Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 11:1-16

11  Nthambi+ idzatuluka pachitsa cha Jese,+ ndipo mphukira+ yotuluka pamizu yake idzakhala yobereka zipatso.+  Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye,+ mzimu wanzeru,+ womvetsa zinthu,+ wolangiza, wamphamvu,+ wodziwa zinthu+ ndi woopa Yehova.+  Iye adzasangalala ndi kuopa Yehova.+ Sadzaweruza potengera zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengera zimene wangomva ndi makutu ake.+  Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka+ ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi. Adzakwapula dziko lapansi ndi ndodo ya pakamwa pake,+ ndipo adzagwiritsa ntchito mzimu wa pakamwa pake kupha munthu woipa.+  Chilungamo ndi kukhulupirika zidzakhala lamba wa m’chiuno mwake.+  Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa wamphongo kwa kanthawi,+ ndipo kambuku* adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi. Mwana wa ng’ombe, mkango wamphamvu+ ndi nyama yodyetsedwa bwino zidzakhala pamodzi,+ ndipo kamnyamata kakang’ono kadzakhala mtsogoleri wawo.  Ng’ombe ndi chimbalangondo zidzadyera pamodzi. Ana awo adzagona pansi pamodzi. Ngakhale mkango udzadya udzu ngati ng’ombe yamphongo.+  Mwana woyamwa adzasewera pa una wa mamba,+ ndipo mwana woleka kuyamwa adzapisa dzanja lake kudzenje la njoka yapoizoni.  Sizidzavulazana+ kapena kuwonongana m’phiri langa lonse loyera,+ chifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.+ 10  M’tsiku limenelo,+ padzakhala muzu wa Jese+ womwe udzaimirire ngati chizindikiro kwa anthu.+ Ngakhale anthu a mitundu ina adzatembenukira kwa iye kuti awatsogolere,+ ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.+ 11  M’tsiku limenelo, Yehova adzaperekanso dzanja lake kachiwiri+ kuti atenge anthu ake otsala kuchokera ku Asuri,+ ku Iguputo,+ ku Patirosi,+ ku Kusi,+ ku Elamu,+ ku Sinara,+ ku Hamati ndi m’zilumba za m’nyanja.+ 12  Iye adzakwezera chizindikiro mitundu ya anthu n’kusonkhanitsa Aisiraeli omwe anamwazikana.+ Ndipo adzasonkhanitsa pamodzi Ayuda omwe anabalalika, kuchokera kumalekezero anayi a dziko lapansi.+ 13  Nsanje ya Efuraimu idzatha,+ ndipo ngakhale anthu odana ndi Yuda adzaphedwa. Efuraimu sadzachitira nsanje Yuda ndiponso Yuda sadzadana ndi Efuraimu.+ 14  Iwo adzauluka paphewa la Afilisiti kumadzulo,+ ndipo onsewa pamodzi, adzalanda katundu wa ana aamuna a Kum’mawa.+ Adzatambasulira dzanja lawo pa Edomu ndi Mowabu,+ ndipo ana a Amoni adzawagonjera.+ 15  Yehova adzaphwetsa chigawo cha nyanja ya Iguputo,+ ndipo adzayendetsa dzanja lake moopseza Mtsinje*+ pogwiritsa ntchito mpweya wake wotentha. Adzamenya mtsinjewo pokwapula timitsinje take 7, ndipo adzachititsa anthu kuwolokapo nsapato zili kuphazi.+ 16  Padzakhala msewu waukulu+ wochokera kudziko la Asuri woti mudzadutse anthu ake amene adzatsale,+ monga mmene panalili msewu umodzi umene Aisiraeli anayendamo m’tsiku limene anatuluka m’dziko la Iguputo.

Mawu a M'munsi

Ena amati “nyalugwe.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.