Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 9:1-26

9  Ndikanakonda kuti m’mutu mwanga mukhale madzi ambiri ndiponso kuti maso anga akhale magwero a misozi.+ Pamenepo ndikanalira usana ndi usiku chifukwa cha anthu ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga.+  Ndikanakonda kukhala ndi malo a m’chipululu ogona anthu apaulendo.+ Pamenepo ndikanasiya anthu anga ndi kuwachokera, pakuti onsewo ndi achigololo,+ gulu la anthu ochita zachinyengo.+  Iwo amakunga lilime lawo ngati uta kuti aponye chinyengo,+ koma iwo si okhulupirika m’dzikoli. “Iwo anali kuchita zoipa motsatizanatsatizana ndipo anandinyalanyaza,”+ watero Yehova.  “Aliyense wa inu asamale ndi mnzake,+ ndipo musakhulupirire m’bale aliyense.+ Pakuti munthu aliyense amalanda malo a m’bale wake, ndipo munthu aliyense amakhala akuyendayenda kunenera mnzake miseche.  Aliyense amapusitsa mnzake+ ndipo salankhula choonadi ngakhale pang’ono. Aphunzitsa lilime lawo kulankhula chinyengo.+ Iwo adzitopetsa okha ndi kuchita zinthu zoipa.+  “Iwe wakhala pakati pa chinyengo.+ Chifukwa cha chinyengo chawo akana kundidziwa ine,”+ watero Yehova.  Choncho, Yehova wa makamu wanena kuti: “Inetu ndikuwasungunula ndipo ndiyenera kuwasanthula.+ Nanga mwana wamkazi wa anthu anga ndingamuchitirenso zotani?  Lilime lawo ndiwo muvi wophera anthu.+ Limalankhula chinyengo chokhachokha. Munthu aliyense amalankhula mwamtendere ndi mnzake, koma mumtima mwake amakonza chiwembu.”  “Kodi sindiyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” watero Yehova. “Kapena kodi sindiyenera kubwezera mtundu woterewu?+ 10  Pakuti ndidzalirira mapiri mokweza ndi modandaula+ ndipo ndidzaimba nyimbo yoimba polira, pamene ndikulirira mabusa a m’chipululu. Ndidzalirira zimenezi chifukwa adzakhala atazitentha+ moti palibe munthu amene adzadutsamo. Anthu sadzamva kulira kwa ziweto+ m’mabusamo ndipo zolengedwa zouluka m’mlengalenga ngakhalenso nyama zidzakhala zitathawamo, zitachoka.+ 11  Yerusalemu ndidzamusandutsa milu ya miyala+ ndiponso malo obisalamo mimbulu.+ Mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa mabwinja, malo opanda wokhalamo.+ 12  “Kodi wanzeru ndani kuti amvetse zimenezi, kapenanso ndani amene Yehova wamulankhula kuti anene zimenezi?+ N’chifukwa chiyani dzikoli lidzawonongedwa ndiponso kutenthedwa n’kukhala ngati chipululu chopanda munthu wodutsamo?” 13  Ndiyeno Yehova anayankha kuti: “Chifukwa chakuti iwo asiya chilamulo changa chimene ndinawapatsa kuti chizikhala pamaso pawo, komanso chifukwa chakuti iwo sanamvere mawu anga ndi kuwatsatira,+ 14  koma iwo anapitirizabe kuumitsa mitima yawo+ ndi kutsatira mafano a Baala, zinthu zimene anaphunzitsidwa ndi makolo awo.+ 15  Choncho Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndidzadyetsa anthu amenewa chitsamba chowawa,+ ndipo ndidzawamwetsa madzi apoizoni.+ 16  Ndidzawamwaza pakati pa mitundu ya anthu imene iwo kapena makolo awo sanaidziwe. Ndidzawakantha ndi lupanga kufikira nditawafafaniza.’+ 17  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Chitani zinthu mozindikira anthu inu, ndipo itanani akazi oimba nyimbo zoimba polira kuti abwere. Tumizani anthu kuti akaitane akazi odziwa kulira maliro,+ 18  kuti abwere mofulumira ndi kudzatiimbira nyimbo zoimba polira. Maso athu atuluke misozi, madzi atuluke m’maso athu owala.+ 19  Pakuti ku Ziyoni kwamveka anthu akulira mofuula kuti:+ “Tafunkhidwa!+ Tachita manyazi kwambiri! Pakuti tasiya dziko lathu ndiponso chifukwa atigwetsera nyumba zathu.” 20  Koma tamverani mawu a Yehova akazi inu, ndipo mutchere khutu ku mawu otuluka m’kamwa mwake. Kenako muphunzitse ana anu aakazi kulira maliro ndipo mkazi aliyense aphunzitse mnzake nyimbo yoimba polira. 21  Pakuti imfa yatilowera m’nyumba kudzera m’mawindo. Yalowa munsanja zathu zokhalamo kuti mumsewu musapezeke mwana aliyense ndiponso kuti anyamata asapezeke m’mabwalo a mzinda.’ 22  “Unene kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Mitembo ya anthu idzangoti mbwee panthaka ngati manyowa. Idzakhala ngati tirigu amene angomumweta kumene koma palibe munthu womusonkhanitsa pamodzi.”’”+ 23  Yehova wanena kuti: “Munthu wanzeru asadzitamande chifukwa cha nzeru zake.+ Munthu wamphamvu asadzitamande chifukwa cha mphamvu zake. Munthu wachuma asadzitamande chifukwa cha chuma chake.” 24  “Koma amene akudzitamanda adzitamande pa chifukwa chakuti, amamvetsa bwino+ njira zanga ndipo amandidziwa, kuti ine ndine Yehova,+ amene ndimasonyeza kukoma mtima kosatha, ndimapereka ziweruzo ndi kuchita chilungamo padziko lapansi. Pakuti zinthu zimenezi zimandisangalatsa,”+ watero Yehova. 25  Yehova wanena kuti, “Taona masiku akubwera ndipo ndidzaimba mlandu aliyense wodulidwa koma amene sanachite mdulidwe wa mtima wake.+ 26  Ndidzaimba mlandu Iguputo,+ Yuda,+ Edomu,+ ana aamuna a Amoni+ ndi Mowabu+ ndi onse odulira ndevu zawo zam’mbali amene amakhala m’chipululu.+ Pakuti mitundu yonse ndi yosadulidwa ndipo anthu onse a m’nyumba ya Isiraeli sanachite mdulidwe wa mitima yawo.”

Mawu a M'munsi