Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 62:1-12

62  Chifukwa cha Ziyoni sindidzakhala phee,+ ndipo chifukwa cha Yerusalemu+ sindidzakhala chete mpaka kulungama kwake kutakhala ngati kuwala,+ ndiponso mpaka chipulumutso chake chitakhala ngati muuni woyaka moto.+  “Mitundu ya anthu idzaona kulungama kwako+ mkazi iwe,+ ndipo mafumu onse adzaona ulemerero wako.+ Iwe udzatchedwa ndi dzina latsopano+ limene pakamwa pa Yehova padzasankhe.  Udzakhala chisoti chokongola m’dzanja la Yehova,+ ndiponso chisoti chachifumu m’dzanja la Mulungu wako.  Sudzatchedwanso mkazi wosiyidwa mpaka kalekale+ ndipo dziko lako silidzatchedwanso labwinja.+ Koma iweyo dzina lako lidzakhala “Ndimakondwera Naye,”+ ndipo dziko lako lidzatchedwa “Mkazi Wokwatiwa.” Pakuti Yehova adzakondwera nawe ndipo dziko lako lidzakhala ngati mkazi wokwatiwa.+  Pakuti monga momwe mnyamata amatengera namwali kuti akhale mkazi wake, ana ako aamuna adzakutenga kuti ukhale mkazi wawo.+ Monga momwe mkwati amakhalira wachimwemwe chifukwa cha mkwatibwi,+ Mulungu wako adzakhala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe.+  Iwe Yerusalemu, ine ndaika alonda pamakoma a mpanda wako.+ Nthawi zonse, tsiku lonse lathunthu ndi usiku wonse wathunthu, iwo asakhale chete.+ “Inu amene mukutchula dzina la Yehova,+ musakhale chete.+  Musaleke kumukumbutsa mpaka atakhazikitsa Yerusalemu monga chinthu chofunika kutamandidwa padziko lapansi.”+  Yehova walumbira ndi dzanja lake lamanja+ ndiponso ndi mkono wake wamphamvu+ kuti: “Sindidzaperekanso mbewu zanu kwa adani anu ngati chakudya,+ ndipo alendo sadzamwanso vinyo wanu watsopano+ amene munachita kumuvutikira.  Koma anthu amene anakolola mbewuzo ndi amene adzazidye, ndipo adzatamanda Yehova. Amene anasonkhanitsa vinyoyo ndi amene adzamumwe m’mabwalo anga oyera.”+ 10  Tulukani! Tulukani pazipata anthu inu. Lambulani njira yodutsa anthu.+ Konzani msewu. Ukonzeni ndithu. Chotsanimo miyala.+ Akwezereni chizindikiro anthu a mitundu yosiyanasiyana.+ 11  Taonani! Yehova wachititsa kuti mawu awa amveke mpaka kumadera akutali kwambiri a dziko lapansi:+ “Anthu inu, uzani mwana wamkazi wa Ziyoni+ kuti, ‘Taona! Chipulumutso chako chikubwera.+ Taona! Mphoto imene iye akufuna kupereka ili ndi iyeyo,+ ndipo malipiro amene akufuna kupereka ali pamaso pake.’”+ 12  Iwo adzatchedwa anthu oyera,+ owomboledwa ndi Yehova.+ Iweyo udzatchedwa “Mzinda Umene Anaufunafuna,” “Mzinda Umene Sanausiyiretu.”+

Mawu a M'munsi