Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 15:1-9

15  Uwu ndi uthenga wokhudza Mowabu:+ Chifukwa chakuti wasakazidwa usiku, Ari+ wa ku Mowabu wakhala chete. Chifukwa chakuti wasakazidwa usiku, Kiri+ wa ku Mowabu wakhala chete.  Iye wapita kukachisi ndi ku Diboni.+ Wapita kumalo okwezeka kukalira. Mowabu akulira mofuula chifukwa cha Nebo+ ndi Medeba.+ Anthu onse a mmenemo ameta mipala.+ Ndevu za munthu aliyense zametedwa.  Anthu avala ziguduli+ m’misewu yake. Pamadenga*+ ake ndi m’mabwalo a mizinda yake, aliyense akufuula. Akulira n’kumapita kumunsi.+  Hesiboni ndi Eleyale+ akulira mofuula. Mawu awo amveka mpaka ku Yahazi.+ N’chifukwa chake amuna onyamula zida a ku Mowabu akungofuula. Mitima yawo ikuchita mantha kwambiri.  Mtima wanga ukulirira Mowabu.+ Anthu ake athawira kutali, ku Zowari+ ndi ku Egilati-selisiya.+ Aliyense akumakwera mtunda wa Luhiti+ akulira. Panjira yopita ku Horonaimu,+ iwo akufuula kwambiri chifukwa cha tsokalo.  Madzi a ku Nimurimu+ aumiratu. Msipu wauma. Udzu watha. Palibenso chobiriwira.+  N’chifukwa chake akumanyamula zinthu zotsala ndi katundu amene anasunga, n’kumapita nazo kuchigwa* cha mitengo ya msondodzi.  Mfuu yamveka m’dziko lonse la Mowabu.+ Kufuula kwake kwamveka mpaka ku Egilaimu. Kufuula kwake kwamveka mpaka ku Beere-elimu,  chifukwa m’madzi onse a ku Dimoni mwadzaza magazi. Dimoni ndidzam’bweretsera zinthu zinanso, monga mikango yoti idye anthu othawa ku Mowabu ndi anthu otsala panthaka yawo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “tsindwi.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.