Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 21:1-34

21  Tsopano Yobu anayankha kuti:   “Amuna inu, mvetserani mwatcheru mawu anga.Zimenezi zikhale zokutonthozani.   Ndilezereni mtima kuti ndilankhule.Ndikamaliza kulankhula, aliyense wa inu akhoza kuyamba kunyoza.+   Kodi ineyo ndauza munthu nkhawa zanga?Kapena n’chifukwa chiyani mzimu wanga sukukwiya?   Tembenuzirani nkhope zanu kwa ine n’kundiyang’ana modabwa,Ndipo muike dzanja lanu pakamwa.   Ndikakumbukira, zikundisokoneza maganizo,Ndipo thupi langa lonse likumanjenjemera.   N’chifukwa chiyani oipa amakhalabe ndi moyo,+Amakalamba komanso amalemera kwambiri?+   Ana awo akhazikika nawo limodzi pamaso pawo,Ndiponso mbadwa zawo zakhazikika iwo akuona.   Nyumba zawo zili pa mtendere, zosaopa chilichonse,+Ndipo ndodo ya Mulungu sili pa iwo. 10  Ng’ombe zawo zamphongo zimapereka bere, ndipo siziwononga mphamvu zobereketsa.Ng’ombe zawo zazikazi zimabereka+ ndipo sizibereka ana akufa. 11  Iwo amalola ana awo kutuluka panja ngati nkhosa,Ndipo anawo amakhala akudumphadumpha pabwalo. 12  Iwo amafuula nthawi zonse poimba maseche ndi azeze.+Amakhala akusangalala poimba zitoliro. 13  Masiku awo onse amakhala moyo wabwino,+Ndipo posakhalitsa amatsikira ku Manda. 14  Amauza Mulungu woona kuti, ‘Chokani kwa ife!+Sitikufuna kudziwa njira zanu.+ 15  Kodi Wamphamvuyonse ndani kuti tim’tumikire?Ndipo kulankhula naye kungatipindulitse chiyani?’+ 16  Komatu, ulemerero wawo saupeza chifukwa cha mphamvu zawo.+Malangizo a anthu oipa atalikirana nane.+ 17  Kodi nyale ya oipa imazimitsidwa kangati?+Ndipo tsoka lawo limawagwera kangati? Kodi ndi kangati pamene Mulungu amawakwiyira ndi kuwalanga?+ 18  Kodi iwo amakhala ngati udzu wouluzika ndi mphepo?Kapena ngati mankhusu* ouluka ndi mphepo yamkuntho? 19  Zoipa zimene munthu anachita, Mulungu adzazisungira ana ake omwe,Adzam’patsa mphoto yake, ndipo iye adzaidziwa.+ 20  Maso ake adzaona kuwola kwake,Ndipo iye adzamwa mkwiyo wa Wamphamvuyonse.+ 21  Kodi adzatha kusangalala ndi ana ake iyeyo atapita,Chiwerengero cha miyezi yake chitadulidwa pakati?+ 22  Kodi adzaphunzitsa Mulungu nzeru,+Pamene Mulunguyo azidzaweruza anthu apamwamba?+ 23  Munthu ameneyo adzafa ali wokhutira.+Adzafa ali pa mtendere ndiponso wosatekeseka. 24  Ntchafu zake zitadzaza mafuta,Ndiponso mafuta a m’mafupa mwake akadali ofewa. 25  Winanso adzafa ali wokwiya,Asanadye zinthu zabwino. 26  Iwo adzagona limodzi m’fumbi,+Ndipo mphutsi zidzawakuta.+ 27  Inetu ndikudziwa bwino maganizo anu amuna inu,Ndiponso zachiwawa zimene mungapangane kuti mundichitire.+ 28  Popeza mukuti, ‘Kodi nyumba ya wolemekezeka ili kuti,Ndipo hema wa oipa ali kuti? Kodi malo awo okhala ali kuti?’+ 29  Kodi simunafunse anthu oyenda m’misewu,Ndipo simuonetsetsa zizindikiro zawo, 30  Kuti pa tsiku la tsoka woipa amapulumuka,+Ndipo pa tsiku la mkwiyo amawomboledwa? 31  Ndani angamuuze za njira yake pamasom’pamaso,+Ndipo ndani adzam’patse mphoto ya zimene wachita?+ 32  Iyeyo anthu adzam’tengera kumanda,+Ndipo anthu adzachezera pamanda ake. 33  Kwa iye zibuma za dothi lochokera m’chigwa* zidzakhala zotsekemera.+Pambuyo pake adzakoka anthu onse,+Ndipo amene anapita iye asanapite n’ngosawerengeka. 34  Choncho, amuna inu mukungodzivuta poyesa kunditonthoza,+Ndipo mayankho anu ndi mabodza okhaokha.”

Mawu a M'munsi

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.