Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 14:1-32

14  Pakuti Yehova adzachitira chifundo Yakobo ndipo adzasankhanso Isiraeli.+ Iye adzawapatsa mpumulo m’dziko lawo. Alendo adzakhala nawo limodzi ndipo adzadziphatika kunyumba ya Yakobo.  Anthu a mitundu ina adzawatenga n’kubwerera nawo kwawo ndipo nyumba ya Isiraeli idzatenga anthuwo kuti akhale awo m’dziko la Yehova, ndiponso kuti akhale antchito awo aamuna ndi aakazi. Iwo adzagwira+ anthu amene anawagwira n’kupita nawo kudziko lina ndipo azidzalamulira anthu amene anali kuwagwiritsa ntchito.  M’tsiku limene Yehova adzakupatseni mpumulo ku ululu wanu, ku nsautso yanu ndi ku ukapolo wowawa umene inu munalimo,  mudzanene mwambi uwu wotonza mfumu ya Babulo: “Uja ankagwiritsa ntchito anzakeyu wasiya ndithu! Wopondereza uja waleka ndithu!+  Yehova wathyola ndodo ya anthu oipa, ndodo ya anthu olamulira,+  amene anali kumenya mwaukali anthu a mitundu yosiyanasiyana powakwapula mosalekeza, ndiponso amene anali kugonjetsa mitundu ya anthu mokwiya, ndi chizunzo chopanda malire.+  Dziko lonse lapansi lapuma, lilibenso chosokoneza.+ Anthu akusangalala ndipo akufuula mokondwera.+  Ngakhale mitengo ya mlombwa+ yakondwa poona zimene zakuchitikira. Nayonso mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni yakondwa, ndipo yonseyi yanena kuti, ‘Kuyambira pamene unagona pansi, palibenso munthu wodula mitengo+ amene wabwera kudzatidula.’  “Ngakhale Manda+ amene ali pansi agwedezeka kuti akumane nawe ukamabwera. Chifukwa cha iwe, mandawo adzutsa akufa,+ adzutsa olamulira onse a padziko lapansi okhala ngati mbuzi.+ Achititsa mafumu onse a mitundu ya anthu kunyamuka pamipando yawo yachifumu.+ 10  Onsewo akulankhula nawe kuti, ‘Kodi iwenso wafooketsedwa ngati ife?+ Kodi zoonadi wafanana ndi ife?+ 11  Kunyada kwako kwatsikira ku Manda limodzi ndi phokoso la zoimbira zako za zingwe.+ Mphutsi zayalana pansi pako ngati bedi, ndipo nyongolotsi zasanduka chofunda chako.’+ 12  “Wagwa kuchokera kumwamba,+ wonyezimirawe, iwe mwana wa m’bandakucha! Wadulidwa n’kugwera padziko lapansi,+ iwe amene unali kupundula mitundu. 13  Iweyo wanena mumtima mwako kuti, ‘Ndikwera kumwamba.+ Ndikweza mpando wanga wachifumu+ pamwamba pa nyenyezi za Mulungu. Ndikhala paphiri lokumanapo+ kumapeto kwenikweni kwa madera a kumpoto.+ 14  Ndikwera pamwamba pamalo okwezeka a m’mitambo.+ Ndidzipanga kukhala wofanana ndi Wam’mwambamwamba.’+ 15  “Koma adzakutsitsira ku Manda,+ pansi penipeni pa dzenje.+ 16  Okuona adzakuyang’ana modabwa. Adzakuyang’anitsitsa n’kunena kuti, ‘Kodi uyu ndi munthu amene anali kugwedeza dziko lapansi uja, amene anali kunjenjemeretsa maufumu,+ 17  amene anachititsa nthaka kukhala ngati chipululu, amene anagonjetsa mizinda ya padziko lapansi, ndiponso amene sanali kutsegulira njira akaidi ake kuti azipita kwawo?’ 18  Mafumu ena onse a mitundu ya anthu anagona pansi mu ulemerero, aliyense m’manda ake.+ 19  Koma iweyo watayidwa popanda kuikidwa m’manda, ngati mphukira yonyansa imene ili pakati pa anthu akufa ophedwa ndi lupanga, amene akutsikira kumiyala ya m’dzenje.+ Watayidwa ngati mtembo wopondedwapondedwa. 20  Sudzakhalira nawo limodzi m’manda, chifukwa unawononga dziko lako lomwe, ndipo unapha anthu ako omwe. Mayina a ana a anthu ochita zoipa sadzatchulidwanso mpaka kalekale.+ 21  “Anthu inu, konzekerani kupha ana ake chifukwa cha zolakwa za makolo awo, kuti asalandenso dziko lapansi n’kulidzaza ndi mizinda.”+ 22  “Ine ndidzawaukira,”+ watero Yehova wa makamu. “M’Babulo ndidzachotsamo dzina,+ anthu otsala, ana, ndi mbadwa,”+ watero Yehova. 23  “Babulo ndidzamusandutsa malo okhala nungu* ndiponso malo a zithaphwi. Ndidzamusesa ndi tsache* la chiwonongeko,”+ watero Yehova wa makamu. 24  Yehova wa makamu walumbira+ kuti: “Ndithu zimene ndaganiza zidzachitika, ndipo zimene ndakonza sizidzalephereka.+ 25  Ndidzathyola Msuri amene ali m’dziko langa+ ndipo ndidzamupondaponda pamapiri anga. Goli lake lidzachoka pa iwo ndipo katundu wake adzachoka pamapewa awo.”+ 26  Izi ndi zimene ndatsimikiza kuchitira dziko lonse lapansi, ndipo ili ndi dzanja limene latambasuka kuti likanthe mitundu yonse ya anthu. 27  Pakuti Yehova wa makamu wagamula,+ ndani angazilepheretse?+ Dzanja lake n’limene latambasuka, ndani angalibweze? 28  M’chaka chimene Mfumu Ahazi inamwalira, uthenga wamphamvu uwu unaperekedwa: 29  “Usasangalale+ iwe Filisitiya, kapena aliyense wokhala mwa iwe chifukwa chakuti ndodo ya amene anali kukumenya yathyoka. Pakuti pamuzu wa njokayo padzaphuka njoka yapoizoni, ndipo chipatso chake chidzakhala njoka yothamanga, yaululu wamoto.+ 30  Ana oyamba kubadwa a anthu onyozeka, ndithu adzadya chakudya. Anthu osauka adzagona pansi popanda chowaopseza.+ Ndidzapha muzu wako ndi njala, ndipo amene adzatsale mwa iwe adzaphedwa.+ 31  Fuula chipata iwe! Lira mokweza mzinda iwe! Nonsenu mudzataya mtima, inu anthu okhala m’Filisitiya! Pakuti utsi ukubwera kuchokera kumpoto, ndipo palibe msilikali amene akutsalira pa magulu ake ankhondo.”+ 32  Kodi munthu adzawayankha chiyani amithenga a mitundu ya anthu? Adzawayankha kuti, Yehova waika maziko a Ziyoni,+ ndipo anthu ake osautsika adzathawira mmenemo.

Mawu a M'munsi

“Nungu” ndi nyama yam’tchire yomwe ili ndi minga zodzitetezera thupi lonse.
Ena amati “chipserero.”