Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 12:1-25

12  Tsopano Yobu anayankha kuti:   “Zoonadi, amuna inu ndinu anthu, Ndipo nzeru zidzathera limodzi ndi inu.+   Inenso ndili ndi zolinga zabwino+ ngati inuyo. Si ine wonyozeka kwa inu,+ Ndipo ndani amene alibe zinthu ngati zimenezi?   Ine ndakhala chinthu choseketsa kwa anthu anzanga,+ Ndakhala munthu woitana kwa Mulungu kuti amuyankhe.+ Munthu wolungama ndi wosalakwa wakhala choseketsa.   Amene ali pa mtendere amanyoza tsoka n’kumaganiza kuti+ Limagwera okhawo amene mapazi awo amaterereka.+   Mahema a anthu olanda amakhala opanda nkhawa,+ Ndipo anthu okwiyitsa Mulungu amakhala pa mtendere Wofanana ndi wa munthu amene watenga mulungu* m’manja mwake.+   Koma funsa nyama zoweta ndipo zikulangiza.+ Komanso zouluka zam’mlengalenga, ndipo zikuuza.+   Kapena chita chidwi ndi dziko lapansi, ndipo likulangiza.+ Nsomba za m’nyanja+ zikuuza.   Ndani pa zonsezi sadziwa bwino Kuti dzanja la Yehova ndi limene lachita zimenezi?+ 10  Iye amene moyo+ wa aliyense uli m’dzanja lake, Ndiponso mzimu wa anthu onse.+ 11  Kodi khutu si paja limasiyanitsa mawu+ Ngati mmene m’kamwa+ mumasiyanitsira kakomedwe ka chakudya? 12  Kodi okalamba si paja amakhala ndi nzeru,+ Ndipo amene akhala masiku ambiri si paja amamvetsa zinthu? 13  Iye ali ndi nzeru ndi mphamvu.+ Amapereka malangizo ndipo amamvetsa zinthu.+ 14  Iyetu amagwetsa zinthu kuti zisamangidwe,+ Zimene iye watseka, palibe munthu amene angazitsegule.+ 15  Amaletsa madzi ndipo amauma,+ Amawatumiza ndipo madziwo amasintha dziko lapansi.+ 16  Iye ali ndi mphamvu ndi nzeru zopindulitsa.+ Kwa iye kuli wochimwa mosazindikira ndi wochimwitsa ena.+ 17  Amachititsa alangizi kuyenda opanda nsapato,+ Ndipo oweruza amawachititsa misala. 18  Zingwe za mafumu amazimasula,+ Ndipo amawamanga lamba m’chiuno. 19  Amachititsa ansembe kuyenda opanda nsapato,+ Ndipo amene akhazikika amawawononga.+ 20  Okhulupirika, iye amawakhalitsa chete, Ndipo amuna okalamba, iye amawachotsera nzeru. 21  Iye amanyoza anthu olemekezeka,+ Ndipo amakhwepetsa lamba wa anthu amphamvu. 22  Amavundukula zinthu zozama zimene zinali pamdima,+ Ndipo amaunika pamdima wandiweyani. 23  Amapatsa mphamvu mitundu kuti aiwononge.+ Amafutukula mitundu kuti aichotse. 24  Amachotsa nzeru za atsogoleri a anthuwo, Kuti iwo aziyendayenda kumalo kopanda kanthu,+ kumene kulibe njira. 25  Iwo amafufuzafufuza mu mdima+ mopanda kuwala, Kuti awachititse kuyendayenda ngati munthu woledzera.+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza, “fano.”