Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 2:1-22

2  Zinthu zimene Yesaya mwana wa Amozi anaona zokhudza Yuda ndi Yerusalemu:+  M’masiku otsiriza,+ phiri la nyumba+ ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa nsonga za mapiri,+ ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa mapiri ang’onoang’ono.+ Mitundu yonse idzakhamukira kumeneko.+  Anthu ochokera m’mitundu yosiyanasiyana adzabwera n’kunena kuti: “Bwerani+ anthu inu. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova. Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo. Iye akatiphunzitsa njira zake, ndipo ife tidzayenda m’njira zakezo.”+ Pakuti mu Ziyoni mudzatuluka malamulo ndipo mawu a Yehova adzatuluka mu Yerusalemu.+  Mulungu adzakhala woweruza pakati pa mitundu+ ndipo adzakonza zinthu+ zokhudza mitundu yambiri ya anthu.+ Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo.+ Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.+  Inu amuna a m’nyumba ya Yakobo, bwerani tidzayende m’kuwala kwa Yehova.+  Pakuti mwawanyanyala anthu anu, nyumba ya Yakobo.+ Iwo adzaza ndi zinthu zochokera Kum’mawa.+ Akuchita zamatsenga+ ngati Afilisiti ndiponso ali ndi ana ambiri a alendo.+  Dziko lawo ladzaza ndi siliva ndi golide, ndipo ali ndi chuma chopanda malire.+ Dziko lawo ladzaza ndi mahatchi,* ndipo ali ndi magaleta* osawerengeka.+  Dziko lawo ladzaza ndi milungu yopanda phindu.+ Iwo amagwadira ntchito ya manja awo. Amagwadira chinthu chimene zala zawo zapanga.+  Anthu ochokera kufumbi anyozeka. Iwo atsika ndipo simungathe kuwakhululukira.+ 10  Lowani muthanthwe ndipo dzibiseni m’fumbi chifukwa cha kuopsa kwa Yehova, ndiponso chifukwa cha ulemerero ndi ukulu wake.+ 11  Maso odzikuza a munthu wochokera kufumbi adzatsika, ndipo anthu odzikweza adzawerama.+ Yehova yekha ndi amene adzakwezedwe pamwamba m’tsiku limenelo.+ 12  Pakuti ilo ndi tsiku la Yehova wa makamu.+ Tsikulo lidzafikira aliyense wodzitukumula ndi wodzikweza. Lidzafikiranso aliyense wokwezeka kapena wotsika.+ 13  Lidzafikira mikungudza yonse ya ku Lebanoni+ yodzikweza ndi yokwezeka. Lidzafikiranso mitengo yonse ikuluikulu ya ku Basana.+ 14  Lidzafikira mapiri onse akuluakulu odzikweza ndi mapiri onse ang’onoang’ono okwezeka.+ 15  Lidzafikiranso nsanja iliyonse yaitali ndi khoma* lililonse lolimba kwambiri.+ 16  Lidzafikira zombo zonse za ku Tarisi,+ ndi ngalawa zonse zabwinozabwino. 17  Munthu wodzikuza wochokera kufumbi adzawerama ndipo anthu odzikweza adzatsitsidwa.+ Yehova yekha ndi amene adzakwezedwe pamwamba m’tsiku limenelo.+ 18  Milungu yopanda phindu idzatheratu.+ 19  Mulungu akadzaimirira kuti dziko lapansi linjenjemere, anthu adzalowa m’mapanga a m’matanthwe ndi m’mayenje a m’nthaka chifukwa cha kuopsa kwa Yehova,+ ndiponso chifukwa cha ulemerero ndi ukulu wake.+ 20  M’tsiku limenelo, munthu wochokera kufumbi adzataya milungu yake yasiliva yopanda pake ndi milungu yake yagolide yopanda phindu, imene anthu anamupangira kuti aziigwadira. Adzaitayira kumene kumakhala aswiswiri* ndi mileme,+ 21  kuti iye abisale m’mayenje a m’matanthwe ndi m’ming’alu ya m’miyala ikuluikulu. Adzachita zimenezi chifukwa cha kuopsa kwa Yehova, ndiponso chifukwa cha ulemerero ndi ukulu wake,+ Mulunguyo akadzaimirira kuti dziko lapansi linjenjemere. 22  Kuti zinthu zikuyendereni bwino, musadalire munthu wochokera kufumbi amene mpweya wake uli m’mphuno mwake,+ pakuti palibe chifukwa choti mum’ganizire iyeyo.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “chipupa,” kapena “chikupa.”
Ena amati “akasusum’njira.”