Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 19:1-25

19  Uwu ndi uthenga wokhudza Iguputo:+ Taonani! Yehova wakwera mtambo wothamanga+ ndipo akubwera mu Iguputo. Milungu yopanda pake ya ku Iguputo idzanjenjemera chifukwa chomuopa+ ndipo mitima ya Aiguputo idzasungunuka mkati mwa dzikolo.+  “Ndidzachititsa kuti Aiguputo ayambane ndi Aiguputo anzawo. Aliyense adzamenyana ndi m’bale wake ndipo aliyense adzamenyana ndi mnzake. Mzinda udzamenyana ndi mzinda unzake ndipo ufumu udzamenyana ndi ufumu unzake.+  Anthu a mu Iguputo adzadabwa kwambiri+ ndipo ine ndidzasokoneza zolinga za dzikolo.+ Iwo adzafunsira kwa milungu yopanda pake,+ kwa anthu amatsenga, kwa olankhula ndi mizimu ndiponso kwa olosera zam’tsogolo.+  Ndidzapereka Iguputo m’manja mwa mbuye wankhanza ndipo mfumu imene idzawalamulire idzakhala yamphamvu,”+ akutero Ambuye woona, Yehova wa makamu.  Madzi adzauma m’nyanja, ndipo mtsinje udzakhala wopanda madzi ndi wouma.+  Mitsinje idzanunkha. Ngalande za ku Iguputo zochokera mumtsinje wa Nailo zidzaphwa ndipo zidzauma.+ Bango+ ndi udzu* zidzafota.  Madambo a m’mphepete mwa mtsinje wa Nailo, malo othera mtsinje wa Nailo, ndi malo onse obzala mbewu m’mphepete mwa mtsinjewo, adzauma.+ Zomera za m’mphepete mwa mtsinjewo zidzauma ndipo zidzauluzika ndi mphepo.  Asodzi a nsomba adzalira ndipo onse oponya mbedza mumtsinje wa Nailo adzamva chisoni. Ngakhale oponya maukonde ophera nsomba pamadziwo adzalefuka.+  Anthu amene amagwiritsira ntchito fulakesi*+ wopalapala pa ntchito yawo adzachita manyazi. Anthu owomba nsalu yoyera adzachitanso manyazi. 10  Anthu ake owomba nsalu+ adzavutika maganizo. Anthu onse ogwira ntchito yolipidwa adzamva chisoni mumtima. 11  Akalonga a ku Zowani+ ndi opusa ndithu. Malangizo a anthu anzeru ochokera pakati pa alangizi a Farao, ndi osathandiza.+ Kodi anthu inu mudzamuuza bwanji Farao kuti: “Ine ndine mwana wa anthu anzeru, mwana wa mafumu akale”? 12  Kodi anthu ako anzeruwo ali kuti?+ Ngati akudziwa, akuuze zimene Yehova wa makamu wakonza zokhudza Iguputo.+ 13  Akalonga a ku Zowani achita zopusa.+ Akalonga a ku Nofi+ anyengezedwa. Atsogoleri+ a mafuko achititsa Iguputo kuyenda uku ndi uku. 14  Yehova waika mzimu wachisokonezo pakati pa dzikolo.+ Atsogoleri awo achititsa Iguputo kuyenda uku ndi uku m’zochita zake zonse, ngati munthu woledzera amene akuterereka m’masanzi ake.+ 15  Sipadzakhala chilichonse choti Iguputo achite, choti mutu kapena mchira komanso mphukira ndi udzu zichite.+ 16  M’tsiku limenelo, Aiguputo adzakhala ngati akazi. Iwo adzanjenjemera+ ndi kuchita mantha, chifukwa Yehova wa makamu adzawatambasulira dzanja lake.+ 17  Dziko la Yuda lidzakhala chinthu choopseza Iguputo.+ Aliyense amene wauzidwa za dzikolo, akuchita mantha chifukwa cha zimene Yehova wa makamu watsimikiza kuwachitira.+ 18  M’tsiku limenelo, padzakhala mizinda isanu m’dziko la Iguputo+ yolankhula chinenero cha ku Kanani+ ndiponso yolumbira+ kwa Yehova wa makamu. Mzinda umodzi udzatchedwa Mzinda wa Chiwonongeko. 19  M’tsiku limenelo, m’dziko la Iguputo mudzakhala guwa lansembe la Yehova,+ ndipo m’malire mwake mudzakhala chipilala cha Yehova. 20  Zimenezi zidzakhala chizindikiro ndi umboni kwa Yehova wa makamu m’dziko la Iguputo,+ pakuti iwo adzalirira Yehova chifukwa cha anthu owapondereza,+ ndipo iye adzawatumizira mpulumutsi wamkulu amene adzawapulumutse.+ 21  Yehova adzadziwika bwino kwa Aiguputo,+ ndipo Aiguputowo adzamudziwa Yehova m’tsiku limenelo. Iwo adzapereka nsembe ndi mphatso+ ndiponso adzachita lonjezo kwa Yehova n’kulikwaniritsa.+ 22  Yehova adzakantha Iguputo.+ Adzamukantha n’kumuchiza,+ ndipo iwo adzabwerera kwa Yehova.+ Iye adzamva kuchonderera kwawo ndipo adzawachiritsa.+ 23  M’tsiku limenelo, padzakhala msewu waukulu+ wochokera ku Iguputo kupita ku Asuri. Anthu a ku Asuri adzapita ku Iguputo ndipo anthu a ku Iguputo adzapita ku Asuri. Aiguputo ndi Asuri adzatumikira Mulungu limodzi. 24  M’tsiku limenelo, Isiraeli adzakhala gawo limodzi mwa magawo atatu, pamodzi ndi Iguputo ndi Asuri,+ kutanthauza kuti adzakhala dalitso padziko lapansi,+ 25  popeza Yehova wa makamu adzawadalitsa+ n’kuwauza kuti: “Adalitsike Aiguputo anthu anga, Asuri+ ntchito ya manja anga, ndi Aisiraeli cholowa changa.”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mlulu.”
“Fulakesi” ndi mbewu imene anali kulima ku Iguputo. Anali kuigwiritsa ntchito popanga ulusi wowombera nsalu.