Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 54:1-17

54  “Iwe mkazi wosabereka amene sunaberekepo mwana,+ fuula mokondwa!+ Iwe amene sunamvepo zowawa za pobereka,+ kondwera! Fuula mokondwa! Kuwa ndi chisangalalo, pakuti ana a mkazi wosiyidwa ndi ambiri kuposa ana a mkazi yemwe ali ndi mwamuna,”+ watero Yehova.  “Kulitsa hema wako.+ Nsalu za hema wako wamkulu zitambasulidwe. Usaumire pochita zimenezi. Talikitsa zingwe za hema wako ndipo ulimbitse zikhomo zake.+  Pakuti iwe udzafutukukira mbali ya kudzanja lamanja ndi kumanzere, ndipo ana ako+ adzalanda ngakhale mitundu ya anthu.+ Iwo adzakhala m’mizinda imene inasiyidwa yabwinja.+  Usachite mantha,+ pakuti sudzachititsidwa manyazi.+ Usachite manyazi, pakuti sudzakhumudwitsidwa.+ Iwe udzaiwala ngakhale manyazi a paubwana wako,+ ndipo sudzakumbukiranso kunyozeka kwa paumasiye wako wa nthawi yaitali.”  “Pakuti Wokupanga Wamkulu+ ndiye mwamuna wako.+ Dzina lake ndi Yehova wa makamu,+ ndipo Woyera wa Isiraeli ndiye Wokuwombola.+ Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.+  Yehova anakuitana ngati kuti unali mkazi wosiyidwa mpaka kalekale ndi wopwetekedwa mumtima,+ ndiponso ngati mkazi wa paunyamata+ amene kenako anadzasiyidwa,”+ watero Mulungu wako.  “Kwa kanthawi kochepa ndinakusiyiratu,+ koma ndidzakusonkhanitsa pamodzi mwachifundo chachikulu.+  Ndi mkwiyo waukulu ndinakubisira nkhope yanga kwa kanthawi,+ koma ndidzakuchitira chifundo+ ndiponso ndidzakusonyeza kukoma mtima kosatha mpaka kalekale,” watero Yehova, Wokuwombola.+  “Kwa ine, zimenezi zili ngati masiku a Nowa.+ Monga mmene ndinalumbirira kuti madzi a Nowa sadzadutsanso padziko lapansi,+ momwemonso ndalumbira kuti sindidzakukwiyira kapena kukudzudzula.+ 10  Pakuti mapiri akhoza kuchotsedwa, ndipo zitunda zikhoza kugwedezeka,+ koma kukoma mtima kwanga kosatha sikudzachotsedwa kwa iwe,+ ndipo pangano langa la mtendere silidzagwedezeka,”+ watero Yehova, amene akukuchitira chifundo.+ 11  “Iwe mkazi wosautsidwa,+ wokankhidwakankhidwa ndi mphepo yamkuntho,+ ndiponso wosatonthozedwa,+ ine ndikumanga miyala yako ndi simenti yolimba,+ ndipo ndidzayala maziko ako+ ndi miyala ya safiro.+ 12  Nsanja za pamakoma ako ndidzazimanga ndi miyala ya rube, ndipo zipata zako ndidzazimanga ndi miyala yofiira ngati moto.+ Zizindikiro za m’malire ako onse ndidzazimanga ndi miyala yamtengo wapatali. 13  Ana ako onse+ adzakhala anthu ophunzitsidwa ndi Yehova,+ ndipo mtendere wa ana ako udzakhala wochuluka.+ 14  Iwe udzakhazikika m’chilungamo.+ Kuponderezedwa udzatalikirana nako,+ ndipo sudzaopa aliyense. Chilichonse choopsa udzatalikirana nacho, pakuti sichidzakuyandikira.+ 15  Ngati aliyense atakuukira, sadzakhala atatumidwa ndi ine.+ Aliyense wokuukira adzagwa chifukwa cha iwe.”+ 16  “Inetu ndi amene ndinalenga mmisiri, amene amauzira+ moto wamakala+ n’kupanga chida chankhondo ndi luso lake. Inenso ndi amene ndinalenga munthu wowononga,+ amene amagwira ntchito yowononga ena. 17  Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana,+ ndipo lilime lililonse limene lidzalimbane nawe pamlandu udzalitsutsa.+ Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova,+ ndipo chilungamo chawo n’chochokera kwa ine,” akutero Yehova.+

Mawu a M'munsi