Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 50:1-46

50  Yehova ananena mawu okhudza Babulo,+ dziko la Akasidi,+ kudzera mwa mneneri Yeremiya. Iye anati:  “Nenani ndi kulengeza zimene zachitika kwa anthu a mitundu ina.+ Imikani mtengo wachizindikiro+ ndipo lengezani zimenezi. Musabise kalikonse amuna inu. Nenani kuti, ‘Babulo walandidwa.+ Beli wachititsidwa manyazi.+ Merodake wachita mantha. Mafano a Babulo achita manyazi.+ Mafano ake onyansawo* achita mantha.’  Pakuti mtundu wina wabwera kudzamuukira kuchokera kumpoto.+ Umenewu ndi mtundu umene wasandutsa dziko lake kukhala chinthu chodabwitsa, moti m’dzikoli mulibe aliyense wokhalamo.+ Anthu ndiponso ziweto zathawa.+ Zonse zapita.”+  “M’masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo+ ana a Isiraeli pamodzi ndi ana a Yuda adzabwera,”+ watero Yehova. “Iwo adzayenda akulira+ ndipo adzafunafuna Yehova Mulungu wawo.+  Iwo adzafunsira njira yopita ku Ziyoni nkhope zawo zitayang’ana kumeneko.+ Iwo adzanena kuti, ‘Bwerani, tiyeni tidziphatike kwa Yehova mwa kuchita pangano lokhalapo mpaka kalekale limene silidzaiwalika.’+  Anthu anga akhala ngati gulu la nkhosa zosakazidwa.+ Abusa awo awayendetsa uku ndi uku.+ Awayendetsa uku ndi uku m’mapiri popanda cholinga.+ Awachotsa paphiri ndi chitunda china kupita paphiri ndi chitunda china. Iwo aiwala malo awo ampumulo.+  Anthu anga adyedwa ndi aliyense wowapeza,+ ndipo adani awo anena kuti,+ ‘Sitipalamula mlandu uliwonse, chifukwa iwo achimwira Yehova,+ malo okhalamo chilungamo.+ Achimwira Yehova chiyembekezo cha makolo awo.’”+  “Thawani m’Babulo ndipo tulukani m’dziko la Akasidi.+ Mukhale ngati mbuzi zamphongo ndi nkhosa zamphongo zimene zikutsogolera gulu lonse.+  Inetu ndikuutsira Babulo mpingo wa mitundu yamphamvu ndi kubweretsa mitunduyo kuchokera kudziko la kumpoto.+ Mitunduyo idzamuukira+ ndi kulanda dziko lake.+ Mauta awo ndi ofanana ndi mauta a munthu wamphamvu amene amapha ana ndipo mautawo sabwerera osachitapo kanthu.+ 10  Dziko la Kasidi lidzatengedwa monga zofunkha.+ Onse ofunkha zinthu zake adzakhutira,”+ watero Yehova. 11  “Anthu inu munali kusangalala,+ ndipo munali kukondwera pamene munali kulanda cholowa changa.+ Munali kudumphadumpha pamsipu ngati ng’ombe yaikazi yosaberekapo+ ndipo munali kulira ngati mahatchi amphongo.+ 12  Mayi wa anthu inu wachita manyazi kwambiri.+ Mayi amene anakuberekani wakhumudwa kwambiri.+ Taonani! Iye ndi wosafunika kwenikweni pakati pa mitundu ina, wakhala ngati dera lopanda madzi ndiponso chipululu.+ 13  Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova, m’dzikomo simudzakhalanso anthu+ ndipo dziko lonselo lidzakhala bwinja.+ Aliyense wodutsa pafupi ndi Babulo adzayang’ana modabwa ndi kumuimbira mluzu chifukwa cha miliri yake yonse.+ 14  “Zungulirani Babulo ndi kumuukira kuchokera kumbali zonse,+ inu nonse odziwa kukunga uta.+ Mulaseni+ ndipo musasunge muvi uliwonse, pakuti iye wachimwira Yehova.+ 15  Mufuulireni mfuu yankhondo kuchokera kumbali zonse.+ Wagwetsa manja ake+ ndipo zipilala zake zagwa. Mipanda yake yagwetsedwa,+ pakuti Yehova akumubwezera.