Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 37:1-38

37  Mfumu Hezekiya itangomva zimenezi, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake n’kuvala chiguduli.+ Kenako inapita m’nyumba ya Yehova.+  Komanso inatuma Eliyakimu+ amene anali woyang’anira banja la mfumu, Sebina mlembi,+ ndi akuluakulu a ansembe,+ onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi.+  Iwo anamuuza kuti: “Hezekiya wanena kuti, ‘Lero ndi tsiku la zowawa+ ndi lodzudzula, tsiku la mnyozo ndi mwano.+ Tili ngati mkazi amene watsala pang’ono kubereka, koma alibe mphamvu zoti aberekere.+  Mwina Yehova Mulungu amva mawu onse a Rabisake,+ amene mbuye wake mfumu ya Asuri yamutuma, kuti adzatonze+ nawo Mulungu wamoyo. Ndipo mwina amulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva.+ Inuyo mupereke pemphero+ m’malo mwa otsalira amene alipo.’”+  Choncho atumiki a Mfumu Hezekiya anafika kwa Yesaya.+  Ndiyeno Yesaya anawauza kuti: “Mukauze mbuye wanu kuti, ‘Yehova wanena kuti:+ “Usachite mantha+ chifukwa cha mawu amene wamva, amene atumiki+ a mfumu ya Asuri andilankhulira monyoza.  Ndiika maganizo+ mwa iye, kuti akamva nkhani inayake,+ abwerere kudziko lake. Ndipo mosalephera, ndidzachititsa kuti akaphedwe ndi lupanga m’dziko lake.”’”+  Rabisake+ anali atamva kuti mfumu ya Asuri yachoka ku Lakisi,+ choncho anabwerera kwa mfumuyo n’kukaipeza ikumenyana ndi Libina.+  Tsopano mfumuyo inamva kuti Tirihaka+ mfumu ya Itiyopiya wabwera kudzamenyana nayo. Itangomva zimenezo, nthawi yomweyo inatumizanso amithenga+ kwa Hezekiya n’kuwauza kuti: 10  “Amuna inu mukamuuze Hezekiya mfumu ya Yuda kuti, ‘Usalole Mulungu wako amene ukumudalira kuti akunamize,+ ponena kuti: “Yerusalemu saperekedwa m’manja mwa mfumu ya Asuri.”+ 11  Iweyo wamva zimene mafumu a Asuri anachita kumayiko onse mwa kuwawononga.+ Ndiye kodi iweyo ukuona ngati upulumuka?+ 12  Kodi milungu+ ya mitundu imene makolo anga anaiwononga inawalanditsa?+ Kodi inalanditsa Gozani,+ Harana,+ Rezefi ndi ana a Edeni+ amene anali ku Tela-sara? 13  Ili kuti mfumu ya Hamati,+ mfumu ya Aripadi,+ ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu,+ Hena, ndi Iva?’”+ 14  Kenako Hezekiya anatenga kalatayo m’manja mwa amithengawo n’kuiwerenga.+ Pambuyo pake iye anapita nayo kunyumba ya Yehova, n’kuitambasula pamaso pa Yehova.+ 15  Ndiyeno Hezekiya anayamba kupemphera kwa Yehova,+ kuti: 16  “Inu Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli+ wokhala pa akerubi, inu nokha ndinu Mulungu woona wa maufumu onse a padziko lapansi.+ Inuyo munapanga kumwamba ndi dziko lapansi.+ 17  Tcherani khutu lanu, inu Yehova, mumve.+ Tsegulani maso anu,+ inu Yehova, muone, ndipo imvani mawu onse a Senakeribu+ amene watumiza kudzatonza nawo Mulungu wamoyo.+ 18  N’zoonadi Yehova, kuti mafumu a Asuri awononga mayiko onse, ndi dziko lawo lomwe.+ 19  Atentha milungu yawo pamoto,+ chifukwa sinali milungu,+ koma ntchito ya manja a anthu,+ mitengo ndi miyala, n’chifukwa chake anaiwononga.+ 20  Tsopano inu Yehova Mulungu wathu,+ tipulumutseni m’manja mwake,+ kuti maufumu onse a padziko lapansi adziwe kuti inu Yehova, inu nokha ndiye Mulungu.”+ 21  Ndiyeno Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti wapemphera kwa ine za Senakeribu mfumu ya Asuri,+ 22  awa ndi mawu otsutsana naye amene Yehova wanena: “Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza ndipo wakuseka.