Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 8:1-22

8  “Pa nthawi imeneyo,” watero Yehova, “anthu adzatulutsa m’manda mafupa a mafumu a Yuda, a akalonga awo, a ansembe, a aneneri ndi a anthu amene anali mu Yerusalemu.+  Mafupawo adzawamwaza poyera ndipo dzuwa, mwezi, ndi makamu onse akumwamba zidzawala pa iwo. Zinthu zimenezi ndi zimene iwo anali kuzikonda, kuzitumikira, kuzitsatira,+ kuzipembedza, ndi kuziweramira.+ Mafupawo sadzasonkhanitsidwa pamodzi kapena kuikidwa m’manda. Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.”+  “Onse otsala a banja loipali, kulikonse kumene ndidzawabalalitsira,+ adzaona kuti ndi bwino kufa kusiyana ndi kukhala moyo,”+ watero Yehova wa makamu.  “Ukawauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Kodi iwo adzagwa osadzukanso?+ Kodi mmodzi akabwerera, winanso sangabwerere?+  N’chifukwa chiyani anthu a mu Yerusalemu ali osakhulupirika ndipo akhalabe osakhulupirika kwa nthawi yaitali chonchi? Iwo akupitiriza kuchita zachinyengo+ ndipo akana kubwerera.+  Ine ndinali tcheru+ ndipo ndinali kuwamvetsera.+ Zimene iwo anali kunena sizinali zoona. Panalibe munthu wolapa zoipa zimene anachita,+ amene ananena kuti, ‘Kodi ndachitiranji zimenezi?’ Aliyense akubwerera kunjira imene anthu ambiri akuitsatira,+ ngati hatchi imene ikuthamangira kunkhondo.  Ngakhale dokowe, mbalame youluka m’mlengalenga, imadziwa bwino nthawi yake yoikidwiratu.+ Ndipo njiwa,+ namzeze* ndi pumbwa,* iliyonse mwa mbalame zimenezi imadziwa nyengo yobwerera kumene yachokera. Koma anthu anga sakudziwa chiweruzo cha Yehova.”’+  “‘Anthu inu munganene bwanji kuti: “Ndife anzeru, ndipo tili ndi chilamulo cha Yehova”?+ Ndithudi, zolembera zachinyengo+ za alembi zagwiritsidwa ntchito mwachinyengo.  Anthu anzeru achita manyazi.+ Achita mantha ndipo adzagwidwa. Taonani! Iwo akana mawu a Yehova. Kodi ali ndi nzeru yotani tsopano?+ 10  Choncho akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena, ndipo minda yawo ndidzaipereka kwa anthu ena.+ Pakuti kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu aliyense wa iwo akupeza phindu lachinyengo.+ Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense wa iwo akuchita zachinyengo.+ 11  Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo+ kuwonongeka kwa mwana wamkazi wa anthu anga ponena kuti: “Kuli mtendere! Kuli mtendere!” pamene kulibe mtendere.+ 12  Kodi iwo anachita manyazi chifukwa anachita zinthu zonyansa?+ Iwo sanachite manyazi ngakhale pang’ono, komanso sanali kudziwa n’komwe kuchita manyazi.+ “‘Choncho iwo adzagwa pamodzi ndi anthu amene akugwa. Pa nthawi yowalanga+ adzapunthwa,’ watero Yehova.+ 13  “‘Pokolola ndidzawafafaniza,’ watero Yehova.+ ‘Mumtengo wa mpesa simudzapezeka mphesa,+ mumtengo wa mkuyu simudzapezeka nkhuyu, ndipo masamba adzafota. Zinthu zimene ndimawapatsa zidzawadutsa.’” 14  “N’chifukwa chiyani tikungokhala? Sonkhanani pamodzi, ndipo tiyeni tilowe m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ kuti tikafere kumeneko. Pakuti Yehova Mulungu wathu watiweruza kuti tife,+ ndipo akutipatsa madzi apoizoni kuti timwe+ chifukwa tachimwira Yehova. 15  Tinali kuyembekezera mtendere, koma panalibe chabwino chilichonse.+ Tinali kuyembekezera kuchiritsidwa, koma m’malomwake tinali kuona zinthu zochititsa mantha.+ 16  Mahatchi ake akumveka kupuma mwawefuwefu ali ku Dani.+ Dziko lonse layamba kugwedezeka chifukwa cha phokoso la kulira kwa mahatchi ake amphongo.+ Adani akubwera kudzawononga dziko ndi zonse zokhala mmenemo, mzinda ndi onse okhala mmenemo.” 17  “Inetu ndikutumiza njoka pakati panu, njoka zapoizoni,+ zimene simungaziimbire nyimbo kuti muziseweretse,+ ndipo zidzakulumani ndithu,” watero Yehova. 18  Ndagwidwa ndi chisoni chosatha.+ Mtima wanga wadwala. 19  Pakumveka mawu olirira thandizo a mwana wamkazi wa anthu anga ali kudziko lakutali.+ Iye akuti: “Kodi Yehova sali mu Ziyoni?+ Kapena kodi mfumu ya Yerusalemu mulibe mmenemo?”+ “N’chifukwa chiyani andikhumudwitsa ndi mafano awo ogoba, ndiponso milungu yawo yachilendo yopanda pake?”+ 20  “Nthawi yokolola yadutsa, ndipo nyengo ya chilimwe yatha. Koma ife sitinapulumutsidwe!”+ 21  Ndasweka mtima+ chifukwa cha kuwonongeka+ kwa mwana wamkazi wa anthu anga. Ndine wachisoni. Ndadabwa kwambiri.+ 22  Kodi mu Giliyadi+ mulibe mafuta a basamu? Kapena kodi mulibe wochiritsa mmenemo?+ N’chifukwa chiyani nanga mwana wamkazi wa anthu anga sakuchira?+

Mawu a M'munsi

 Mbalame imeneyi ena amati “kaluweluwe” kapena “kamembe.”
Mbalame imeneyi ena amati “nyapwere.”