Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 38:1-22

38  M’masiku amenewo, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pang’ono kufa.+ Choncho mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi anabwera kwa iye n’kumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Uza banja lako zochita,+ chifukwa iweyo ufa ndithu. Sukhala ndi moyo.’”+  Atamva mawu amenewa, Hezekiya anatembenukira kukhoma+ n’kuyamba kupemphera kwa Yehova.+  Iye anapemphera kuti: “Ndikukupemphani inu Yehova, chonde kumbukirani+ kuti ndinayenda+ pamaso panu mokhulupirika+ ndiponso ndi mtima wathunthu,+ komanso ndinachita zabwino pamaso panu.” Kenako Hezekiya anayamba kulira kwambiri.+  Tsopano Yehova analankhula+ ndi Yesaya kuti:  “Pita, kauze Hezekiya kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako+ wanena kuti: “Ndamva pemphero lako,+ ndipo ndaona misozi yako.+ Tsopano ndiwonjezera zaka 15 pa masiku ako.+  Ndidzalanditsa iweyo ndi mzindawu m’manja mwa mfumu ya Asuri, ndipo ndidzateteza mzinda uno.+  Chizindikiro chochokera kwa Yehova, chakuti Yehova adzakwaniritsadi mawu amene walankhula, ndi ichi:+  Ndichititsa mthunzi wa dzuwa+ umene wapita kale kutsogolo pamasitepe a Ahazi, kuti ubwerere m’mbuyo masitepe 10.”’”+ Choncho dzuwa linabwerera m’mbuyo pang’onopang’ono masitepe 10 pa masitepe pomwe linali litapita kale kutsogolo.+  Hezekiya mfumu ya Yuda atadwala+ n’kuchira, analemba zotsatirazi.+ 10  Ine ndinati: “Pakatikati pa masiku anga ndidzalowa pazipata+ za Manda. Ndidzamanidwa zaka zanga zotsala.”+ 11  Ndanena kuti: “Sindidzamuona Ya.* Ndithu Ya sindidzam’penya m’dziko la amoyo.+ Anthu sindidzawaonanso. Ndidzakhala ndi anthu okhala kudziko limene kulibe moyo. 12  Malo anga okhala ali ngati hema wa abusa. Mitengo yake yazulidwa ndipo hemayo wachotsedwapo.+ Ndakulunga moyo wanga ngati munthu wowomba nsalu. Winawake wandidula+ ngati mmene amadulira nsalu kuchowombera nsalu akamaliza kuiwomba. Kuyambira m’mawa mpaka usiku mumandipereka ku zowawa.+ 13  Ndadzitonthoza mpaka m’mawa.+ Mafupa anga onse, iye akungokhalira kuwaphwanya ngati mkango.+ Kuyambira m’mawa mpaka usiku mukungokhalira kundipereka ku zowawa.+ 14  Ndikungokhalira kulira ngati namzeze* kapena pumbwa.*+ Ndikungokhalira kubuula ngati njiwa.+ Maso anga akupenyetsetsa kumwamba motopa. Choncho ndinati:+ ‘Inu Yehova ine ndapanikizika. Chonde ndithandizeni.’+ 15  Kodi ndinene kuti chiyani? Kodi iyeyo andiuza kuti chiyani?+ Iyeyonso wachitapo kanthu.+ Zaka zanga zonse, ndikungokhalira kuyenda ndili khuma chifukwa cha chisoni cha mtima wanga.+ 16  ‘Ndi mawu anu, anthu amakhalabe ndi moyo inu Yehova, ndipo mofanana ndi wina aliyense, mzimu wanga umapeza moyo kudzera mu zochita zanu.+ Inu mudzandibwezera thanzi langa n’kundisiya ndi moyo.+ 17  M’malo mopeza mtendere ndinapeza zowawa, zowawatu zedi!+ Inuyo mwamamatira moyo wanga ndipo mwauteteza kuti usapite kudzenje la chiwonongeko.+ Pakuti machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu.+ 18  Pakuti Manda sangakutamandeni.+ Imfa singakulemekezeni.+ Anthu amene akutsikira kudzenje sangayembekezere kukhulupirika kwanu.+ 19  Munthu wamoyo, amene akupuma, ndi amene angakutamandeni,+ Ngati mmene ineyo ndikuchitira lero.+ Bambo akhoza kuphunzitsa+ ana ake za kukhulupirika kwanu. 20  Inu Yehova bwerani mudzandipulumutse,+ ndipo tidzaimba nyimbo zimene ine ndinapeka. Ndidzaimba ndi zoimbira za zingwe+ Kunyumba ya Yehova masiku onse a moyo wathu.’”+ 21  Kenako Yesaya anati: “Anthu atenge nkhuyu zouma zoumba pamodzi ndipo azikhukhutize pachithupsa+ chimene ali nacho kuti achire.”+ 22  Pa nthawiyi, Hezekiya anati: “Kodi chizindikiro chakuti ndidzapita kunyumba ya Yehova n’chiyani?”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 15:2.
Mbalame imeneyi ena amati “kaluweluwe” kapena “kamembe.”
Mbalame imeneyi ena amati “nyapwere.”