+ Mubwezereni, ndipo monga mmene iye anachitira, inunso muchitireni zomwezo.+ 16  Iphani munthu wofesa mbewu mu Babulo,+ ndiponso amene akugwira chikwakwa nthawi yokolola. Aliyense adzabwerera kwa anthu a mtundu wake, ndipo aliyense adzathawira kudziko lakwawo chifukwa choopa lupanga loopsa.+ 17  “Isiraeli ndi nkhosa yosochera.+ Mikango ndi imene yamuchititsa kuthawa.+ Poyamba, mfumu ya Asuri inadya Isiraeli,+ ndipo ulendo uno Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo yakukuta mafupa ake.+ 18  Choncho Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ine ndikulanga mfumu ya Babulo ndi dziko lake ngati mmene ndinalangira mfumu ya Asuri.+ 19  Isiraeli ndidzamubwezeretsa kumalo ake odyerako msipu+ moti adzadya msipu paphiri la Karimeli+ ndi ku Basana.+ Iye adzakhutira m’madera amapiri a Efuraimu+ ndi Giliyadi.’”+ 20  “M’masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo,+ cholakwa cha Isiraeli chidzafufuzidwa+ koma sichidzapezeka,” watero Yehova. “Machimo a Yuda+ adzafufuzidwa koma sadzapezeka, pakuti ine ndidzakhululukira anthu amene ndawasiya amoyo.”+ 21  “Ukirani dziko la Merataimu. Liukireni+ ndipo muukirenso anthu a ku Pekodi.+ Apululeni ndi kuwawonongeratu. Chitani zonse zimene ndakulamulani,” watero Yehova.+ 22  “Mukumveka phokoso lankhondo m’dzikomo ndi kuwonongeka kwakukulu.+ 23  Taonani! Nyundo yophwanyira mitundu+ ya anthu padziko lonse lapansi yathyoledwa ndipo yawonongeka.+ Taonani! Babulo wakhala chinthu chodabwitsa pakati pa mitundu ina.+ 24  Iwe Babulo ndinakutchera msampha ndipo wakodwa koma iwe sunadziwe.+ Unapezeka ndi kugwidwa chifukwa unali kulimbana ndi Yehova.+ 25  “Yehova watsegula nkhokwe yake ya zida ndipo akutulutsamo zida zake zodzudzulira mwamphamvu.+ Akutero chifukwa chakuti Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa,+ ali ndi ntchito yoti achite m’dziko la Akasidi.+ 26  Lowani m’dziko lake kuchokera kudera lakutali.+ Tsegulani nkhokwe zake.+ Muunjikeni pamodzi ngati mmene anthu amaunjikira milu ya tirigu+ ndipo mumuwonongeretu.+ M’dzikomo musapezeke aliyense wotsala.+ 27  Iphani ng’ombe zake zonse zazing’ono zamphongo.+ Zonse zipite kokaphedwa.+ Tsoka kwa iwo, chifukwa tsiku lawo lafika. Nthawi yoti alangidwe yafika.+ 28  “Kukumveka phokoso la anthu amene akuthawa komanso amene apulumuka m’dziko la Babulo+ kuti akanene ku Ziyoni za chilango chimene Yehova Mulungu wathu akubwezera.+ Iye akubwezera kuwonongedwa kwa kachisi wake.+ 29  “Babulo muitanireni oponya mivi ndi uta, onse okunga uta.+ Mangani misasa momuzungulira. Pasapezeke wothawa.+ Mubwezereni zimene anachita.+ Muchitireni zonse zimene iye anachita.+ Iye wachita zinthu modzikuza pamaso pa Yehova, pamaso pa Woyera wa Isiraeli.+ 30  Choncho anyamata ake adzaphedwa m’mabwalo a mizinda yake,+ ndipo tsiku limenelo amuna ake onse ankhondo adzaphedwa,”+ watero Yehova. 31  “Taona! Iwe Babulo Wodzikuza,+ ndikukuthira nkhondo,”+ watero Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa.+ “Pakuti tsiku lako lifika, nthawi imene ndiyenera kukulanga. 32  Pa tsiku limenelo Babulo Wodzikuza ameneyu adzapunthwa ndi kugwa+ ndipo sipadzapezeka wina womudzutsa.