Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 53:1-12

53  Kodi ndani wakhulupirira zimene ife tamva?+ Ndipo kodi dzanja la Yehova+ laonetsedwa kwa ndani?+  Iye adzaphuka ngati nthambi+ pamaso pa winawake, ndiponso ngati muzu m’dziko lopanda madzi. Alibe maonekedwe alionse apamwamba kapena okongola,+ ndipo maonekedwe ake si osiririka m’maso mwathu.+  Iye ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa.+ Anali munthu amene anadziwa kupweteka ndiponso amene anadziwa matenda.+ Ife tinali kuyang’ana kumbali kuti tisaone nkhope yake.+ Ananyozedwa ndipo tinamuona ngati wopanda pake.+  Zoonadi, iye anatinyamulira matenda athu+ ndipo anatisenzera zowawa zathu.+ Koma ifeyo tinamuona ngati wosautsidwa,+ wokwapulidwa ndi Mulungu,+ ndiponso wozunzidwa.+  Iye anabayidwa+ chifukwa cha zolakwa zathu.+ Anaphwanyidwa chifukwa cha zochimwa zathu.+ Chilango chotibweretsera mtendere chinam’gwera iyeyo,+ ndipo chifukwa cha zilonda zake+ ifeyo tachiritsidwa.+  Tonsefe tinkangoyendayenda uku ndi uku ngati nkhosa.+ Aliyense analowera njira yake ndipo Yehova wachititsa cholakwa cha aliyense wa ife kugwera pa ameneyo.+  Iye anapanikizidwa+ ndipo analola kuti asautsidwe,+ koma sanatsegule pakamwa pake. Anatengedwa ngati nkhosa yopita kokaphedwa,+ ndipo mofanana ndi nkhosa yaikazi imene imakhala chete akamaimeta ubweya, nayenso sanatsegule pakamwa pake.+  Iye anaponderezedwa ndipo anatengedwa popanda kuweruzidwa mwachilungamo.+ Ndani amene anaganizira tsatanetsatane wa mibadwo ya makolo ake?+ Pakuti iye anadulidwa+ m’dziko la amoyo.+ Chifukwa cha zolakwa+ za anthu anga, iye anakwapulidwa.+  Manda ake adzakhala limodzi ndi a anthu oipa,+ ndipo adzakhala limodzi ndi anthu olemera pa imfa yake,+ ngakhale kuti iye sanachite zachiwawa zilizonse+ ndipo m’kamwa mwake munalibe chinyengo.+ 10  Koma zinamukomera Yehova kuti mtumiki wake aphwanyidwe.+ Iye anamulola kuti adwale.+ Mukapereka moyo wake monga nsembe ya kupalamula,+ iye adzaona ana ake.+ Adzatalikitsa masiku ake+ ndipo ndi dzanja lake, adzakwaniritsa zokonda+ Yehova.+ 11  Chifukwa cha kuvutika kwake, iye adzaona zabwino+ ndipo adzakhutira.+ Chifukwa cha zimene akudziwa, mtumiki wanga wolungamayo+ adzachititsa kuti anthu ambiri azionedwa olungama,+ ndipo adzasenza zolakwa zawo.+ 12  Pa chifukwa chimenechi, ndidzamupatsa gawo pamodzi ndi ambiri+ ndipo iye adzagawana zolanda ndi amphamvu,+ chifukwa anakhuthula moyo wake mu imfa+ ndipo anaonedwa monga mmodzi wa ochimwa.+ Iye ananyamula tchimo la anthu ambiri+ ndipo analowererapo kuti athandize olakwa.+

Mawu a M'munsi