Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 60:1-22

60  “Imirira+ mkazi iwe! Onetsa kuwala kwako,+ pakuti kuwala kwako kwafika,+ ndipo ulemerero wa Yehova wakuunika.+  Taona! Mdima+ udzaphimba dziko lapansi, ndipo mdima wandiweyani udzaphimba mitundu ya anthu. Koma kuwala kwa Yehova kudzafika pa iwe, ndipo ulemerero wake udzaonekera pa iwe.+  Mitundu ya anthu idzatsata kuwala kwako,+ ndipo mafumu+ adzatsata kunyezimira kwako.+  “Takweza maso ako uone zonse zimene zikuchitika mokuzungulira. Onse asonkhanitsidwa pamodzi.+ Abwera kwa iwe.+ Kuchokera kutali, ana ako aamuna akubwera limodzi ndi ana ako aakazi, amene adzasamalidwe atanyamulidwa m’manja.+  Pa nthawi imeneyo, nkhope yako idzasangalala ukadzaona zimenezi.+ Mtima wako udzanthunthumira ndi kufutukuka, chifukwa chuma cha m’nyanja chidzabwera kwa iwe. Katundu wa mitundu ya anthu adzabwera kwa iwe.+  Chikhamu cha ngamila zamphongo zing’onozing’ono za ku Midiyani ndi ku Efa+ chidzadzaza dziko lako. Anthu onse a ku Sheba+ adzabwera atanyamula golide ndi lubani. Iwo adzatamanda Yehova pamaso pa anthu onse.+  Nkhosa zonse za ku Kedara+ zidzasonkhanitsidwa kwa iwe. Nkhosa zamphongo za ku Nebayoti+ zidzakutumikira.+ Ine ndidzazilandira paguwa langa lansembe,+ ndipo ndidzakongoletsa nyumba yanga yokongola.+  “Kodi amene akubwera chouluka ngati mtambowa ndani?+ Ndani awa akubwera ngati nkhunda zimene zikuulukira kumakomo a makola awo?  Pakuti zilumba zidzayembekezera ine.+ Nazonso zombo za ku Tarisi+ zidzayembekezera ine ngati poyamba paja, kuti zikubweretsere ana ako aamuna kuchokera kutali.+ Iwo adzabwera atanyamula siliva ndi golide wawo,+ kuti alemekeze dzina+ la Yehova Mulungu wako ndi Woyera wa Isiraeli,+ pakuti iye adzakhala atakukongoletsa.+ 10  Alendo adzamanga mipanda yako,+ ndipo mafumu awo adzakutumikira.+ Ine ndinakulanga mu mkwiyo wanga,+ koma chifukwa cha kukoma mtima kwanga ndidzakuchitira chifundo.+ 11  “Zipata zako zidzakhala zotsegula nthawi zonse.+ Sizidzatsekedwa usana ndi usiku kuti chuma cha mitundu ya anthu chibwere kwa iwe,+ ndipo mafumu awo ndiwo adzakhale patsogolo pochita zimenezi.+ 12  Pakuti mtundu uliwonse ndi ufumu uliwonse umene sudzakutumikira udzawonongedwa, ndipo mitundu ya anthu idzasakazidwa ndithu.+ 13  “Ulemerero wa Lebanoni udzabwera kwa iwe. Mtengo wofanana ndi mkungudza, mtengo wa ashi, ndiponso mtengo wa paini zidzabwera pa nthawi imodzi,+ kuti zikongoletse malo anga opatulika,+ ndipo ine ndidzalemekeza malo oikapo mapazi anga.+ 14  “Ana a anthu okusautsa adzabwera kwa iwe atawerama.+ Onse amene anali kukuchitira chipongwe adzagwada pamapazi ako,+ ndipo adzakutcha mzinda wa Yehova, Ziyoni+ wa Woyera wa Isiraeli. 15  “M’malo mokhala wosiyidwa mpaka kalekale ndi wodedwa, popanda aliyense wodutsa mwa iwe,+ ine ndidzakuika monga chinthu chonyaditsa mpaka kalekale, ndiponso chinthu chokondweretsa ku mibadwomibadwo.+ 16  Iwe udzayamwa mkaka wa mitundu ya anthu,+ ndipo udzayamwa bere la mafumu.+ Udzadziwadi kuti ine Yehova+ ndine Mpulumutsi wako,+ ndipo Wamphamvu+ wa Yakobo ndiye Wokuwombola.+ 17  M’malo mwa mkuwa, ndidzabweretsa golide.+ M’malo mwa chitsulo, ndidzabweretsa siliva. M’malo mwa mtengo, ndidzabweretsa mkuwa ndipo m’malo mwa miyala, ndidzabweretsa chitsulo. Ndidzaika mtendere kuti ukhale ngati wokuyang’anira,+ ndi chilungamo kuti chikhale ngati wokupatsa ntchito.+ 18  “M’dziko lako simudzamvekanso zachiwawa. Mkati mwa malire ako simudzakhalanso kusakaza kapena kuwononga.+ Mipanda yako udzaitcha Chipulumutso+ ndipo zipata zako udzazitcha Chitamando. 19  Dzuwa silidzakhalanso lokuunikira masana, ndipo mwezi sudzakuunikiranso. Kwa iwe, Yehova adzakhala kuwala kosatha mpaka kalekale,+ ndipo Mulungu wako adzakhala kukongola kwako.+ 20  Dzuwa lako silidzalowanso, ndipo mwezi wako sudzapitanso kumdima. Pakuti kwa iwe, Yehova adzakhala kuwala kosatha mpaka kalekale,+ ndipo masiku ako olira adzakhala atatha.+ 21  Anthu ako onse adzakhala olungama.+ Iwo adzakhala m’dzikomo mpaka kalekale.+ Anthuwo adzakhala mmera wobzalidwa ndi ine+ ndiponso ntchito ya manja anga,+ kuti ineyo ndikongoletsedwe.+ 22  Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu.+ Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.”+

Mawu a M'munsi