Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 2:1-13

2  Pambuyo pa zimenezi, linafika tsiku limene ana a Mulungu woona ankapita kukaonekera pamaso pa Yehova, ndipo nayenso Satana anapita nawo limodzi kukaonekera pamaso pa Yehova.+  Kenako Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi ukuchokera kuti iwe?” Satanayo anamuyankha Yehova kuti: “Ndinali kuzungulirazungulira m’dziko lapansi ndi kuyendayendamo.”+  Ndiyeno Yehova anafunsanso Satana kuti: “Kodi mtima wako uli pa mtumiki wanga Yobu,+ poti palibe wina wokhala ngati iyeyo padziko lapansi? Iyetu ndi munthu wopanda cholakwa ndi wowongoka mtima,+ woopa Mulungu+ ndiponso wopewa zoipa.+ Komabe iye akadali ndi mtima wosagawanika+ ngakhale kuti iweyo ukundiumiriza+ kuti ndimuwononge popanda chifukwa.”+  Koma Satana+ anamuyankha Yehova kuti: “Khungu kusinthanitsa ndi khungu. Munthu angalolere kupereka chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.+  Tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza mnofu wake mpaka fupa lake, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!”+  Choncho Yehova anauza Satana kuti: “Chabwino, ndam’pereka m’manja mwako. Koma samala kuti usakhudze moyo wake.”  Kenako Satana anachoka pamaso pa Yehova+ n’kukagwetsera Yobu zilonda zopweteka,+ kuyambira kuphazi mpaka kumutu.  Ndiyeno Yobu anatenga phale loti azidzikanda nalo ndipo anali kukhala paphulusa.+  Patapita nthawi, mkazi wake anam’funsa kuti: “Kodi mukupitirizabe kukhala ndi mtima wosagawanika?+ Tukwanani Mulungu mufe!” 10  Koma Yobu anamuyankha kuti: “Ukulankhula ngati mmene amalankhulira akazi opusa.+ Kodi tizingolandira zabwino zokha kuchokera kwa Mulungu woona osalandiranso zoipa?”+ M’zonsezi Yobu sanachimwe ndi milomo yake.+ 11  Tsopano anzake atatu a Yobu anamva za tsoka lonse limene linamugwera ndipo aliyense wa iwo anabwera kuchokera kwawo. Mayina awo anali Elifazi wa ku Temani,+ Bilidadi wa ku Shuwa+ ndi Zofari wa ku Naama.+ Iwo anakumana pamodzi atachita kupangana+ kuti apite kukazonda Yobu ndi kukamulimbikitsa.+ 12  Atakweza maso awo ali chapatali, sanamuzindikire poyamba. Kenako anayamba kulira mokweza mawu ndipo aliyense anang’amba+ malaya ake akunja odula manja, n’kuwaza fumbi m’mwamba pamwamba pa mitu yawo.+ 13  Kenako anakhala+ naye limodzi pansi masiku 7 usana ndi usiku, ndipo palibe amene anali kumulankhula chilichonse popeza iwo anaona kuti ululu+ wake unali waukulu kwambiri.

Mawu a M'munsi