Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 12:1-6

12  M’tsiku limenelo+ ndithu udzanena kuti: “Ndikukuthokozani inu Yehova pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu unabwerera pang’onopang’ono+ ndipo munanditonthoza.+  Taonani! Mulungu ndiye chipulumutso changa.+ Ndidzamukhulupirira ndipo sindidzaopa chilichonse,+ pakuti Ya* Yehova ndiye mphamvu zanga+ ndi nyonga zanga,+ ndipo iye wakhala chipulumutso changa.”+  Anthu inu ndithu mudzatunga madzi mosangalala pa akasupe a chipulumutso.+  M’tsiku limenelo mudzanenadi kuti: “Yamikani Yehova anthu inu.+ Itanani pa dzina lake.+ Dziwitsani mitundu ya anthu zochita zake.+ Nenani kuti dzina lake n’lokwezeka.+  Muimbireni nyimbo Yehova+ chifukwa wachita zopambana.+ Zimenezi zikulengezedwa m’dziko lonse lapansi.  “Fuula mwachisangalalo iwe mkazi wokhala mu Ziyoni, pakuti Woyera wa Isiraeli ndi wamkulu pakati pako.”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 15:2.