Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 18:1-21

18  Tsopano Bilidadi wa ku Shuwa anayankha kuti:   “Kodi zikutengerani nthawi yaitali bwanji anthu inu kuti musiye kulankhula? Muyenera kumvetsa kuti kenako tilankhule.   N’chifukwa chiyani mukutiona ngati zinyama,+ Ndiponso mukutiona ngati odetsedwa m’maso mwanu?   Iwe amene ukukhadzula moyo wako mumkwiyo wako, Kodi dziko lapansi lingasiyidwe chifukwa cha iwe? Kapena mwala ungasunthe pamalo ake chifukwa cha iwe?   Kuwala kwa oipa kudzazimitsidwa,+ Ndipo moto wake sudzawala.   Kuwala kudzazima m’hema wake,+ Nyale yake idzazimitsidwa mmenemo.   Adzasiya kuyenda mwamphamvu n’kuyamba kuyenda mopanikizika. Ngakhale malangizo ake adzam’gwetsa.+   Pakuti adzakodwa mu ukonde ndi mapazi ake, Ndipo adzayenda m’zingwe za ukonde.+   Msampha wam’gwira chidendene.+ Khwekhwe+ lam’kola. 10  Chingwe choti chim’kole chabisidwa pansi, Ndipo msampha woti um’gwire uli panjira yake. 11  Paliponse, zoopsa zadzidzidzi zimamuchititsa mantha,+ Ndipo zimamuthamangitsa zili pafupi naye kwambiri. 12  Mphamvu zake zimachepa, Ndipo tsoka+ limakhala likudikira kuti limuyendetse motsimphina. 13  Mwana woyamba wa imfa azidzanyotsola khungu la munthuyo n’kumadya. Iye adzadya ziwalo zake. 14  Zinthu zimene amazidalira zidzachotsedwa m’hema wake,+ Ndipo zidzapita naye kwa mfumu ya zoopsa. 15  M’hema mwake mudzakhala chinthu chimene si chake. Sulufule+ adzawazidwa pamalo ake okhala. 16  Pansi, mizu yake idzauma.+ Pamwamba, nthambi yake idzafota. 17  Dzina lake silidzatchulidwanso padziko lapansi,+ Ndipo mumsewu simudzakhala dzina lake. 18  Adzamuchotsa powala n’kumukankhira kumdima. Adzamuthamangitsa panthaka ya padziko lapansi. 19  Iye sadzasiya ana kapena mbadwa pakati pa anthu ake,+ Ndipo sipadzakhala wopulumuka pamalo amene iye akukhala monga mlendo. 20  Pa tsiku la tsoka lake anthu a Kumadzulo adzayang’ana modabwa, Ndipo anthu a Kum’mawa adzanjenjemera. 21  Izi n’zimene zimachitikira malo okhala munthu woipa, Ndipo awa ndiwo malo a munthu wosadziwa Mulungu.”

Mawu a M'munsi