Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 43:1-28

43  Tsopano iwe Yakobo, mvera zimene wanena Yehova Mlengi wako,+ yemwe anakupanga+ iwe Isiraeli. Iye wanena kuti: “Usachite mantha, pakuti ine ndakuwombola.+ Ndakuitana pokutchula dzina.+ Iwe ndiwe wanga.+  Ukamadzadutsa pamadzi,+ ine ndidzakhala nawe.+ Ukamadzawoloka mitsinje, madzi sadzakumiza.+ Ukamadzayenda pamoto sudzapsa ndipo ngakhale lawi la moto silidzakuwaula.+  Pakuti ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Isiraeli ndiponso Mpulumutsi wako.+ Ndapereka Iguputo monga dipo* lokuwombolera.+ Ndaperekanso Itiyopiya+ ndi Seba m’malo mwako.  Chifukwa chakuti ndiwe wamtengo wapatali kwa ine,+ ndimakulemekeza ndipo ndimakukonda.+ Ndidzapereka anthu m’malo mwa iwe, ndipo ndidzapereka mitundu ya anthu m’malo mwa moyo wako.+  “Usachite mantha chifukwa ine ndili nawe.+ Ndidzabweretsa mbewu yako kuchokera kotulukira dzuwa, ndipo ndidzakusonkhanitsani pamodzi kuchokera kolowera dzuwa.+  Ndidzauza kumpoto kuti,+ ‘Abwezere kwawo!’ ndipo ndidzauza kum’mwera kuti, ‘Usawakanize! Bweretsa ana anga aamuna kuchokera kutali, ndi ana anga aakazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+  Bweretsa aliyense amene amatchedwa ndi dzina langa,+ amene ndinamulenga chifukwa cha ulemerero wanga,+ amene ndinamuumba ndiponso amene ndinamupanga.’+  “Bweretsa anthu akhungu ngakhale kuti ali ndi maso, ndiponso anthu ogontha ngakhale kuti ali ndi makutu.+  Mitundu yonse isonkhanitsidwe pamalo amodzi, ndipo mitundu ya anthu ikhale pamodzi.+ Ndani pakati pawo amene anganene zimenezi?+ Kapena ndani amene angatiuze zinthu zimene zidzayambirire kuchitika?+ Abweretse mboni zawo+ kuti akhale olungama ndipo mbonizo zimve ndi kunena kuti, ‘Zimenezo ndi zoona!’”+ 10  “Inu ndinu mboni zanga,”+ akutero Yehova. “Ndinu mtumiki wanga amene ndakusankhani+ kuti mundidziwe+ ndi kundikhulupirira,+ komanso kuti mumvetse kuti ine sindinasinthe.+ Ine ndisanakhaleko kunalibe Mulungu amene anapangidwa,+ ndipo pambuyo panga palibenso wina.+ 11  Ine ndine Yehova.+ Popanda ine palibenso mpulumutsi wina.”+ 12  “Ine ndanena ndipo ndapulumutsa.+ Pa nthawi imene pakati panu panalibe mulungu wachilendo,+ ine ndinachititsa kuti chipulumutsocho chimveke. Choncho inuyo ndinu mboni zanga,+ ndipo ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.+ 13  “Komanso, nthawi zonse ine sindisintha.+ Palibenso wina amene angathe kupulumutsa anthu m’dzanja langa.+ Ndikayamba kuchitapo kanthu,+ ndani amene angalimbane ndi dzanja langa?”+ 14  Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti: “Chifukwa cha inu, ndidzawatumiza ku Babulo. Ndidzachititsa kuti zitsulo za ndende zimasuke+ ndiponso ndidzagonjetsa Akasidi amene ali m’zombo ndi kuwachititsa kulira mokuwa.+ 15  Ine ndine Yehova, Woyera wanu,+ Mlengi wa Isiraeli+ ndiponso Mfumu yanu.”+ 16  Izi n’zimene Yehova wanena, yemwe amapanga njira panyanja. Amapanga msewu ngakhale pamadzi amphamvu.+ 17  Amatsogolera magaleta ankhondo ndi mahatchi, komanso gulu lankhondo ndi asilikali amphamvu pa nthawi imodzi.+ Iye wanena kuti: “Iwo adzagona pansi,+ sadzadzuka+ ndipo adzatha.+ Adzazimitsidwa ngati chingwe cha nyale.”+ 18  “Musakumbukire zinthu zoyambirira, ndipo musaganizirenso zinthu zakale. 19  Taonani! Ndikupanga zinthu zatsopano.+ Zimenezi zionekera ndipo anthu inu muzidziwa ndithu.+ M’chipululu, ine ndidzatsegulamo njira+ ndi mitsinje.+ 20  Zilombo zakutchire zidzanditamanda.+ Mimbulu ndi nthiwatiwa+ zidzanditamanda chifukwa ndidzapereka madzi ndi mitsinje m’chipululu,+ kuti anthu anga, wosankhidwa wanga,+ amwe, 21  ndiponso kuti anthu amene ndinawapanga kuti akhale anga, anene za ulemerero wanga.+ 22  “Koma iwe Yakobo, iwe Isiraeli, sunapemphe thandizo kwa ine+ chifukwa chakuti watopa nane.+ 23  Iwe sunandibweretsere nkhosa zako zansembe zopsereza zathunthu. Sunandilemekeze ndi nsembe zako.+ Ine sindinakuumirize kuti uzindipatsa mphatso ndipo sindinakutopetse n’kukupempha lubani.*+ 24  Iwe sunandigulire bango lonunkhira+ ndi ndalama iliyonse, ndipo sunandikhutitse ndi mafuta a nsembe zako.+ Koma m’malomwake, wandiumiriza ndi machimo ako kuti ndikutumikire. Wanditopetsa ndi zolakwa zako.+ 25  “Ineyo ndi amene ndikufafaniza+ zolakwa zako,+ ndipo machimo ako sindidzawakumbukiranso.+ 26  Tiye tikhale pa mlandu. Ndikumbutse.+ Fotokoza mbali yako kuti iweyo ukhale wosalakwa.+ 27  Bambo wako, woyamba uja, anachimwa+ ndipo anthu okulankhulira andilakwira.+ 28  Chotero ndidzadetsa akalonga a pamalo oyera. Yakobo ndidzamuwononga ndipo Isiraeli ndidzamunyozetsa.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.