Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 48:1-22

48  Mverani izi inu a m’nyumba ya Yakobo, inu amene mumadzitcha ndi dzina la Isiraeli,+ amene munatuluka kuchokera m’madzi a Yuda,+ amene mumalumbira pa dzina la Yehova,+ ndiponso inu amene mumaitana Mulungu wa Isiraeli,+ koma osati m’choonadi kapena m’chilungamo.+  Pakuti iwo amadzitcha kuti amakhala mumzinda woyera,+ ndipo amadalira Mulungu wa Isiraeli+ amene dzina lake ndi Yehova wa makamu.+  “Ndanena zinthu zoyambirira kuchokera pa nthawi imeneyo. Zinatuluka pakamwa panga, ndipo ndinazichititsa kumveka.+ Mwadzidzidzi, ndinazichita ndipo zinachitikadi.+  Podziwa kuti ndinu olimba,+ ndi kuti mtsempha wa khosi lanu uli ngati chitsulo,+ ndiponso kuti mphumi yanu ili ngati mkuwa,+  ine ndinakuuzani zonse kuyambira nthawi imeneyo. Ndinakuuzani zisanachitike,+ kuti musadzanene kuti, ‘Fano langa ndi limene lachita zimenezi, ndipo chifaniziro changa chosema komanso chifaniziro changa chopangidwa ndi chitsulo chosungunula, n’zimene zalamula zimenezi.’+  Inuyo mwazimva.+ Onani zonsezo.+ Kodi simudzazifotokozera ena?+ Kuyambira panopa ine ndikukuuzani zinthu zatsopano. Ndakuuzani zinthu zobisika zimene simunali kuzidziwa.+  Zinthu zimene ndikulengazi n’zatsopano, si zinthu zakale ayi. Ndi zinthu zimene simunazimvepo m’mbuyomu. Ndikuchita izi chifukwa munganene kuti, ‘Ifetu tinali kuzidziwa kale zimenezi.’+  “Komanso, inu simunafune kumva+ kapena kumvetsa zimenezi. Kuyambira pa nthawi imeneyo kupita m’tsogolo, simunatsegule khutu lanu. Pakuti ine ndinkadziwa ndithu kuti inu munali kuchita zachinyengo,+ ndipo mwatchedwa ‘wochimwa chibadwire.’+  Ndidzabweza mkwiyo wanga chifukwa cha dzina langa,+ ndipo chifukwa cha ulemerero wanga, ine ndidzadziletsa kuti ndisakuwonongeni.+ 10  Taonani! Ndinakuyengani koma osati ngati mmene amayengera siliva.+ Ndinakusankhani pamene munali m’ng’anjo ya masautso.+ 11  Ndithu, ndidzachitapo kanthu chifukwa cha dzina langa.+ Pakuti munthu angalekerere bwanji dzina lake likuipitsidwa?+ Ulemerero wanga sindidzaupereka kwa wina aliyense.+ 12  “Ndimvere iwe Yakobo, iwe Isiraeli amene ndinakuitana. Ine sindinasinthe.+ Ine ndine woyamba.+ Ndinenso womaliza.+ 13  Komanso dzanja langa linayala maziko a dziko lapansi,+ ndipo dzanja langa lamanja linatambasula kumwamba.+ Ndimafuulira maziko a dziko lapansi ndi kumwamba, kuti ziimirire.+ 14  “Sonkhanani pamodzi anthu nonsenu kuti mumve.+ Ndani pakati pawo ananenapo zinthu zimenezi? Iye amene Yehova wamukonda+ adzachitira Babulo zimene akufuna.+ Dzanja lake lidzakhala pa Akasidi.+ 15  Ineyo ndalankhula, komanso ndamuitana.+ Ndamubweretsa, ndipo ndidzachititsa kuti zochita zake zimuyendere bwino.+ 16  “Bwerani pafupi ndi ine anthu inu. Mvetserani izi. Kuyambira pa chiyambi, ine sindinalankhulirepo m’malo obisika.+ Pamene zinthu zonenedwazo zinayamba kuchitika, ine ndinalipo.” Tsopano Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, watumiza ine ndiponso watumiza mzimu wake.+ 17  Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino,+ amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.+ 18  Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga!+ Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje,+ ndipo chilungamo chanu chidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.+ 19  Mbadwa zanu zochokera mkati mwa matupi anu zidzakhala ngati mchenga.+ Dzina lawo silidzatha kapena kuwonongedwa pamaso panga.”+ 20  Tulukani m’Babulo anthu inu!+ Thawani m’manja mwa Akasidi.+ Nenani zimenezi ndi mfuu yachisangalalo kuti zimveke.+ Zineneni mokuwa mpaka zimveke kumalekezero a dziko lapansi.+ Munene kuti: “Yehova wawombola mtumiki wake Yakobo.+ 21  Iwo sanamve ludzu+ ngakhale pamene iye anawayendetsa m’chipululu.+ Iye anawatulutsira madzi pathanthwe. Anang’amba thanthwe kuti madzi atulukepo.”+ 22  Yehova wanena kuti, “Oipa alibe mtendere.”+

Mawu a M'munsi