Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 17:1-16

17  “Mzimu wanga wasweka,+ masiku anga atha. Kwanga n’kumanda.+   Ndithu, onyoza andizungulira,+ Ndipo diso langa likuyang’anitsitsa khalidwe lawo lopanduka.   Chonde, mundisungire chotsimikizira changa.+ Palinso ndani amene angagwirane nane chanza+ monga chikole?   Pakuti mtima wawo mwauchititsa kuti ukhale wopanda nzeru.+ N’chifukwa chake simukuwakweza.   Munthu angauze anzake kuti atengepo mbali yawo, Koma maso a ana ake adzachita mdima.+   Iye wandisandutsa mwambi+ wa anthu, Mwakuti ndakhala munthu womulavulira kumaso.+   Chifukwa cha kuzunzika, diso langa layamba kuchita mdima.+ Ziwalo zanga zonse zakhala ngati mthunzi.   Anthu owongoka mtima akuyang’ana zimenezi modabwa, Ndipo ngakhale munthu wosalakwa wakwiyira wopanduka.   Wolungama akuyendabe panjira yake,+ Ndipo wa manja oyera+ akungowonjezeka mphamvu.+ 10  Komabe, amuna nonsenu mungathe kuyambiranso kundinena. Chotero pitirizani, Chifukwa sindikuonapo wanzeru pakati panu.+ 11  Masiku anga atha,+ zolinga zanga zasokonezedwa,+ Zofuna za mtima wanga zasokonezedwa. 12  Anzanga akungokhalira kunena zabodza m’malo monena zoona.*+ Iwo akunena kuti: ‘Kuwala kuli pafupi, pamene ine ndikungoona mdima wokhawokha.’ 13  Ndikapitiriza kudikira, ku Manda kukhala kunyumba kwanga.+ Ndidzayala bedi langa mu mdima.+ 14  Ndidzaitana dzenje+ kuti, ‘Ndinu bambo anga!’ Kwa mphutsi+ ndidzati, ‘Mayi anga ndi mlongo wanga!’ 15  Chotero, kodi chiyembekezo changa chili kuti?+ Kodi pali amene akuona kuti ine ndili ndi chiyembekezo? 16  Iwo adzatsikira ku Manda otsekedwa ndi zitsulo, Pa nthawi imene tonsefe tidzatsikira limodzi kufumbi.”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Anzanga akungokhalira kuika usiku m’malo mwa masana.”