Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 34:1-17

34  Mitundu inu, bwerani pafupi kuti mumve.+ Inu mitundu ya anthu,+ mvetserani. Dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo zimvetsere.+ Nthaka ya padziko lapansi+ ndi zonse zimene zili pamenepo zimve.+  Pakuti Yehova wakwiyira mitundu yonse.+ Wapsera mtima asilikali awo onse.+ Iye awawononga ndipo awapha.+  Anthu awo ophedwa adzatayidwa, ndipo fungo loipa la mitembo yawo lidzakwera m’mwamba.+ Mapiri adzasungunuka chifukwa cha magazi awo.+  Makamu onse akumwamba adzawola.+ Kumwamba kudzapindidwa ngati mpukutu wolembapo.+ Makamu onse akumwambawo adzafota ngati mmene masamba amafotera pamtengo wa mpesa n’kuthothoka, ndiponso ngati mmene nkhuyu yonyala imathothokera mumtengo wa mkuyu.+  “Pakuti lupanga langa+ lidzakhala magazi okhaokha kumwambako. Lupangalo lidzatsikira pa Edomu+ ndi pa anthu amene ndikufuna kuwawononga+ mogwirizana ndi chilungamo changa.  Yehova ali ndi lupanga. Lupangalo lidzakhala magazi okhaokha+ ndipo lidzaterera ndi mafuta. Lidzadzaza magazi a nkhosa zamphongo zing’onozing’ono ndi a mbuzi zamphongo. Lidzaterera ndi mafuta+ a impso za nkhosa zamphongo, pakuti Yehova adzapereka nsembe ku Bozira ndipo adzapha nyama zambiri m’dziko la Edomu.+  Ng’ombe zamphongo zam’tchire+ zidzatsetserekera nawo kumeneko, zing’onozing’ono ndi zamphamvu zomwe.+ Dziko lawo lidzakhala magazi okhaokha, ndipo fumbi lawo lidzanona ndi mafuta.”+  Pakuti Yehova ali ndi tsiku lobwezera adani ake,+ ndi chaka chopereka chilango, chifukwa cha zolakwa zimene Ziyoni anachitiridwa.+  Mitsinje yake* idzasintha n’kukhala phula. Fumbi lake lidzakhala sulufule, ndipo dziko lake lidzakhala ngati phula loyaka moto.+ 10  Usana ndi usiku, motowo sudzazima. Utsi wake uzidzakwera m’mwamba mpaka kalekale.+ Dzikolo lidzakhala louma ku mibadwomibadwo.+ Mpaka muyaya palibe amene adzadutseko.+ 11  Mbalame zotchedwa vuwo ndi nungu zidzakhala kumeneko. Komanso akadzidzi a makutu ataliatali ndi akhwangwala azidzakhala kumeneko.+ Iye adzatambasulira dzikolo chingwe choyezera+ malo opanda kanthu, ndiponso miyala yoyezera kuwongoka kwa chinthu. 12  Palibe aliyense wochokera pa anthu ake olemekezeka amene adzakhale mfumu, ndipo akalonga ake onse adzatha.+ 13  Minga zidzamera pansanja zake zokhalamo. Zomera zoyabwa ndi zitsamba zaminga zidzamera pamalo ake otetezeka,+ ndipo iye adzakhala malo okhala mimbulu+ ndi bwalo la nthiwatiwa.+ 14  Nyama zokhala kumadera opanda madzi zidzakumana ndi nyama zolira mokuwa, ndipo ngakhale ziwanda zooneka ngati mbuzi,*+ zizidzaitanizana kumeneko. Mbalame yotchedwa lumbe izidzasangalalako n’kupezako malo okhala.+ 15  Kumeneko, njoka yodumpha idzakonzako chisa chake n’kuikira mazira. Idzakhalira mazirawo n’kuswa tiana, ndipo idzatisonkhanitsa pansi pa mthunzi wake. Mbalame zotchedwa akamtema+ zidzasonkhana kumeneko iliyonse ndi mwamuna wake. 16  Fufuzani m’buku+ la Yehova ndipo muwerenge mokweza. Palibe ndi imodzi yomwe imene ikusowekapo.+ Zonsezo sizilephera kupeza mwamuna, chifukwa pakamwa pa Yehova ndi pamene palamula.+ Mzimu wake ndi umene wazisonkhanitsa pamodzi.+ 17  Iye ndi amene waziponyera maere, ndipo dzanja lake lazigawira malowo ndi chingwe choyezera.+ Zidzakhala kumeneko mpaka kalekale. Kudzakhala kwawo ku mibadwomibadwo.

Mawu a M'munsi

“Yake” akuimira Bozira, likulu la Edomu.
Onani mawu a m’munsi pa Yes 13:21.