Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 41:1-29

41  “Zilumba inu,+ mvetserani mawu anga mutakhala chete, ndipo mitundu ya anthu+ ipezenso mphamvu. Ibwere pafupi,+ kenako ilankhule. Anthu inu bwerani kufupi nane kumalo oweruzira mlandu.+  “Kodi ndani anautsa winawake kuchokera kotulukira dzuwa?+ Kodi ndani anamuitana mwachilungamo kuti ayandikire kumapazi ake, kuti amupatse mitundu ya anthu pamaso pake, ndiponso kuti amuchititse kupita kukagonjetsa ngakhale mafumu?+ Kodi ndani amene anali kuwapereka kulupanga lake ngati fumbi, moti auluzika ndi uta wake ngati mapesi?+  Kodi ndani amene anali kuwathamangitsa? Ndani amene anali kuyenda mwamtendere ndi mapazi ake panjira imene anali asanadutsepo n’komwe?  Ndani wachita zimenezi,+ kuitana mibadwo kuyambira pa chiyambi?+ “Ndineyo Yehova, Woyamba,+ ndipo ndidzakhala chimodzimodzi ngakhale kwa omalizira.”+  Zilumba+ zinaona n’kuyamba kuopa. Malekezero a dziko lapansi anayamba kunjenjemera.+ Mitundu ya anthu inasonkhana pamodzi n’kumangobwerabe.  Aliyense anali kuthandiza mnzake, ndipo munthu anali kuuza mbale wake kuti: “Limba mtima.”+  Chotero mmisiri wa mitengo anali kulimbikitsa mmisiri wa zitsulo.+ Amene anali kusalaza zitsulo ndi nyundo anali kulimbikitsa amene anali kumenya zitsulo ndi nyundo. Ponena za ntchito yowotcherera zitsulo ndi mtovu, iye anati: “Zili bwino.” Pomalizira pake, wina anakhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwedezeke.+  “Koma iwe Isiraeli, ndiwe mtumiki wanga,+ iwe Yakobo amene ndakusankha,+ mbewu ya bwenzi langa+ Abulahamu.+  Ndakutenga kuchokera kumalekezero a dziko lapansi,+ ndiponso ndakuitana kuchokera kumadera akutali a dziko lapansi.+ Chotero ndinakuuza kuti, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga.+ Ndasankha iweyo+ ndipo sindinakutaye.+ 10  Usachite mantha, pakuti ndili nawe.+ Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.+ Ndikulimbitsa.+ Ndithu ndikuthandiza.+ Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja+ lachilungamo.’+ 11  “Taona! Onse okupsera mtima adzachita manyazi ndipo adzanyozeka.+ Anthu amene akukangana nawe sadzakhalanso ngati kanthu ndipo adzatha.+ 12  Anthu amene akulimbana nawe udzawafunafuna koma sudzawapeza. Anthu amene akumenyana nawe+ adzakhala ngati kulibeko ndipo sadzakhalanso ngati kanthu.+ 13  Pakuti ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja.+ Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha.+ Ineyo ndikuthandiza.’+ 14  “Usachite mantha, nyongolotsi iwe+ Yakobo, inuyo amuna a Isiraeli.+ Ineyo ndikuthandizani,” akutero Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli. 15  “Taona! Ndakusandutsa chopunthira mbewu,+ chida chatsopano chopunthira mbewu chokhala ndi mano. Udzapondaponda mapiri n’kuwaphwanya, ndipo zitunda udzazisandutsa mankhusu.+ 16  Udzapeta+ mapiri ndi zitundazo ndipo mphepo idzaziuluza.+ Mphepo yamkuntho idzaziuluzira kumalo osiyanasiyana.+ Iweyo udzasangalala chifukwa cha Yehova.+ Udzadzitama chifukwa cha Woyera wa Isiraeli.”+ 17  “Anthu ozunzika ndi osauka akufunafuna madzi,+ koma sakuwapeza. Lilime lawo lauma ndi ludzu.+ Ineyo Yehova ndidzawayankha.+ Ineyo Mulungu wa Isiraeli, sindidzawasiya.+ 18  Ndidzatsegula mitsinje pamapiri opanda zomera zilizonse, ndipo pakatikati pa zigwa ndidzatsegulapo akasupe.+ Chipululu ndidzachisandutsa dambo lamadzi, ndipo dziko lopanda madzi ndidzalisandutsa pochokera madzi.+ 19  M’chipululu ndidzabzalamo mtengo wa mkungudza, mtengo wa mthethe, mtengo wa mchisu, ndi mtengo wamafuta.+ M’dera lachipululu ndidzabzalamo mtengo wofanana ndi mkungudza, mtengo wa ashi,* ndi mtengo wa paini pa nthawi imodzimodziyo.+ 20  Ndidzachita zimenezi kuti anthu onse pamodzi aone, adziwe, amve, ndiponso azindikire, kuti dzanja la Yehova ndi limene lachita zimenezi, ndiponso kuti Woyera wa Isiraeli ndi amene wachititsa zimenezi.”+ 21  “Bweretsani kuno mlandu wanu wovuta,”+ akutero Yehova. “Nenani mfundo zanu,”+ ikutero Mfumu ya Yakobo.+ 22  “Tionetseni ndipo mutiuze zinthu zimene zidzachitike. Tiuzeni kuti zinthu zoyambirira zinali zotani, kuti tiziganizire mozama mumtima mwathu ndi kudziwa tsogolo lake. Kapena mutiuze zinthu zimene zikubwera.+ 23  Nenani zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, kuti tidziwe kuti inu ndinu milungu.+ Inde, muyenera kuchita zabwino kapena zoipa, kuti tizionere limodzi ndi kuchita mantha.+ 24  Taonani! Inuyo sindinu kanthu ndipo zimene mwachita si kanthu.+ Aliyense wokusankhani ndi wochititsa nyansi.+ 25  “Ine ndautsa winawake kuchokera kumpoto, ndipo abwera.+ Iye adzaitana pa dzina langa kuchokera kotulukira dzuwa.+ Adzaukira atsogoleri ngati kuti ndi dongo+ ndiponso ngati kuti iyeyo ndi woumba amene amapondaponda dongo laliwisi. 26  “Kodi ndani wanenapo chilichonse kuchokera pa chiyambi kuti tidziwe, kapena kuchokera nthawi zakalekale kuti tinene kuti, ‘Akunena zoona’?+ Ndithu palibe amene akunena chilichonse. Ndithu palibe amene akulankhula chilichonse kuti anthu amve. Ndithu palibe aliyense amene akumva mawu alionse a anthu inu.”+ 27  Pali woyamba, amene akunena kwa Ziyoni kuti: “Tamverani zimene zidzachitike!”+ Yerusalemu ndidzamupatsa munthu wobweretsa uthenga wabwino.+ 28  Ndinapitiriza kuyang’ana, koma panalibe munthu aliyense. Pakati pa mafanowo panalibe aliyense amene anali kupereka malangizo,+ ndipo ndinapitiriza kuwafunsa kuti ayankhe. 29  Onsewo ali ngati chinthu choti kulibeko. Ntchito zawo si kanthu. Mafano awo opangidwa ndi zitsulo zosungunula ali ngati mphepo ndiponso zinthu zomwe si zenizeni.+

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mtengo waukulu umene umatalika mpaka mamita 15. Umakhala ndi masamba osabiriwira kwambiri ndi nthambi zotuwa ngati phulusa.