Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 6:1-30

6  Bisalani, inu ana a Benjamini, thawani pakati pa Yerusalemu. Ku Tekowa+ imbani lipenga la nyanga ya nkhosa.+ Ku Beti-hakeremu+ kwezani moto wa chizindikiro, chifukwa chiwonongeko chachikulu, tsoka, lasuzumira kuchokera kumpoto.+  Ndithudi mwana wamkazi wa Ziyoni wafanana ndi mkazi wachisasati* wooneka bwino.+  Abusa ndi magulu awo a ziweto anali kubwera kwa iye. Anamanga mahema awo momuzungulira kuti amuukire.+ Aliyense wa iwo anali kudyetsa ziweto zake pamalo ake.+  Anakonzekera kumuthira nkhondo ndipo anati:+ “Nyamukani, tiyeni tipite dzuwa lili paliwombo!”+ “Tsoka ife chifukwa nthawi yatithera ndipo zithunzithunzi zikupitiriza kutalika!”  “Nyamukani, ndipo tiyeni tipite usiku kuti tikawononge nsanja zake zokhalamo anthu.”+  Pakuti Yehova wa makamu wanena kuti: “Dulani mitengo+ kuti tipangire Yerusalemu chiunda chomenyerapo nkhondo.*+ Yerusalemu ndi mzinda woyenera kuimbidwa mlandu.+ Mkati mwake muli kuponderezana kokhakokha.+  Monga mmene chitsime chimasungira madzi ake ali ozizira, Yerusalemu wasunga zoipa zake ngati zinthu zabwino. Mkati mwake mumamveka zachiwawa ndi kufunkha.+ Nthawi zonse ndimaona matenda ndi miliri mumzindawo.  Iwe Yerusalemu, mvera chilango+ kuti ndisatembenuke ndi kukufulatira chifukwa chonyansidwa nawe,+ kuti ndisakusandutse bwinja, dziko lopanda munthu aliyense wokhalamo.”+  Yehova wa makamu wanena kuti: “Mosalephera adani adzakunkha otsalira a Isiraeli ngati mmene amakunkhira mphesa.+ Kweza dzanja lako ngati munthu amene akuthyola mphesa panthambi za mtengo wa mpesa.” 10  “Kodi ndilankhule ndi ndani ndipo ndichenjeze ndani kuti amve? Taonani! Makutu awo sanawachite mdulidwe, moti sangamve.+ Taonani! Mawu a Yehova akhala onyozeka kwa iwo,+ ndipo sakukondwera nawo.+ 11  Ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova. Ndatopa ndi kukhala chete.”+ “Tsanulira mkwiyowo pa mwana amene ali mumsewu+ ndipo nthawi yomweyo uutsanulirenso pa kagulu ka anyamata okondana. Mwamuna pamodzi ndi mkazi wake, munthu wachikulire pamodzi ndi munthu wokalamba, onsewo adzagwidwa.+ 12  Nyumba zawo, minda yawo ndi akazi awo, zonse pamodzi zidzaperekedwa kwa anthu ena.+ Pakuti ine ndidzatambasula dzanja langa ndi kuwononga anthu okhala m’dzikoli,” watero Yehova.+ 13  “Pakuti aliyense wa iwo, kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu akupeza phindu lachinyengo.+ Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense wa iwo akuchita zachinyengo.+ 14  Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo+ kuwonongeka kwa anthu anga ponena kuti, ‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’ pamene kulibe mtendere.+ 15  Kodi iwo anachita manyazi chifukwa chochita zinthu zonyansazi?+ Iwo sanachite manyazi ngakhale pang’ono, komanso sadziwa n’komwe kuchita manyazi.+ Choncho iwo adzagwa pamodzi ndi anthu amene akugwa.+ Pamene ndidzakhala ndikuwaimba mlandu adzapunthwa,” watero Yehova. 