ 16  Mulungu wachititsa mantha mtima wanga.+ Wamphamvuyonse wandisokoneza,+ 17  Pakuti sindinaletsedwe kulankhula chifukwa cha mdima, Kapenanso chifukwa chakuti mdima wandiweyani waphimba nkhope yanga.

Mawu a M'munsi