+ Kumbuyo kwako, mwana wamkazi wa Yerusalemu wakupukusira mutu.+ 23  Kodi ndani amene iwe wamutonza+ ndi kumulankhula monyoza?+ Ndipo ndani amene iwe wam’kwezera mawu,+ Ndi kum’kwezera maso ako m’mwamba?+ Ndi Woyera wa Isiraeli!+ 24  Kudzera mwa antchito ako watonza Yehova ndipo wanena kuti,+ Ndi magaleta anga ankhondo ambiri, ine,+ Ineyo ndidzakwera ndithu madera amapiri mpaka pamwamba.+ Ndidzafika kumadera akutali kwambiri a Lebanoni+ Ndipo ndidzadula mitengo yake ya mkungudza italiitali, ndi mitengo yake yabwino kwambiri yofanana ndi mkungudza.+ Ndidzalowa kumalo ake okhala akutali kwambiri, kunkhalango yokongola.+ 25  Ndithu ineyo ndidzakumba zitsime ndi kumwa madzi, Ndidzaumitsa ndi mapazi anga ngalande zonse zamadzi za mtsinje wa Nailo+ wa ku Iguputo.’+ 26  Kodi sunamve?+ Kuyambira nthawi zakale izi n’zimene ndidzachite.+ Ndinakonza zimenezi kuyambira masiku amakedzana.+ Tsopano ndizichita.+ Iweyo udzagwira ntchito yosandutsa mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, kukhala yopanda anthu ngati milu ya mabwinja.+ 27  Anthu okhala m’mizindayo adzafooka manja.+ Adzachita mantha kwambiri ndiponso adzachita manyazi.+ Adzakhala ngati zomera zakutchire, ndi udzu wanthete wobiriwira,+ Ngati udzu womera padenga+ ndiponso wa m’mizere ya m’munda, ukawauka ndi mphepo yotentha yakum’mawa.+ 28  Ukakhala phee, ukamatuluka,+ ndiponso ukamalowa, ine ndimadziwa bwino,+ Ndimadziwanso ukandipsera mtima,+ 29  Chifukwa kundipsera mtima kwako+ ndi kufuula kwako zafika m’makutu mwanga.+ Ndithu ndidzakola mphuno yako ndi ngowe yanga, ndipo ndidzamanga zingwe zanga pakamwa pako.+ Kenako ndidzakukoka n’kukubweza kudzera njira imene unadutsa pobwera.”+ 30  “‘Ichi chidzakhala chizindikiro chanu: Chaka chino mudya mbewu zomera zokha zimene zinagwera pansi.+ Chaka chamawa mudzadya mbewu zongomera zokha, koma chaka chamkuja, anthu inu mudzabzale mbewu n’kukolola, ndipo mudzalime minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.+ 31  Anthu a m’nyumba ya Yuda amene adzapulumuke, amene adzatsale,+ ndithu adzazika mizu pansi n’kubereka zipatso m’mwamba.+ 32  Chifukwa anthu otsala adzachoka ku Yerusalemu,+ ndipo opulumuka adzachoka kuphiri la Ziyoni.+ Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+ 33  “‘Chotero Yehova wanena izi zokhudza mfumu ya Asuri:+ “Sadzalowa mumzinda uno,+ kapena kuponyamo muvi, kapena kufikamo ndi chishango, kapenanso kumanga chiunda chomenyerapo nkhondo pafupi ndi mpanda wa mzindawu atauzungulira.”’+ 34  “‘Adzabwerera kudzera njira imene anadutsa pobwera, ndipo sadzalowa mumzinda uno,’ ndiwo mawu a Yehova.+ 35  ‘Ndithu ndidzateteza+ mzinda uno kuti ndiupulumutse chifukwa cha ine mwini+ ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’”+ 36  Ndiyeno mngelo+ wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri n’kukapha asilikali 185,000.+ Anthu podzuka m’mawa, anangoona kuti onse aja ndi mitembo yokhayokha.+ 37  Choncho Senakeribu+ mfumu ya Asuri anachokako n’kubwerera+ kukakhala ku Nineve.+ 38  Pamene Senakeribu anali kugwada m’kachisi wa mulungu wake+ Nisiroki,+ ana ake Adarameleki ndi Sarezere anamupha ndi lupanga,+ iwo n’kuthawira kudziko la Ararati.+ Kenako Esari-hadoni+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

Mawu a M'munsi