Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yesaya 1:1-31

1  Masomphenya amene Yesaya mwana wa Amozi anaona, okhudza Yuda ndi Yerusalemu m’masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a Yuda:+  Imvani+ kumwamba inu, ndipo tchera khutu iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena kuti: “Ndalera ana ndi kuwakulitsa, koma iwo andipandukira.  Ng’ombe yamphongo imam’dziwa bwino munthu amene anaigula, ndipo bulu amadziwa chinthu chimene mbuye wake amam’dyetseramo. Koma Isiraeli sandidziwa,+ ndipo anthu anga sanachite zinthu mozindikira.”  Tsoka kwa mtundu wochimwa,+ anthu olemedwa ndi zolakwa, mbewu yochita zoipa, ana obweretsa chiwonongeko.+ Iwo amusiya Yehova. Achitira Woyera wa Isiraeli zinthu zopanda ulemu, ndipo abwerera m’mbuyo.+  Kodi mumenyedwanso pati+ mmene mukupitiriza kupandukamu?+ Mutu wanu uli ndi zilonda zokhazokha, ndipo mtima wanu wafooka.  Kuyambira kuphazi mpaka kumutu palibe pabwino.+ Thupi lanu lonse lili ndi mabala ndi zilonda, ndiponso lanyukanyuka. Palibe amene wafinya zilonda zanuzo kapena kuzimanga. Palibenso amene wazifewetsa ndi mafuta.+  Dziko lanu lawonongedwa.+ Mizinda yanu yatenthedwa ndi moto,+ ndipo alendo akudya zokolola zochokera munthaka yanu, inu mukuona. Chilichonse chawonongeka ngati mmene zimakhalira adani akalanda dziko.  Mwana wamkazi wa Ziyoni+ wasiyidwa ngati msasa m’munda wa mpesa, ngati chisimba* m’munda wa minkhaka, ndiponso ngati mzinda umene wazunguliridwa ndi adani.  Yehova wa makamu akanapanda kutisiyira anthu ochepa opulumuka, tikanakhala ngati Sodomu, ndipo tikanafanana ndi Gomora. 10  Imvani mawu a Yehova,+ inu olamulira ankhanza+ a ku Sodomu. Mvetserani malamulo a Mulungu wathu, inu anthu a ku Gomora. 11  Yehova wanena kuti: “Kodi nsembe zanu zambirimbirizo zili ndi phindu lanji kwa ine? Nsembe zopsereza zathunthu+ za nkhosa zamphongo ndiponso mafuta a nyama zodyetsedwa bwino zandikwana. Ine sindikusangalalanso ndi magazi a ana a ng’ombe amphongo, ana a nkhosa amphongo ndiponso a mbuzi zamphongo.+ 12  Inu mukamabwerabwera kuti mudzaone nkhope yanga, kodi ndani wakuuzani kuti muchite zimenezi, kuti muzipondaponda mabwalo a panyumba panga?+ 13  Musabweretsenso nsembe zina zaufa zopanda phindu.+ Zofukiza zanu ndikunyansidwa nazo.+ Mumasunga masiku okhala mwezi ndi sabata, ndipo mumaitanitsa misonkhano. Koma ine ndatopa kukuonani mukugwiritsira ntchito mphamvu zamatsenga pamene mukuchita misonkhano yapadera. 14  Moyo wanga ukudana ndi masiku anu okhala mwezi ndi zikondwerero zanu.+ Zimenezi zasanduka katundu wolemera kwa ine,+ ndipo ndatopa kuzinyamula.+ 15  Mukatambasula manja anu, ndimakubisirani maso anga.+ Ngakhale mupereke mapemphero ambiri,+ ine sindimvetsera.+ Manja anu adzaza magazi amene mwakhetsa.+ 16  Sambani,+ dziyeretseni.+ Chotsani zochita zanu zoipa pamaso panga.+ Lekani kuchita zoipa.+ 17  Phunzirani kuchita zabwino.+ Funafunani chilungamo.+ Dzudzulani munthu wopondereza ena.+ Weruzani mwachilungamo mwana wamasiye.*+ Thandizani mkazi wamasiye pa mlandu wake.” 18  Yehova akuti, “Bwerani tsopano anthu inu. Tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine.+ Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.+ Ngakhale atakhala ofiira ngati magazi, adzayera ngati thonje. 19  Mukakhala ndi mtima wofuna kundimvera, mudzadya zabwino za m’dziko lanu.+ 20  Koma mukakana n’kupanduka, mudzawonongedwa ndi lupanga, chifukwa pakamwa pa Yehova m’pamene panena zimenezi.” 21  Taonani! Mzinda wokhulupirika uja+ wasanduka hule.+ Unali wodzaza ndi chilungamo ndipo zachilungamo zinali kukhala mwa iye, koma tsopano muli zigawenga zopha anthu.+ 22  Siliva wako wasanduka zonyansa.*+ Mowa wako wa tirigu wasukuluka ndi madzi.+ 23  Akalonga ako ndi aliuma ndipo ndi anzawo a mbala.+ Aliyense wa iwo amakonda ziphuphu ndipo amafunafuna mphatso.+ Mwana wamasiye samuweruza mwachilungamo ndipo ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye safuna kuuweruza. 24  Choncho mawu a Ambuye woona, Yehova wa makamu, Wamphamvu wa Isiraeli,+ ndi akuti: “Eya! Ndidzibweretsera mpumulo pochotsa adani anga ndipo ndibwezera+ odana nane. 25  Ndidzakutembenuzirani dzanja langa. Ndidzasungunula zonyansa zanu zonse, ndipo ndidzachotsa nyansi zanu zonse.+ 26  Ndidzakubweretseraninso oweruza ngati pa chiyambi paja, ndi aphungu ngati poyamba paja. Pambuyo pa zimenezi mudzatchedwa Mzinda Wachilungamo ndi Mzinda Wokhulupirika.+ 27  Ziyoni adzapulumutsidwa ndi chilungamo ndipo anthu ake amene adzabwerere, adzapulumutsidwanso ndi chilungamo.+ 28  Kuwonongeka kwa opanduka ndi kwa ochimwa kudzachitikira limodzi,+ ndipo anthu omusiya Yehova adzatha. 29  Pakuti anthu adzachita manyazi ndi mitengo ikuluikulu imene inu munali kuilakalaka,+ ndipo mudzagwetsa nkhope zanu chifukwa cha minda imene mwasankha.+ 30  Pakuti mudzakhala ngati mtengo waukulu umene masamba ake akufota+ ndiponso ngati munda umene ulibe madzi. 31  Munthu wamphamvu adzakhala ngati chingwe chabwazi,+ ndipo ntchito yake idzakhala ngati kamoto kakang’ono. Zonsezi zidzayakira limodzi popanda wozizimitsa.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “khumbi,” kapena “chitala.”
Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”
Zimenezi ndi zonyansa zotsalira poyenga zitsulo.