Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yobu 10:1-22

10  “Ineyo ndikunyansidwa ndi moyo wanga.+ Ndilankhula mwamphamvu za nkhawa zanga. Ndilankhula chifukwa cha kuwawa kwa moyo wanga.   Ndimuuza Mulungu kuti, ‘Musanene kuti ndine woipa. Ndiuzeni chifukwa chimene mukulimbanirana nane.   Kodi ndi bwino kuti inuyo muchite zoipa,+ Kuti mukane chinthu chimene manja anu anagwira ntchito mwamphamvu pochipanga,+ Ndiponso kuti muvomereze malangizo a anthu oipa?   Kodi maso anu+ ali ngati a munthu, Kapena kodi mumaona ngati mmene munthu amaonera?+   Kodi masiku anu ali ngati masiku a munthu,+ Kapena kodi zaka zanu zili ngati masiku a mwamuna wamphamvu,   Kuti muyese kupeza cholakwa changa, Ndi kuti muzifunafuna tchimo langa?+   Chonsecho mukudziwa kuti ndine wosalakwa,+ Ndipo palibe wondipulumutsa m’manja mwanu.+   Manja anu omwe ndi amene anandiumba, ndipo anandipanga+ Kuzungulira thupi langa lonse, koma tsopano mukufuna kundimeza.   Chonde kumbukirani kuti munandiumba ndi dongo,+ Ndipo mudzandibwezera kufumbi.+ 10  Kodi simunandikhuthule ngati mkaka Ndi kundisefa ngati mkaka wosasa?+ 11  Munandiveka khungu ndiponso mnofu, Ndipo munandiluka ndi mafupa ndi mitsempha.+ 12  Mwandipatsa moyo ndi kundisonyeza kukoma mtima kosatha,+ Ndipo mwa kundisamalira+ mumateteza moyo wanga. 13  Zinthu zimenezi mwazibisa mumtima mwanu. Ndikudziwa bwino kuti zinthu zimenezi zili ndi inu. 14  Ngati ndachimwa ndipo inu mwaona zonsezo,+ Ndiponso simunandikhululukire zolakwa zanga,+ 15  Ngati ndine wolakwa, tsoka kwa ine!+ Ngati ndine wosalakwa, ndisadzutse mutu wanga.+ Ndachita manyazi kwambiri ndipo ndadzazidwa ndi mavuto.+ 16  Mutu wanga ukadzikweza,+ mudzandisaka ngati kuti ndinu mkango wamphamvu,+ Ndipo mudzandichitira chinthu chinanso chodabwitsa. 17  Mudzabweretsa mboni zanu zatsopano pamaso panga, Ndipo mudzakulitsa mkwiyo wanu pa ine. Mavuto anga akungotsatizanatsatizana. 18  Kodi munanditulutsiranji m’mimba?+ Zikanakhala bwino ndikanafa kuti diso ndi limodzi lomwe lisandione. 19  Bwenzi nditakhala ngati sindinakhaleko. Ndikanangochokera m’mimba n’kupita kumanda.’ 20  Kodi masiku anga si paja ndi ochepa?+ Iye andisiye, Asiye kundiyang’anitsitsa kuti ndisangalaleko+ pang’ono 21  Ndisanapite. Ndikapita sindibweranso,+ Ndikapita kudziko lamdima wandiweyani,+ 22  Kudziko lopanda kuwala, lamdima wandiweyani Ndi lachisokonezo, losaona kuwala mofanana ndi malo amdima.”

Mawu a M'munsi