Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 59:1-21

59  Dzanja la Yehova silinafupike moti n’kulephera kupulumutsa,+ komanso khutu lake silinagonthe moti n’kulephera kumva.+  Ayi si choncho. Koma zolakwa za anthu inu n’zimene zakulekanitsani ndi Mulungu wanu,+ ndipo machimo anu amuchititsa kuti akubisireni nkhope yake, kuti asamve zimene mukunena.+  Pakuti m’manja mwanu mwaipitsidwa ndi magazi,+ ndipo zala zanu zaipitsidwa ndi zolakwa.+ Milomo yanu yanena zabodza. Lilime lanu limangokhalira kunena zinthu zopanda chilungamo.+  Palibe amene akufuula mwachilungamo,+ ndipo palibe amene amalankhula mokhulupirika akapita kukhoti. Anthu inu mukukhulupirira zinthu zachabechabe+ ndipo mukulankhula zopanda pake.+ Mwatenga pakati pa mavuto ndipo mwabereka zopweteka.+  Iwo aikira mazira a njoka yapoizoni, ndipo ankangokhalira kuluka ukonde wa kangaude.+ Aliyense wodya mazira a njoka yapoizoniyo amafa, ndipo dzira limene laswedwa limaswa mphiri.+  Ukonde wawo wa kangaude sudzakhala chovala chawo, ndipo iwo sadzavala zochita zawo.+ Ntchito zawo n’zopweteka ena, ndipo m’manja mwawo muli ntchito zachiwawa.+  Mapazi awo amangothamangira kukachita zoipa,+ ndipo amafulumira kuti akakhetse magazi osalakwa.+ Maganizo awo ndi opweteka anzawo.+ M’misewu mwawo amangokhalira kusakazana ndi kuwonongana.+  Iwo amangonyalanyaza njira yamtendere,+ ndipo m’njira zawo mulibe chilungamo.+ Misewu yawo aikhotetsakhotetsa.+ Palibe munthu aliyense woyenda mmenemo amene adzadziwe mtendere.+  N’chifukwa chake chilungamo chatitalikira kwambiri, ndipo zolungama sizikutipeza. Tinali kuyembekezera kuunika koma m’malomwake tikungoona mdima. Tinali kuyembekezera kuwala koma tikungoyendabe mu mdima wosatha.+ 10  Tikungoyenda ndi khoma ngati anthu akhungu, ndipo tikungofufuzafufuza ngati anthu opanda maso.+ Tapunthwa masanasana ngati kuti tili mu mdima wamadzulo. Pakati pa anthu ojintcha, tikungokhala ngati anthu akufa.+ 11  Tonsefe tikungolira ngati zimbalangondo ndipo tikungokhalira kubuula momvetsa chisoni ngati njiwa.+ Tinali kuyembekezera chilungamo+ koma sichinabwere. Tinali kuyembekezera chipulumutso koma chakhala nafe kutali.+ 12  Pakuti zolakwa zathu zachuluka pamaso panu,+ ndipo tchimo lathu lililonse likupereka umboni wotsutsana nafe.+ Pakuti zolakwa zathu zili pa ife, ndipo zochimwa zathu tikuzidziwa bwino.+ 13  Ife taphwanya malamulo ndipo tamukana Yehova.+ Tabwerera m’mbuyo n’kumusiya Mulungu wathu. Tanena zinthu zopondereza ena ndi zopanduka.+ Taganiza mawu achinyengo mumtima mwathu n’kumawalankhula chapansipansi.+ 14  Chilungamo tinachikankhira m’mbuyo,+ ndipo chilungamocho chinakangoima patali.+ Pakuti choonadi chapunthwa ngakhale m’bwalo la mumzinda, ndipo zinthu zolungama zikulephera kulowamo.+ 15  Choonadi chikusowa+ ndipo aliyense wokana zoipa akusakazidwa.+ Yehova anaona zimenezi ndipo zinamuipira m’maso mwake poona kuti panalibe chilungamo.+ 16  Iye ataona kuti panalibe munthu aliyense woti n’kuthandizapo, anadabwa kwambiri poona kuti palibe amene akulowererapo.+ Chotero anapulumutsa anthu ndi dzanja lake, ndipo chilungamo chake n’chimene chinamulimbikitsa kuchita zimenezo.+ 17  Choncho iye anavala chilungamo monga chovala chodzitetezera chamamba achitsulo,+ ndiponso anavala chisoti cholimba chachipulumutso kumutu kwake.+ Kuwonjezera apo, anavala chilungamo monga chovala kuti akapereke chilango kwa adani ake+ ndiponso kuchita zinthu modzipereka kwambiri kunali ngati chovala chake chodula manja.+ 18  Iye adzawapatsa mphoto mogwirizana ndi zochita zawo.+ Adani ake adzawapatsa mkwiyo ndipo anthu otsutsana naye adzawapatsa chilango chowayenerera.+ Zilumbanso adzazipatsa chilango choyenerera.+ 19  Amene ali kolowera dzuwa adzayamba kuopa dzina la Yehova,+ ndipo amene ali kotulukira dzuwa adzaopa ulemerero wake.+ Pakuti iye adzabwera ngati mtsinje woyambitsa mavuto woyendetsedwa ndi mzimu wa Yehova.+ 20  “Wowombolayo+ adzabwera ku Ziyoni+ ndiponso kwa mbadwa za Yakobo zimene zasiya zolakwa zawo,”+ akutero Yehova. 21  Yehova wanena kuti: “Koma pangano langa ndi iwowo+ ndi ili: “Mzimu wanga umene uli pa iwe+ ndi mawu anga amene ndaika m’kamwa mwako,+ sizidzachoka m’kamwa mwako ndiponso m’kamwa mwa ana ako kapenanso m’kamwa mwa ana a ana ako, kuyambira panopa mpaka kalekale,” watero Yehova.+

Mawu a M'munsi