Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 64:1-12

64  Zikanakhalatu bwino mukanang’amba kumwamba, mukanatsika pansi pano,+ komanso mapiri akanagwedezeka chifukwa cha inu,+  ngati momwe zimakhalira moto ukayatsa tchire la zitsamba ndiponso ukawiritsa madzi. Zikanakhala bwino mukanachita zimenezi kuti dzina lanu lidziwike kwa adani anu,+ ndiponso kuti mitundu ya anthu igwedezeke chifukwa cha inu.+  Inu munatsikira pansi pano pamene munachita zinthu zochititsa mantha+ zimene sitinali kuyembekezera. Mapiri anagwedezeka chifukwa cha inu.+  Kuyambira kalekale palibe amene anamvapo+ kapena kuganizira za Mulungu wina kupatula inu,+ ndipo palibe amene anamuonapo. Inu mumathandiza munthu amene akukuyembekezerani.+  Mwabwera kudzathandiza anthu amene akukondwera ndiponso amene akuchita zolungama,+ anthu amene amakukumbukirani potsatira njira zanu.+ Koma inuyo munakwiya+ chifukwa chakuti ifeyo tinkangopitirizabe kuchimwa+ kwanthawi yaitali. Choncho kodi ndife oyenera kupulumutsidwa?+  Tonsefe takhala ngati munthu wodetsedwa, ndipo zochita zathu zonse zolungama zili ngati kansalu kamene mkazi amavala pa nthawi yosamba.+ Tonsefe tidzayoyoka ngati masamba+ ndipo zolakwa zathu zidzatiuluzira kutali ngati mphepo.+  Palibe amene akutamanda dzina lanu.+ Palibe amene akutekeseka kuti akufunefuneni ndi kukugwirani mwamphamvu, pakuti mwatibisira nkhope yanu+ ndipo mwatichititsa kuti tisungunuke+ ndi mphamvu ya zolakwa zathu.  Komatu inu Yehova, inu ndinu Atate wathu.+ Ife ndife dongo+ ndipo inu ndinu Wotiumba.+ Tonsefe ndife ntchito ya manja anu.+  Inu Yehova musatikwiyire kwambiri,+ ndipo musakumbukire zolakwa zathu kwamuyaya.+ Chonde, kumbukirani kuti tonsefe ndife anthu anu.+ 10  Mizinda yanu yoyera+ yasanduka chipululu. Ziyoni+ wangosanduka chipululu basi, ndipo Yerusalemu wasanduka bwinja.+ 11  Nyumba yathu yoyera ndiponso yokongola+ imene makolo athu anali kukutamandiranimo,+ yasanduka chinthu chofunika kuchitentha pamoto,+ ndipo zinthu zathu zonse zabwinozabwino+ zasakazidwa. 12  Poona zinthu zonsezi, kodi mupitiriza kumangokhala osachitapo kanthu,+ inu Yehova? Kodi muzingoonerera pamene ife tikusautsidwa koopsa?+

Mawu a M'munsi