Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 16:1-22

16  Tsopano Yobu anayankha kuti:   “Ndamva zinthu zambiri ngati zimenezi. Nonsenu ndinu otonthoza onditopetsa!+   Kodi mawu opanda pakewa saatha?+ Kapena chikukupwetekani n’chiyani kuti muziyankha?   Inenso ndikanatha kulankhula ngati mmene mukuchitiramu, Moyo wanu ukanakhala ngati mmene ulili moyo wanga, Kodi ndikanalankhula mawu ogometsa okunenani?+ Ndipo kodi ndikanakupukusirani mutu?+   Ndikanakulimbikitsani  ndi mawu a m’kamwa mwanga,+ Ndipo chitonthozo cha milomo yanga chikanachepetsa . . .   Ndikalankhula, ululu wanga sukuchepa.+ Ndikasiya kutero, n’chiyani chikundichokera?   Koma tsopano Mulungu wanditopetsa.+ Wawononga onse osonkhana nane.   Komanso inu mwandigwira. Umenewu wakhala umboni,+ Mwakuti kuwonda kwanga kwandiukira ndipo kukuchitira umboni pankhope panga.   Mkwiyo wa Mulungu wandikhadzula. Iye ali nane chidani+ Ndipo akundikukutira mano.+ Mdani wanga akundiyang’ana ndi diso lozonda.+ 10  Iwo ayasamula kukamwa kwawo kuti andimeze.+ Andimenya mbama ndi mnyozo. Asonkhana ambirimbiri kuti alimbane nane.+ 11  Mulungu wandipereka kwa anyamata, Ndipo wandiponya mwamphamvu m’manja mwa oipa.+ 12  Ine ndinali pa mtendere koma iye anandikhutchumula.+ Anandigwira kumbuyo kwa khosi n’kundimenyetsa pansi, Ndipo walunjikitsa mivi yake pa ine. 13  Anthu ake oponya mivi ndi uta+ andizungulira. Iye wandiboola impso+ koma osamva chisoni, Wakhuthulira ndulu yanga pansi. 14  Iye akungokhalira kundiboola ngati mpanda. Akundithamangira ngati mmene amachitira wamphamvu.+ 15  Khungu langa ndalisokera ziguduli*+ zoti livale, Ndipo ndaika nyanga yanga m’fumbi.+ 16  Nkhope yanga yafiira chifukwa cholira,+ Ndipo pazikope zanga pali mdima wandiweyani,+ 17  Chonsecho manja anga sanachite zachiwawa, Ndipo pemphero langa ndi loyera.+ 18  Iwe dziko lapansi, usaphimbe magazi anga.+ Pasapezeke malo osungira kulira kwanga. 19  Komanso, wochitira umboni za ine ali kumwamba, Ndipo mboni yanga ili m’mwamba.+ 20  Anzanga asanduka ondilankhulira otsutsana nane.+ Diso langa lakhala likuyang’ana kwa Mulungu osagona.+ 21  Chiweruzo chiperekedwe pakati pa mwamuna wamphamvu ndi Mulungu, Mofanana ndi pakati pa mwana wa munthu ndi mnzake.+ 22  Chifukwa pangotsala zaka zochepa, Ndipo ndidzapita ndi njira yomwe sindidzabwerera nayonso.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “masaka.”