+ Mizinda imene iye amalamulira ndidzaiyatsa moto, ndipo motowo udzawononganso madera onse ozungulira mizindayo.”+ 33  Yehova wa makamu wanena kuti: “Ana a Isiraeli ndi ana a Yuda, onse akuponderezedwa. Anthu onse amene agwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina akuwakakamira+ ndipo sakuwalola kubwerera kwawo.+ 34  Wowawombola ndi wamphamvu,+ dzina lake ndi Yehova wa makamu.+ Iye sadzalephera kuwaweruzira mlandu wawo+ kuti apumitse dziko lawo+ ndiponso kusokoneza mtendere wa anthu okhala m’Babulo.”+ 35  “Lupanga lidzawononga Akasidi,”+ watero Yehova, “lidzawononganso anthu okhala m’Babulo,+ akalonga ake+ ndi anthu ake anzeru.+ 36  Lupanga lidzawononga anthu olankhula zinthu zopanda pake.+ Anthu amenewo adzachita zinthu mopanda nzeru.+ Lupanga lidzawononga anthu amphamvu a m’Babulo,+ moti adzagwidwa ndi mantha.+ 37  Lupanga lidzawononga mahatchi awo,+ magaleta awo ankhondo ndi khamu lonse la anthu a mitundu yosiyanasiyana amene ali pakati pawo+ ndipo adzakhala ngati akazi.+ Lupanga lidzawononga chuma chake+ ndipo chidzafunkhidwa. 38  Madzi ake adzawonongedwa ndipo adzauma.+ Dziko limeneli ndi la zifaniziro zogoba,+ ndipo anthu ake amachita zinthu mosaganiza chifukwa cha masomphenya awo ochititsa mantha. 39  Choncho nyama za m’madera opanda madzi, nyama zokonda kulira mokuwa ndi nthiwatiwa zidzakhala mmenemo.+ Simudzakhalanso munthu mmenemo ndipo mzindawo sudzapezekanso ku mibadwomibadwo.”+ 40  “Monga mmene Mulungu anawonongera Sodomu ndi Gomora+ pamodzi ndi midzi yake yapafupi,+ dzikolo lidzawonongedwanso moti palibe munthu amene adzakhalanso mmenemo. Mwana wa munthu sadzakhalanso mmenemo ngati mlendo,”+ watero Yehova. 41  “Taona! Mtundu wa anthu ukubwera kuchokera kumpoto. Mtundu wamphamvu+ ndi mafumu akuluakulu+ adzautsidwa kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ 42  Iwo amadziwa kuponya mivi ndi uta komanso nthungo.+ Amenewo ndi anthu ankhanza ndipo sadzakumvera chifundo.+ Phokoso lawo lili ngati phokoso la nyanja yowinduka.+ Adzakwera pamahatchi+ ndi kukuzungulira mogwirizana n’cholinga choti akuthire nkhondo, iwe mwana wamkazi wa Babulo.+ 43  “Mfumu ya Babulo yamva za iwo,+ ndipo yataya mtima ndi kulefuka.+ Ikuda nkhawa ndipo ikumva zowawa ngati mkazi amene akubereka.+ 44  “Taona! Wina adzabwera ngati mkango kuchokera m’nkhalango zowirira za m’mphepete mwa Yorodano.+ Iye adzafika pamalo otetezeka odyetsera nkhosa koma m’kanthawi kochepa ndidzathamangitsa eni malowo.+ Ndidzasankha ndi kuika woyang’anira malowo,+ pakuti ndani angafanane ndi ine,+ ndipo ndani angalimbane ndi ine,+ komanso ndi m’busa uti tsopano amene angatsutsane nane?+ 45  Tsopano amuna inu, tamverani zimene Yehova wasankha+ kuchitira Babulo+ ndiponso zimene waganiza kuti achitire dziko la Akasidi.+ Ndithudi chilombo chidzakokera ana a nkhosa uku ndi uku,+ ndipo chidzawononga malo awo okhala chifukwa cha anthuwo.+ 46  Dziko lapansi lidzagwedezeka chifukwa cha phokoso la kugwidwa kwa Babulo,+ ndipo kulira kudzamveka pakati pa mitundu ya anthu.”+

Mawu a M'munsi

Mawu amene ali m’mipukutu yoyambirira pa mawu akuti “onyansa” amatanthauza “ndowe.”