Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 65:1-25

65  “Ine ndalola kuti anthu amene sanafunse za ine+ andifunefune.+ Ndalola kuti anthu amene sanandifunefune andipeze.+ Ndanena kuti, ‘Ndili pano, ndili pano!’+ kwa mtundu umene sunaitane pa dzina langa.+  “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu amakani,*+ amene akuyenda m’njira yoipa+ potsatira maganizo awo,+  anthu amene akundichitira mwano+ nthawi zonse m’maso muli gwa! Amene amapereka nsembe m’minda,+ amene amafukiza nsembe zautsi+ panjerwa,  amene amakhala pansi kumanda,+ amene amakhala usiku wonse m’tinyumba ta alonda, amene amadya nyama ya nkhumba,+ ndipo m’miphika mwawo muli msuzi wa zinthu zodetsedwa.+  Iwo amanena kuti, ‘Khala pawekha. Usandiyandikire, kuti ndingakupatsire chiyero changa.’+ Iwo ali ngati utsi m’mphuno mwanga,+ ngati moto woyaka tsiku lonse.+  “Taonani! Zalembedwa pamaso panga.+ Ine sindidzakhala chete,+ koma ndidzapereka mphoto.+ Mphotoyo ndidzaiika pachifuwa pawo,+  chifukwa cha zolakwa zawo ndi zolakwa za makolo awo pa nthawi imodzi,”+ watero Yehova. “Popeza afukiza nsembe zautsi pamapiri ndipo andinyoza+ pazitunda,+ ine ndidzawayezera mphoto yawo choyamba, n’kuiika pachifuwa pawo.”+  Yehova wanena kuti: “Monga momwe vinyo watsopano+ amapezekera m’tsango la mphesa ndipo wina amanena kuti, ‘Musaliwononge,+ pakuti muli dalitso mmenemu,’+ inenso ndidzachita zomwezo chifukwa cha atumiki anga, kuti ndisawawononge onse.+  Mwa Yakobo ndidzatulutsamo mwana,+ ndipo mwa Yuda ndidzatulutsamo yemwe adzalandire cholowa cha mapiri anga.+ Anthu anga osankhidwa mwapadera adzapatsidwa dziko lamapirilo,+ ndipo atumiki anga adzakhala mmenemo.+ 10  Sharoni+ adzakhala malo odyetserapo nkhosa.+ Chigwa cha Akori+ chidzakhala malo opumulirapo ng’ombe za anthu anga amene andifunafuna.+ 11  “Koma anthu inu mwamusiya Yehova.+ Mwaiwala phiri langa loyera.+ Inu mumayalira tebulo mulungu wa Mwayi.+ Mumadzaza chikho ndi vinyo wosakaniza n’kupereka kwa mulungu wa Zokonzedweratu.+ 12  Choncho ine ndidzakonzeratu zoti anthu inu mudzaphedwe ndi lupanga.+ Nonsenu mudzawerama kuti akupheni,+ popeza ndinakuitanani+ koma simunayankhe. Ndinalankhula koma simunamvere.+ Munapitiriza kuchita zinthu zoipa pamaso panga+ ndipo munasankha zinthu zimene sindisangalala nazo.”+ 13  Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Atumiki anga adzadya,+ koma inuyo mudzakhala ndi njala.+ Atumiki anga adzamwa,+ koma inuyo mudzakhala ndi ludzu.+ Atumiki anga adzasangalala,+ koma inuyo mudzachita manyazi.+ 14  Atumiki anga adzafuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima,+ koma inuyo mudzalira chifukwa chopwetekedwa mtima ndipo mudzafuula chifukwa chosweka mtima.+ 15  Anthu inu mudzasiya dzina lanu kuti anthu anga osankhidwa mwapadera aziligwiritsa ntchito potemberera ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzakuphani mmodzi ndi mmodzi,+ koma atumiki ake adzawapatsa dzina lina.+ 16  Chotero aliyense wofuna kudalitsidwa padziko lapansi adzadalitsidwa ndi Mulungu wokhulupirika.+ Aliyense wolumbira padziko lapansi adzalumbira pa Mulungu wokhulupirika,+ chifukwa masautso akale adzaiwalika ndipo sadzaonedwanso ndi maso anga.+ 17  “Pakuti ndikulenga kumwamba kwatsopano+ ndi dziko lapansi latsopano.+ Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso+ ndipo sizidzabweranso mumtima.+ 18  Koma kondwerani anthu inu,+ ndipo sangalalani kwamuyaya ndi zimene ndikulenga.+ Pakuti ndikulenga Yerusalemu kuti akhale chinthu chosangalatsa ndipo anthu ake akhale chinthu chokondweretsa.+ 19  Ndidzasangalala ndi Yerusalemu ndipo ndidzakondwera ndi anthu anga.+ Mwa iye simudzamvekanso kulira kokweza mawu kapena kulira kwachisoni.”+ 20  “Kumeneko sikudzakhalanso mwana woyamwa wongokhala ndi moyo masiku ochepa okha,+ kapena nkhalamba imene sidzakwanitsa masiku ake.+ Pakuti ngakhale munthu womwalira ali ndi zaka 100 adzaoneka ngati kamnyamata, ndipo wochimwa, ngakhale ali ndi zaka 100, temberero lidzamugwera.+ 21  Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo.+ Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.+ 22  Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya. Pakuti masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo,+ ndipo anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo.+ 23  Sadzagwira ntchito pachabe+ komanso sadzaberekera tsoka,+ chifukwa iwo ndiponso ana awo+ ndi odalitsidwa ndi Yehova.+ 24  Iwo asanandiitane, ine ndidzayankha.+ Asanamalize kulankhula, ine ndidzamva.+ 25  “Mmbulu+ ndi mwana wa nkhosa zidzadyera pamodzi.+ Mkango udzadya udzu ngati ng’ombe yamphongo,+ ndipo njoka izidzadya fumbi.+ Zimenezi sizidzapweteka aliyense+ kapena kuwononga chilichonse m’phiri langa lonse loyera,”+ watero Yehova.

Mawu a M'munsi

Ena amati “anthota.”