Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 66:1-24

66  Yehova wanena kuti: “Kumwamba ndiko mpando wanga wachifumu,+ ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga.+ Kodi anthu inu mungandimangire nyumba yotani? Ndipo malo oti ine ndingapumulirepo, ali kuti?”  “Zinthu zonsezi ndinazipanga ndi dzanja langa, choncho zinakhalapo,”+ akutero Yehova. “Ine ndidzayang’ana munthu amene ali wosautsidwa, wosweka mtima, ndiponso wonjenjemera ndi mawu anga.  “Munthu amene akupha ng’ombe yamphongo ali ngati wopha munthu.+ Amene akupereka nsembe ya nkhosa ali ngati wothyola khosi la galu. Wopereka mphatso ali ngati wopereka magazi a nkhumba. Wopereka lubani wachikumbutso ali ngati wopereka dalitso pogwiritsa ntchito mawu onenerera zamatsenga. Anthuwo asankha njira zawozawo, ndipo amasangalala ndi zinthu zawo zonyansa.  Ineyo ndidzasankha njira zowazunzira.+ Ndidzawabweretsera zinthu zimene amachita nazo mantha+ chifukwa ndinaitana koma palibe amene anayankha. Ndinalankhula koma palibe amene anamvera.+ Iwo anapitiriza kuchita zinthu zoipa pamaso panga ndipo anasankha zinthu zimene sindisangalala nazo.”  Inu amene mukunjenjemera ndi mawu ake, imvani mawu a Yehova: “Abale anu amene akudana nanu,+ amene akukusalani chifukwa cha dzina langa,+ anati, ‘Alemekezeke Yehova!’+ Mulungu adzaonekera ndipo inu mudzasangalala,+ koma iwowo ndi amene adzachite manyazi.”+  Mumzinda mukumveka phokoso lachisokonezo, phokoso lochokera kukachisi.+ Limeneli ndi phokoso losonyeza kuti Yehova akubwezera adani ake chilango chowayenerera.  Mkazi anabereka asanayambe kumva zowawa za pobereka.+ Ululu wa pobereka usanamubwerere, iye anabereka mwana wamwamuna.+  Ndani anamvapo zinthu ngati zimenezi?+ Ndani anaonapo zinthu zoterezi?+ Kodi dziko+ limatulutsidwa ndi zowawa za pobereka tsiku limodzi lokha?+ Kapena kodi mtundu+ umabadwa nthawi imodzi?+ Pakuti Ziyoni wamva zowawa za pobereka ndipo wabereka ana ake aamuna.  “Kodi ine ndingachititse kuti chiberekero chitseguke koma osachititsa kuti mwana abadwe?” akutero Yehova. “Kapena kodi ndingachititse kuti mwana atsale pang’ono kubadwa kenako n’kutseka chiberekero?” watero Mulungu wanu. 10  Sangalalani ndi Yerusalemu ndipo kondwerani naye, inu nonse omukonda.+ Kondwerani naye kwambiri, inu nonse amene mukumulirira,+ 11  chifukwa mudzayamwa bere lake ndipo mudzakhuta kutonthoza kwake. Komanso mudzayamwa mkaka wake ndipo mudzasangalala kwambiri ndi bere lake laulemerero.+ 12  Pakuti Yehova wanena kuti: “Ndidzamupatsa mtendere ngati mtsinje+ ndi ulemerero wa mitundu ya anthu ngati mtsinje wosefukira,+ ndipo inu mudzayamwadi.+ Adzakunyamulani m’manja ndipo adzakusisitani mwachikondi atakuikani pamwendo.+ 13  Mofanana ndi munthu amene mayi ake amamutonthoza, inenso ndidzakutonthozani anthu inu,+ ndipo mudzatonthozedwa chifukwa cha Yerusalemu.+ 14  Mudzaona zimenezi ndipo mtima wanu udzasangalala.+ Mafupa anu+ adzakhala ndi mphamvu ngati udzu wobiriwira.+ Dzanja la Yehova lidzadziwika kwa atumiki ake,+ koma iye adzakwiyira adani ake.”+ 15  “Pakuti Yehova akubwera ngati moto, ndipo magaleta ake ali ngati mphepo yamkuntho+ kuti adzawabwezere mwaukali ndi mokwiya, ndiponso kuti adzawadzudzule ndi malawi a moto. 16  Pakuti ngati moto woyaka, Yehova adzaweruza anthu onse ndi lupanga lake,+ ndipo anthu ophedwa ndi Yehova adzakhala ambiri.+ 17  Anthu amene akudzipatula ndi kudziyeretsa kuti apite kuminda+ n’kukaima kuseri kwa fano limene lili pakati pa mundawo, amene akudya nyama ya nkhumba ndi chinthu chonyansa, amene akudya ngakhale makoswe, onsewo adzathera limodzi,” akutero Yehova. 18  “Popeza ndikudziwa ntchito zawo+ ndi maganizo awo, ine ndikubwera kudzasonkhanitsa pamodzi mitundu yonse ndi zilankhulo zonse za anthu,+ ndipo iwo adzabwera n’kuona ulemerero wanga.”+ 19  “Ndidzachita zinthu zazikulu pakati pawo monga chizindikiro. Opulumuka ena ndidzawatumiza ku mitundu ya anthu,+ ku Tarisi, ku Puli, ndi ku Ludi. Ndidzawatumiza kwa anthu odziwa kukoka uta ku Tubala ndi ku Yavani. Ndidzawatumiza kuzilumba zakutali,+ kwa anthu amene sanamve mbiri yanga kapena kuona ulemerero wanga.+ Iwo adzanenadi za ulemerero wanga pakati pa mitundu ya anthu.+ 20  Adzabweretsa abale anu onse kuchokera ku mitundu yonse monga mphatso kwa Yehova.+ Adzayenda pamahatchi, pangolo, pangolo zotseka pamwamba, panyulu,* ndi pangamila zazikazi zothamanga,+ popita kuphiri langa loyera,+ ku Yerusalemu. Adzachita zimenezi ngati mmene ana a Isiraeli amabweretsera mphatso m’nyumba ya Yehova, ataiika m’chiwiya choyera,” watero Yehova. 21  “Pakati pawo ndidzatengapo anthu ena kuti akhale ansembe ndi Alevi,” watero Yehova. 22  “Pakuti monga momwe kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ndikupanga zidzakhalirebe pamaso panga,+ momwemonso ana anu+ ndi dzina lanu zidzakhalapo mpaka kalekale,”+ akutero Yehova. 23  “Kuyambira mwezi watsopano mpaka mwezi wina watsopano, ndiponso sabata ndi sabata, anthu onse adzabwera kudzagwada pamaso panga,”+ watero Yehova. 24  “Iwo adzapita kukaona mitembo ya anthu amene anali kuphwanya malamulo anga,+ pakuti mphutsi zodya mitemboyo sizidzafa. Moto woinyeketsa sudzazima+ ndipo idzakhala chinthu chonyansa kwa anthu onse.”+

Mawu a M'munsi

Imeneyi ndi nyama yooneka ngati hatchi.