Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 63:1-19

63  Kodi amene akuchokera ku Edomuyu+ ndi ndani, amene akuchokera ku Bozira+ atavala zovala zowala zamitundumitundu, amene zovala zake ndi zolemekezeka, ndiponso amene akuyenda mwamphamvu chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake? “Ndi ine, amene ndimalankhula mwachilungamo,+ amene ndili ndi mphamvu zambiri zopulumutsa.”+  N’chifukwa chiyani zovala zanu zili zofiira, ndipo n’chifukwa chiyani zovala zimene mwavala zikuoneka ngati za munthu woponda mphesa m’choponderamo mphesa?+  “Moponderamo mphesa ndapondapondamo ndekha,+ chifukwa palibe munthu amene anali nane wochokera pakati pa mitundu ya anthu. Iwo ndawapondaponda mu mkwiyo wanga,+ ndipo ndawapondereza mu ukali wanga.+ Magazi awo awazikira pazovala zanga,+ ndipo ndaipitsa zovala zanga zonse.  Pakuti tsiku lobwezera lili mumtima mwanga,+ ndipo chaka choti anthu anga awomboledwe chafika.  Ndinayang’anayang’ana, koma panalibe wondithandiza. Ndinayamba kudabwa, koma panalibe woti angandichirikize.+ Choncho ndinabweretsa chipulumutso ndi dzanja langa,+ ndipo ukali wanga+ ndi umene unandichirikiza.  Ndinapondaponda mitundu ya anthu mu mkwiyo wanga, ndipo ndinawaledzeretsa ndi ukali wanga.+ Ndinachititsa kuti magazi awo atuluke mwamphamvu n’kutayikira pansi.”+  Ndidzanena za ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+ Ndidzatamanda Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene Yehova watichitira.+ Ndidzauza nyumba ya Isiraeli zabwino zochuluka+ zimene iye wawachitira chifukwa cha chifundo chake,+ komanso chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha ndiponso kwakukulu.  Iye anati: “Ndithu awa ndi anthu anga,+ ana amene sadzachita zachinyengo.”+ Choncho iye anakhala Mpulumutsi wawo.+  Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.+ Mthenga amene iye anawatumizira, anawapulumutsa.+ Chifukwa cha chikondi chake ndi chisoni chake, iye anawawombola.+ Anawakweza m’mwamba ndi kuwanyamula masiku onse akale.+ 10  Koma iwo anapanduka+ ndi kukhumudwitsa mzimu wake woyera.+ Chotero iye anasintha n’kukhala mdani+ wawo ndipo anachita nawo nkhondo.+ 11  Iwo anayamba kukumbukira masiku akale, masiku a Mose mtumiki wake, ndipo anafunsa kuti: “Kodi amene anawatulutsa m’nyanja+ pamodzi ndi abusa a anthu ake uja, ali kuti?+ Ali kuti amene anaika mzimu wake woyera mwa iye?+ 12  Ali kuti amene anachititsa mkono wake wokongola+ kupita kudzanja lamanja la Mose, amene anagawanitsa madzi pamaso pawo+ kuti adzipangire dzina lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale,+ 13  amene anawawolotsa pamadzi amphamvu moti sanapunthwe, mofanana ndi hatchi m’chipululu?+ 14  Monga momwe chilombo chakutchire chimatsetserekera kuchigwa, mzimu wa Yehova unawapumitsa.”+ Chotero inu munatsogolera anthu anu kuti mudzipangire dzina lokongola.+ 15  Yang’anani muli kumwamba,+ ndipo muone kuchokera pamalo anu okhala apamwamba, oyera ndi okongola.+ Kodi mtima wanu wodzipereka kwambiri+ ndiponso mphamvu zanu zonse zili kuti? Kodi kubwadamuka kwa m’mimba mwanu+ ndi chifundo+ chanu zili kuti? Inuyo mwaleka kundichitira zimenezi.+ 16  Inutu ndinu Atate wathu.+ Ngakhale kuti Abulahamu sanatidziwe ndipo Isiraeli sanatizindikire, inuyo Yehova ndinu Atate wathu. Dzina lanu ndinu Wotiwombola wakalekale.+ 17  N’chifukwa chiyani inu Yehova mukutichititsa kuchoka panjira zanu? N’chifukwa chiyani mukuumitsa mtima wathu kuti tisakuopeni?+ Bwererani chifukwa cha atumiki anu, mafuko a cholowa chanu.+ 18  Kwa kanthawi kochepa, anthu anu oyera+ anali ndi zinthu. Koma adani athu apondaponda malo anu opatulika.+ 19  Kwanthawi yaitali, takhala ngati anthu amene simunawalamulirepo, ngati anthu amene sanatchedwepo ndi dzina lanu.+

Mawu a M'munsi