Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 6:1-13

6  M’chaka chimene Mfumu Uziya inamwalira, ine ndinaona Yehova atakhala pampando wachifumu wolemekezeka umene unali pamalo okwezeka, ndipo zovala zake zinadzaza m’kachisi.+  Pamwamba pake panali aserafi.+ Mserafi aliyense anali ndi mapiko 6. Mapiko awiri anaphimbira nkhope yake, awiri anaphimbira mapazi ake ndipo awiri anali kuulukira.  Aliyense anali kuuza mnzake kuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova wa makamu. Zonse zimene zili padziko lapansi zimasonyeza ulemerero wake.”  Chifukwa cha mawuwo, mafelemu a zitseko+ anayamba kunjenjemera ndipo pang’ono ndi pang’ono, m’nyumbamo munadzaza utsi.+  Ine ndinati: “Tsoka kwa ine! Popeza maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu. Nditsikira kuli chete pakuti ndine munthu wa milomo yodetsedwa,+ ndipo ndikukhala pakati pa anthu a milomo yodetsedwa.”+  Pamenepo mserafi mmodzi anaulukira kwa ine. M’manja mwake munali khala lamoto+ limene analitenga paguwa lansembe ndi chopanira.+  Iye anakhudza pakamwa panga+ n’kunena kuti: “Taona! Khalali lakhudza milomo yako, chotero zolakwa zako zachoka ndipo machimo ako aphimbidwa.”+  Kenako ndinayamba kumva mawu a Yehova akufunsa kuti: “Kodi nditumiza ndani, ndipo ndani apite m’malo mwa ife?” Ine ndinayankha kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.”  Iye anapitiriza kunena kuti: “Pita ukauze anthu awa kuti, ‘Imvani mobwerezabwereza anthu inu, koma musamvetsetse. Onani mobwerezabwereza, koma musazindikire chilichonse.’+ 10  Ukachititse anthu awa kuumitsa mtima wawo, ndipo ukachititse makutu awo kuti asamamve.+ Ukamate maso awo kuti asamaone ndi maso awowo, ndiponso kuti asamamve ndi makutu awo, komanso kuti mtima wawo usamvetsetse zinthu, kuti angatembenuke n’kuchira.” 11  Pamenepo ndinafunsa kuti: “Mpaka liti, Yehova?”+ Iye anayankha kuti: “Mpaka mizinda yawo itawonongedwa n’kukhala bwinja, yopanda wokhalamo. Mpaka nyumba zawo zitakhala zopanda anthu okhalamo, ndiponso mpaka nthaka itawonongekeratu. 12  Mpaka Yehova atathamangitsira anthu kutali, ndiponso mpaka mbali yaikulu ya dzikolo itakhala bwinja. 13  M’dzikolo mudzakhalabe chakhumi+ ndipo chidzakhalanso chinthu chofunika kuchitentha ngati mtengo waukulu, ndiponso ngati chimtengo chachikulu, chimene chikadulidwa+ pamatsala chitsa.+ Mbewu yopatulika idzakhala chitsa chake.”

Mawu a M'munsi