Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 45:1-25

45  Ine Yehova ndalankhula kwa wodzozedwa wanga.+ Ndalankhula kwa Koresi amene ndamugwira dzanja lake lamanja+ kuti ndigonjetse mitundu ya anthu pamaso pake,+ kuti ndimasule m’chiuno mwa mafumu, kuti ndimutsegulire zitseko zokhala ziwiriziwiri, moti ngakhale zipata sizidzatsekedwa. Ndalankhula kuti:  “Ine ndidzakhala kutsogolo kwako+ ndipo ndidzasalaza zitunda za m’dzikolo.+ Ndidzaphwanyaphwanya zitseko zamkuwa ndipo ndidzadula mipiringidzo yachitsulo.+  Ndidzakupatsa chuma+ chimene chili mu mdima ndi chuma chobisika chimene chili m’malo achinsinsi, kuti udziwe kuti ine ndine Yehova, Mulungu wa Isiraeli, amene ndikukuitana ndi dzina lako.+  Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo ndi Isiraeli wosankhidwa wanga,+ ine ndinakuitana ndi dzina lako. Ndinakupatsa dzina laulemu, ngakhale kuti sunali kundidziwa.+  Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.+ Palibenso Mulungu kupatulapo ine.+ Ndidzakumanga mwamphamvu m’chiuno mwako, ngakhale kuti sukundidziwa,  kuti anthu adziwe kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kolowera dzuwa kuti palibenso wina kupatulapo ine.+ Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.+  Ndimapanga kuwala+ ndiponso ndimabweretsa mdima.+ Ndimabweretsa mtendere+ ndiponso tsoka.+ Ine Yehova ndimapanga zonsezi.+  “Inu kumwamba, chititsani chilungamo kuvumba ngati mvula.+ Kumwamba kwa mitambo kuchuche chilungamo.+ Dziko lapansi litseguke ndipo libale chipulumutso. Lichititse chilungamo kuphuka+ pa nthawi imodzimodziyo. Ine Yehova ndachititsa zimenezi.”+  Tsoka kwa amene walimbana ndi amene anamuumba,+ ngati phale limene likulimbana ndi mapale ena amene ali pansi. Kodi dongo+ lingafunse amene akuliumba kuti: “Kodi ukupanga chiyani?” Ndipo kodi chimene unapanga chinganene kuti: “Amene uja alibe manja”? 10  Tsoka kwa wofunsa bambo kuti: “Kodi n’chiyani mwaberekachi?” Ndiponso wofunsa mkazi kuti: “Kodi zowawa za pobereka zimene mukumvazi mukufuna mubereke chiyani?”+ 11  Yehova, Woyera wa Isiraeli+ ndiponso amene anamuumba,+ wanena kuti: “Ndifunseni za zinthu zimene zikubwera+ zokhudza ana anga.+ Ndipo pa zinthu zokhudza ntchito+ ya manja anga mundifunse kuti ndikuyankheni. 12  Ineyo ndinapanga dziko lapansi+ ndipo ndinalenga munthu n’kumuikapo.+ Manja anga anatambasula kumwamba,+ ndipo nyenyezi ndi zonse zimene zili kumwambako ndimazilamulira.”+ 13  “Ine ndautsa winawake m’chilungamo+ ndipo njira zake zonse ndidzaziwongola.+ Iye ndi amene adzamange mzinda wanga+ ndipo anthu anga amene ali ku ukapolo adzawamasula,+ koma osati ndi malipiro+ kapena ndi chiphuphu,” watero Yehova wa makamu. 14  Yehova wanena kuti: “Antchito osalipidwa a ku Iguputo,+ amalonda a ku Itiyopiya, ndi Asabeya,+ amuna ataliatali,+ adzabwera kwa iwe ndipo adzakhala ako.+ Iwo adzayenda pambuyo pako. Adzabwera kwa iwe atamangidwa m’matangadza+ ndipo adzakugwadira.+ Adzapemphera kwa iwe kuti, ‘Zoonadi Mulungu ali ndi iwe+ ndipo palibenso wina. Palibenso Mulungu wina.’”+ 15  Ndithu, inu ndinu Mulungu yemwe amadzibisa,+ Mulungu wa Isiraeli, Mpulumutsi.+ 16  Anthu adzachita manyazi ndipo onsewo adzanyozeka. Anthu opanga mafano adzayenda monyozeka onse pamodzi.+ 17  Koma Isiraeli adzapulumutsidwa chifukwa chokhala pa mgwirizano ndi Yehova+ ndipo adzakhala wopulumutsidwa mpaka kalekale.+ Anthu inu simudzachita manyazi+ ndipo simudzanyozeka+ mpaka kalekale, ngakhale kwamuyaya. 18  Pakuti Yehova, Mlengi wa kumwamba,+ Mulungu woona,+ amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga,+ amene analikhazikitsa mwamphamvu,+ amene sanalilenge popanda cholinga, amene analiumba kuti anthu akhalemo,+ wanena kuti: “Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.+ 19  Ine sindinalankhule m’malo obisika,+ m’malo amdima a padziko lapansi. Sindinauze mbewu ya Yakobo kuti, ‘Anthu inu muzindifunafuna pachabe.’+ Ine ndine Yehova, wolankhula zolungama, wonena zowongoka.+ 20  “Sonkhanani pamodzi n’kubwera kwa ine.+ Unjikanani pamodzi, inu anthu opulumuka ku mitundu ya anthu.+ Amene amanyamula chifaniziro chawo chosema chamtengo sadziwa kanthu, mofanana ndi amene amapemphera kwa mulungu woti sangawapulumutse.+ 21  Lankhulani ndipo mufotokoze mlandu wanu.+ Inde, iwo afunsanefunsane mogwirizana. Kodi ndani wachititsa zimenezi kuti zimveke kuyambira kalekale?+ Ndani wazinena kuyambira nthawi imene ija?+ Kodi si ine Yehova, amene palibenso Mulungu wina kupatulapo ine?+ Ine ndine Mulungu wolungama ndi Mpulumutsi+ ndipo palibenso wina kupatulapo ine.+ 22  “Tembenukirani kwa ine kuti mupulumuke,+ inu nonse amene muli kumapeto kwa dziko lapansi, pakuti ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.+ 23  Ndalumbira pa ine mwini.+ Mawuwo atuluka m’kamwa mwanga m’chilungamo,+ moti sadzabwerera.+ Ndalumbira kuti bondo lililonse lidzagwadira ine+ ndipo lilime lililonse lidzalumbira kwa ine,+ 24  kuti, ‘Zoonadi, kwa Yehova kuli chilungamo chonse ndi mphamvu.+ Onse omukwiyira adzabwereranso kwa iyeyo n’kuchita manyazi.+ 25  Mbewu+ yonse ya Isiraeli idzaona kuti inalondola+ potumikira Yehova ndipo idzadzitama.’”+

Mawu a M'munsi