Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 49:1-26

49  Ndimvereni zilumba inu,+ ndipo mvetserani, inu mitundu ya anthu akutali.+ Yehova anandiitana+ ndili m’mimba.+ Ndili mkati mwa mayi anga, anatchula dzina langa.+  Iye anachititsa m’kamwa mwanga kukhala ngati lupanga lakuthwa.+ Anandibisa mumthunzi+ wa dzanja lake.+ Anandisandutsa muvi wonola bwino. Anandibisa m’kachikwama kake koikamo mivi.  Kenako anandiuza kuti: “Iwe Isiraeli ndiwe mtumiki wanga.+ Ine ndidzaonetsera kukongola kwanga pa iwe.”+  Koma ine ndinati: “Ndangovutika pachabe.+ Mphamvu zanga ndangoziwonongera zinthu zopanda pake ndi zachabechabe.+ Ndithu, Yehova ndiye amene adzandiweruze+ ndipo Mulungu wanga ndiye amene adzandipatse mphoto yanga.”+  Tsopano Yehova, amene anandipanga ndili m’mimba kuti ndikhale mtumiki wake,+ wanena kuti ndimubwezere Yakobo,+ n’cholinga choti Isiraeli asonkhanitsidwe kwa iye.+ Ine ndidzakhala wolemekezeka pamaso pa Yehova ndipo Mulungu wanga adzakhala mphamvu yanga.  Ndiyeno iye anati: “Si nkhani yochepa kuti iweyo wakhala mtumiki wanga, n’cholinga choti ubwezeretse mafuko a Yakobo ndi kubweza Aisiraeli amene ali otetezeka.+ Ndakupereka kuti ukhale kuwala kwa mitundu ya anthu,+ kuti chipulumutso changa chifike mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”+  Yehova, Wowombola Isiraeli,+ Woyera wake, wauza yemwe ananyozedwa kwambiri,+ yemwe amadedwa ndi mtundu wa anthu,+ mtumiki wa atsogoleri,+ kuti: “Mafumu adzaimirira chifukwa cha zimene adzaone,+ ndipo akalonga adzagwada chifukwa cha Yehova. Iye ndi wokhulupirika,+ Woyera wa Isiraeli, amene anakusankha.”+  Yehova wanena kuti: “Pa nthawi yapadera yosonyeza kukoma mtima kwanga, ndinakuyankha.+ M’tsiku la chipulumutso, ndinakuthandiza.+ Ndinakuteteza kuti ndikupereke ngati pangano kwa anthu,+ kuti ndikonzenso dzikolo,+ kuti anthu ayambirenso kukhala m’cholowa chawo chimene chinali bwinja,+  kuti ndiuze akaidi+ kuti, ‘Tulukani!’+ ndi amene ali mu mdima+ kuti, ‘Dziululeni!’+ Iwo adzadya msipu m’mphepete mwa msewu, ndipo m’mphepete mwa njira zonse zodutsidwadutsidwa mudzakhala malo awo odyeramo msipu.+ 10  Iwo sadzakhala ndi njala+ ndipo sadzamva ludzu.+ Sadzamva kutentha kapena kupsa ndi dzuwa.+ Pakuti yemwe amawamvera chisoni adzawatsogolera+ ndipo adzapita nawo ku akasupe amadzi.+ 11  Ndidzachititsa kuti mapiri anga onse akhale njira, ndipo misewu yanga yonse idzakhala pamalo okwera.+ 12  Taonani! Awa adzachokera kutali,+ ndipo awa adzachokera kumpoto+ ndi kumadzulo.+ Awanso adzachokera kudziko la Sinimu.” 13  Fuulani mokondwa kumwamba inu,+ ndipo sangalala iwe dziko lapansi.+ Mapiri asangalale ndipo afuule ndi chisangalalo.+ Pakuti Yehova watonthoza anthu ake+ ndipo amamvera chisoni anthu ake osautsidwa.+ 14  Koma Ziyoni ankangonena kuti: “Yehova wandisiya+ ndipo Yehova wandiiwala.”+ 15  Kodi mayi angaiwale mwana wake woyamwa, osamvera chisoni mwana wochokera m’mimba mwake?+ Ngakhale amayi amenewa akhoza kuiwala,+ koma ine sindidzakuiwala.+ 16  Taona! Ndakudinda m’manja mwanga.+ Makoma ako ali pamaso panga nthawi zonse.+ 17  Ana ako abwera mofulumira. Anthu amene anali kukukhadzula ndi kukuwononga adzakuchokera. 18  Takweza maso ako uone zonse zimene zikuchitika mokuzungulira. Onse asonkhanitsidwa pamodzi.+ Abwera kwa iwe. Yehova wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo,+ onsewo udzadzikongoletsa nawo ngati zokongoletsera, ndipo udzawavala ngati ndiwe mkwatibwi.+ 19  Ngakhale kuti panopa malo ako ndi owonongeka, osakazidwa ndiponso abwinja,+ ngakhale kuti panopa malo ako ndi osatakasuka mokwanira kuti n’kukhalamo bwinobwino, ndipo okumeza akhala kutali,+ 20  koma ana ako amene unabereka ana ena onse atamwalira,+ adzakuuza kuti, ‘Malowa atichepera.+ Tipezereni malo oti tikhalemo.’+ 21  Iweyo udzanenadi mumtima mwako kuti, ‘Kodi bambo wa ana amene ndaberekawa ndani, popeza ine ndine mayi woferedwa ana ndiponso wosabereka, mayi yemwe anatengedwa kupita kudziko lina ku ukaidi?+ Nanga ana awa, anawalera ndani?+ Inetu ndinasiyidwa m’mbuyo ndekhandekha.+ Ndiyeno ana awa anali kuti?’”+ 22  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Taona! Ineyo ndidzakwezera dzanja langa mitundu ya anthu,+ ndipo anthu a mitundu yosiyanasiyana ndidzawakwezera chizindikiro.+ Iwo adzakubweretsera ana ako aamuna atawanyamulira pachifuwa, ndipo ana ako aakazi adzawanyamulira paphewa.+ 23  Mafumu adzakhala okusamalira,+ ndipo ana awo aakazi adzakhala okuyamwitsira ana ako. Iwo adzakugwadira mpaka nkhope zawo pansi+ ndipo adzanyambita fumbi la kumapazi ako.+ Pamenepo, ndithu iweyo udzadziwa kuti ine ndine Yehova, ndiponso kuti anthu okhulupirira mwa ine sadzachita nane manyazi.”+ 24  Kodi anthu amene atengedwa kale angalandidwe m’manja mwa munthu wamphamvu,+ kapena kodi gulu la anthu amene agwidwa ndi wolamulira wankhanza lingathawe?+ 25  Koma Yehova wanena kuti: “Ngakhale gulu la anthu ogwidwa ndi munthu wamphamvu lidzatengedwa,+ ndipo amene anatengedwa kale ndi wolamulira wankhanza adzathawa.+ Aliyense wolimbana nawe, ineyo ndidzalimbana naye,+ ndipo ana ako ndidzawapulumutsa.+ 26  Amene akukuzunza ndidzawachititsa kuti adye mnofu wawo womwe, ndipo adzaledzera ndi magazi awo omwe ngati kuti amwa vinyo wotsekemera. Anthu onse ndithu adzadziwa kuti ine, Yehova,+ ndine Mpulumutsi wako+ ndiponso Wokuwombola,+ Wamphamvu wa Yakobo.”+

Mawu a M'munsi