16  Yehova wauza anthuwo kuti: “Imani chilili panjira anthu inu, kuti muone ndi kufunsa za njira zakale, kuti mudziwe kumene kuli njira yabwino.+ Mukaipeza muyende mmenemo+ kuti mupeze mpumulo wa miyoyo yanu.”+ Koma iwo anapitiriza kunena kuti: “Ife sitiyendamo.”+ 17  “Koma anthu inu ndinakuutsirani alonda+ ndipo ndinati, ‘Mverani kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa!’”+ Koma iwo anapitiriza kunena kuti: “Ife sitidzamvera.”+ 18  “Choncho tamverani, inu mitundu ya anthu, kuti mudziwe anthu inu, zimene zidzawachitikira. 19  Tamverani, inu okhala padziko lapansi! Ine ndikubweretsa tsoka pa anthu awa+ chifukwa cha maganizo awo,+ pakuti sanamvere mawu anga ndipo anapitirizabe kukana chilamulo changa.”+ 20  “N’chifukwa chiyani mukundibweretsera lubani* wochokera ku Sheba+ ndi mabango onunkhira ochokera kudziko lakutali? Zimenezi zili ndi ntchito yanji kwa ine? Nsembe zanu zopsereza zathunthu sizikundisangalatsa,+ ndipo nsembe zina zonse zimene mukupereka sizikundikondweretsa.”+ 21  Choncho Yehova wanena kuti: “Tsopano ndikuikira anthu awa zinthu zopunthwitsa,+ ndipo onse pamodzi, abambo ndi ana, adzapunthwa pa zinthu zimenezi, munthu aliyense limodzi ndi mnzake adzatheratu.”+ 22  Yehova wanena kuti: “Taonani! Anthu akubwera kuchokera kudziko la kumpoto. Pali mtundu wamphamvu umene udzadzutsidwa kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ 23  Iwo adzagwira uta ndi nthungo.*+ Umenewu ndi mtundu wankhanza ndipo sudzachita chisoni. Mawu awo adzamveka ngati mkokomo wa nyanja+ ndipo adzabwera pamahatchi.+ Mtunduwo wafola pokonzekera kumenya nawe nkhondo ngati mmene mwamuna wankhondo amachitira, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni.”+ 24  Ife tamva uthenga wa zimenezi. Manja athu angoti lendee!+ Tagwidwa ndi nkhawa ndipo tikumva ululu ngati wa mkazi amene akubereka.+ 25  Musatuluke kupita kunja ndipo musayende m’njira pakuti kumeneko kuli lupanga la mdani. Zochititsa mantha zili paliponse.+ 26  Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, vala chiguduli*+ ndi kuvimvinizika m’phulusa.+ Lira ngati kuti ukulira maliro a mwana wamwamuna mmodzi yekhayo. Lira mowawidwa mtima+ chifukwa wofunkha adzatiukira modzidzimutsa.+ 27  “Ndakusandutsa woyesa zitsulo pakati pa anthu anga. Ndakusandutsa wofufuza mosamala ndipo udzaonetsetsa ndi kufufuza njira zawo.+ 28  Onse ndi anthu ouma khosi kwambiri,+ oyenda uku ndi uku ngati anthu amiseche.+ Iwo ali ngati mkuwa ndi chitsulo. Onsewo ndi anthu owononga.+ 29  Zipangizo zopemerera moto+ zatenthedwa ndi moto ndipo pamoto wawo pakutuluka mtovu.+ Munthu wakhala akuyenga chitsulo mobwerezabwereza koma osaphula kanthu, ndipo zoipa sizinachotsedwemo.+ 30  Anthu adzawatcha, ‘siliva wokanidwa,’+ pakuti Yehova wawakana.”+

Mawu a M'munsi

Munthu “wachisasati” ndi munthu wopusa chifukwa chakuti anamulera momulekerera ndipo sanaphunzire ntchito kapena zinthu zina zomuthandiza pamoyo wake.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Tikati nthungo tikutanthauza mkondo waung’ono, wopepukirako.
Ena amati “saka.”