Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 51:1-23

51  “Ndimvereni, inu anthu amene mukufunafuna chilungamo,+ inu amene mukufuna kupeza Yehova.+ Yang’anani kuthanthwe+ limene munasemedwako, ndi kuphanga la dzenje limene munakumbidwako.  Yang’anani kwa tate+ wanu Abulahamu,+ ndi kwa Sara+ amene anakuberekani ndi zowawa za pobereka. Abulahamuyo anali munthu mmodzi pamene ndinamuitana,+ koma ndinamudalitsa ndi kumusandutsa anthu ambiri.+  Pakuti Yehova adzatonthoza Ziyoni.+ Iye adzatonthozadi malo ake onse owonongedwa.+ Adzachititsa chipululu chake kukhala ngati Edeni+ ndi dera lake lachipululu kukhala ngati munda wa Yehova.+ Mwa iye mudzakhala kusangalala ndi kukondwera, kuyamikira ndi kuimba nyimbo.+  “Inu anthu anga, tandimverani. Iwe mtundu wanga,+ tatchera khutu kwa ine. Pakuti kwa ine kudzachokera lamulo+ ndipo ndidzachititsa chigamulo changa kukhazikika monga kuwala kwa mitundu ya anthu.+  Chilungamo changa chili pafupi.+ Chipulumutso+ chochokera kwa ine chili m’njira ndipo manja anga adzaweruza mitundu ya anthu.+ Zilumba zidzayembekezera ine+ ndipo zidzadikira dzanja langa.+  “Kwezani maso anu kumwamba,+ ndipo yang’anani padziko lapansi. Pakuti kumwamba kudzabenthukabenthuka n’kumwazidwa ngati utsi,+ ndipo dziko lapansi lidzatha ngati chovala.+ Anthu okhalamo adzafa ngati ntchentche. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka kalekale+ ndipo chilungamo changa sichidzaphwanyika.+  “Ndimvereni, inu odziwa chilungamo, inu amene muli ndi lamulo langa mumtima mwanu.+ Musaope chitonzo cha anthu ndipo musachite mantha chifukwa cha mawu awo onyoza.+  Pakuti njenjete idzawadya ngati chovala ndipo kachilombo kodya zovala kadzawadya ngati thonje.+ Koma chilungamo changa chidzakhala mpaka kalekale ndipo chipulumutso changa chidzafikira mibadwo yosawerengeka.”+  Dzuka! Dzuka! Vala mphamvu,+ iwe dzanja la Yehova!+ Dzuka ngati masiku akale, ngati m’mibadwo yakalekale.+ Kodi si iwe amene unaphwanyaphwanya Rahabi,+ amene unabaya* chilombo cha m’nyanja?+ 10  Kodi si iwe amene unaumitsa nyanja, amene unaumitsa madzi akuya kwambiri?+ Si iwe kodi amene unasandutsa pansi pa nyanja kukhala njira yoti anthu owomboledwa awolokerepo?+ 11  Chotero, owomboledwa a Yehova adzabwerera ku Ziyoni ndi mfuu yachisangalalo,+ ndipo pamutu pawo padzakhala chisangalalo mpaka kalekale.+ Iwo adzapeza chisangalalo ndi chimwemwe.+ Chisoni ndi kuusa moyo zidzachoka.+ 12  “Ineyo ndi amene ndikukutonthozani anthu inu.+ “Kodi n’chifukwa chiyani iwe ukuopa munthu woti adzafa,+ ndi mwana wa munthu yemwe adzakhale ngati udzu wobiriwira?+ 13  Kodi n’chifukwa chiyani ukuiwala Yehova amene anakupanga,+ amene anatambasula kumwamba+ ndi kuyala maziko a dziko lapansi?+ N’chifukwa chiyani ukuchita mantha nthawi zonse, tsiku lonse lathunthu, poopa mkwiyo wa yemwe akukupanikizira mkati,+ ngati kuti iye wakonzeka kuti akuwononge?+ Kodi mkwiyo wa amene akukupanikizira mkati uli kuti?+ 14  “Yemwe wawerama atamangidwa maunyolo adzamasulidwa msangamsanga.+ Iye sadzafa, sadzatsikira kudzenje,+ komanso sadzasowa chakudya.+ 15  “Koma ine Yehova ndine Mulungu wako, amene ndimavundula nyanja kuti mafunde ake achite phokoso.+ Yehova wa makamu ndiye dzina langa.+ 16  Ndidzaika mawu anga m’kamwa mwako+ ndipo ndidzakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa.+ Ndidzachita zimenezi n’cholinga choti ndikhazikitse kumwamba+ ndi kuyala maziko a dziko lapansi,+ ndiponso kuti ndiuze Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’+ 17  “Dzuka! Dzuka! Imirira iwe Yerusalemu,+ iwe amene wamwa chikho cha mkwiyo wa Yehova kuchokera m’dzanja lake.+ Iweyo wamwa ndipo wagugudiza chipanda, chikho chochititsa munthu kuyenda dzandidzandi.+ 18  Pa ana onse amene iye anabereka, palibe ndi mmodzi yemwe+ amene anali kutsogolera mayiyo poyenda. Pa ana onse amene iye analera, palibe ndi mmodzi yemwe amene anagwira dzanja lake.+ 19  Zinthu ziwiri zidzakugwera.+ Kodi adzakumvera chisoni ndani?+ Udzalandidwa katundu ndi kuphwanyidwa, ndiponso udzakumana ndi njala ndi lupanga.+ Kodi adzakutonthoza ndani?+ 20  Ana ako akomoka.+ Agona m’misewu yonse ngati nkhosa zakutchire zokodwa mu ukonde,+ ngati anthu okhuta mkwiyo wa Yehova,+ okhuta kudzudzula kwa Mulungu wako.”+ 21  Chotero mvetsera izi, iwe mkazi+ wosautsidwa ndi woledzera, koma osati ndi vinyo.+ 22  Ambuye wako, Yehova, Mulungu wako, amene amateteza+ anthu ake, wanena kuti: “Taona! Ine ndidzachotsa m’manja mwako chikho chochititsa munthu kudzandira.+ Sudzamwanso chipanda, chikho cha mkwiyo wanga.+ 23  Ndidzachiika m’manja mwa amene akukuvutitsa,+ amene akukuuza kuti, ‘Werama kuti tiwolokere pamsana pako,’ amene akuona msana wako ngati pansi popondapo, ndiponso ngati njira yowolokerapo.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “kulasa.”