Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 33:1-24

33  Tsoka iwe amene ukulanda zinthu koma iweyo osalandidwa. Tsoka kwa iwe amene ukuchita zachinyengo pamene ena sanakuchitire zachinyengo. Ukadzangomaliza kulanda, nawenso udzalandidwa.+ Ukadzangomaliza kuchitira ena zachinyengo, iwonso adzakuchitira zachinyengo.+  Inu Yehova, tikomereni mtima.+ Ife tikudalira inu.+ Tilimbitseni ndi dzanja lanu+ m’mawa uliwonse.+ Mukhale chipulumutso chathu pa nthawi ya masautso.+  Mitundu ya anthu yathawa itamva mkokomo wa mawu anu.+ Mitundu yamwazikana chifukwa chakuti inu mwanyamuka.+  Zinthu zimene anthu inu munalanda ena zidzasonkhanitsidwa ngati mphemvu zikasonkhana pamodzi, ndiponso ngati chigulu cha dzombe chimene chikukhamukira kwa munthu.+  Yehova adzakwezedwa pamwamba,+ pakuti amakhala pamalo apamwamba.+ Iye adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo.+  M’masiku anu, kukhulupirika kudzabweretsa chipulumutso chachikulu.+ Nazonso nzeru, kudziwa zinthu,+ ndi kuopa Yehova,+ komwe ndiko chuma chake zidzabweretsa chipulumutso chachikulu.  Ndipotu anthu awo otchuka adzalira mofuula m’misewu. Amithenga a mtendere+ adzalira momvetsa chisoni.  Misewu ikuluikulu yawonongeka. Palibenso munthu woyenda m’njira.+ Iye waphwanya pangano ndipo wanyansidwa ndi mizinda. Sasamala za munthu aliyense.  Dzikolo likulira, lafota.+ Lebanoni wachita manyazi, wanyala.+ Sharoni+ wakhala ngati chipululu ndipo Basana ndi Karimeli akuyoyola masamba awo.+ 10  Yehova wati: “Tsopano ndinyamuka,+ ndidzikweza.+ Tsopano ndidziika pamwamba.+ 11  Anthu inu muli ndi pakati pa udzu wouma+ ndipo mudzabereka mapesi. Mzimu wanu udzakunyeketsani+ ngati moto.+ 12  Mitundu ya anthu idzakhala ngati zotsala za laimu akatenthedwa. Iwo adzayaka ndi moto ngati minga zimene zasadzidwa. 13  Anthu inu amene muli kutali, imvani zimene ndikufuna kuchita.+ Inu amene muli pafupi, dziwani mphamvu zanga.+ 14  Mu Ziyoni, anthu ochimwa akuchita mantha.+ Opanduka akunjenjemera kwambiri.+ Akufunsa kuti: ‘Ndani wa ife angakhale pambali pa moto wowononga? Ndani wa ife angakhale pafupi ndi moto woyaka kwambiri wosatherapo?’+ 15  “Pali munthu amene amayenda m’chilungamo nthawi zonse,+ amene amalankhula zowongoka, amene amakana kupeza phindu mwachinyengo, amene salola kuti manja ake alandire chiphuphu, amene amatseka makutu ake kuti asamve nkhani zokhudza kukhetsa magazi, ndiponso amene amatseka maso ake kuti asaone zoipa.+ 16  Iye ndi amene adzakhale pamalo apamwamba.+ Malo ake okhala adzakhala otetezeka m’matanthwe movuta kufikamo.+ Iye adzapatsidwa chakudya+ ndipo madzi ake sadzatha.”+ 17  Maso ako adzaona kukongola kwa mfumu.+ Adzaona dziko lakutali.+ 18  Mtima wako udzalankhula motsitsa mawu+ za chinthu choopsa kuti: “Kodi mlembi ali kuti? Kodi wopereka malipiro uja ali kuti? Uja amawerenga nsanjayu ali kuti?” 19  Simudzaona anthu achipongwe, amene chilankhulo chawo n’chovuta kumva, anthu achibwibwi olankhula zinthu zovuta kumva. 20  Taonani Ziyoni,+ tauni yathu yochitiramo zikondwerero. Maso anu adzaona Yerusalemu, amene ndi malo okhala aphee, opanda chosokoneza chilichonse. Iye ndi hema woti palibe amene adzamuchotse.+ Zikhomo zake sizidzazulidwa ndipo zingwe zake sizidzaduka.+ 21  Koma kumeneko, Yehova Wolemekezeka+ adzakhala malo a mitsinje+ ndi a ngalande zikuluzikulu kwa ife. Kumalo amenewo sikudzadutsa gulu la ngalawa kapena zombo zikuluzikulu. 22  Pakuti Yehova ndiye Woweruza wathu. Yehova ndiye Wotipatsa Malamulo. Yehova ndiye Mfumu yathu.+ Iye adzatipulumutsa.+ 23  Zingwe zidzakhala zosamanga. Mtengo wautali wa pangalawa sadzatha kuuimika mowongoka. Chinsalu chapangalawayo sadzatha kuchitambasula. Pa nthawi imeneyo adzagawana zofunkha zambirimbiri. Ngakhale anthu olumala adzatenga nawo katundu wambiri wofunkha. 24  Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: “Ndikudwala.” Anthu okhala mmenemo adzakhala amene machimo awo anakhululukidwa.+

Mawu a M'munsi