Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 5:1-31

5  Pitani mukayendeyende m’misewu ya mu Yerusalemu kuti mukaone, mukafufuze m’mabwalo ake ndi kudziwa ngati mungapezeke munthu,+ ngati muli aliyense wochita chilungamo,+ kapena aliyense wokhulupirika.+ Ngati mungamupeze munthu woteroyo, ndidzaukhululukira mzinda umenewu.  Ngakhale atalumbira kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo!” adzakhala akulumbira mwachinyengo.+  Inu Yehova, kodi maso anu sakulakalaka kuona munthu wokhulupirika?+ Mwawalanga+ koma sanamve kupweteka.+ Ngakhale kuti munatsala pang’ono kuwafafaniza onse,+ iwo sanaphunzirepo* kanthu.+ Anaumitsa nkhope zawo ngati thanthwe.+ Ndipo anakana kubwerera kwa inu.+  Ine ndinati: “Ndithudi, amenewa ndi anthu onyozeka. Anachita zinthu mopusa, pakuti anakana njira ya Yehova. Anakana chilamulo cha Mulungu wawo.+  Ndidzapita kwa akuluakulu ndi kulankhula nawo,+ pakuti mosakayikira aganizira njira ya Yehova ndi chilamulo cha Mulungu wawo.+ Ndithudi onsewo athyola goli la Mulungu ndipo mosakayikira adula zomangira za Mulungu.”+  N’chifukwa chake mkango wa m’nkhalango wawaukira, mmbulu wa m’chipululu ukupitirizabe kuwawononga+ ndipo kambuku* akukhalabe tcheru pa mizinda yawo.+ Aliyense wotuluka m’mizindayo amakhadzulidwakhadzulidwa, chifukwa zolakwa zawo zachuluka ndipo zochita zawo za kusakhulupirika zawonjezeka kwambiri.+  Kodi ndingakukhululukire bwanji zinthu zimenezi? Ana ako aamuna andisiya ndipo amalumbira+ pa zinthu zina osati Mulungu.+ Ndinali kuwapatsa zofuna zawo+ koma anapitiriza kuchita chigololo+ ndipo anali kupita kunyumba ya hule m’magulumagulu.  Iwo akhala ngati mahatchi amphongo achilakolako champhamvu chofuna kukwera, okhala ndi mavalo amphamvu. Aliyense amamemesa* mkazi wa mnzake.+  “Kodi sindiyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” watero Yehova.+ “Kapena kodi sindiyenera kubwezera mtundu wa anthu amakhalidwe oterewa?”+ 10  “Bwerani mudzaukire mizere yake ya mitengo ya mpesa ndi kuiwononga,+ koma anthu inu musaifafaniziretu.+ M’chotsereni mphukira zake zamasamba ambiri chifukwa si za Yehova.+ 11  Pakuti a m’nyumba ya Isiraeli ndi a m’nyumba ya Yuda andichitiradi zachinyengo,” watero Yehova.+ 12  “Iwo akana Yehova, ndipo akunena kuti, ‘Iye kulibe.+ Ndipo ife tsoka silidzatigwera. Sitidzaona lupanga lililonse kapena njala yaikulu.’+ 13  Aneneri nawonso akulankhula zopanda pake ndipo mwa iwo mulibe mawu a Mulungu.+ Iwo adzakhala opanda pake ngati mawu awo omwewo.” 14  Chotero Yehova, Mulungu wa makamu wanena kuti: “Pakuti iwo akunena zimenezi, ndichititsa mawu anga m’kamwa mwako kukhala ngati moto+ koma anthu awa adzakhala ngati nkhuni ndipo motowo udzawanyeketsa.”+ 15  “Tsopano anthu inu, ndikukubweretserani mtundu wa anthu akutali,+ inu a m’nyumba ya Isiraeli,” watero Yehova. “Umenewu ndi mtundu umene wakhalapo kwa nthawi yaitali,+ mtundu wakale, mtundu umene chilankhulo chawo simuchidziwa ndipo simungamve ndi kuzindikira zimene akulankhula. 16  Kachikwama kawo koikamo mivi kali ngati manda otseguka. Onse ndi amuna amphamvu.+ 17  Iwo adzadya zokolola zanu ndi mkate wanu.+ Amuna amenewo adzadya ana anu aamuna ndi ana anu aakazi. Adzadya nkhosa zanu ndi ng’ombe zanu. Adzadya mtengo wanu wa mpesa ndi mtengo wanu wa mkuyu.+ Iwo adzagwetsa ndi lupanga mizinda yanu imene mumaidalira, yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.” 18  Yehova wanena kuti: “Ngakhale masiku amenewo sindidzakufafanizani nonse anthu inu.+ 19  Ndiyeno mudzanena kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu watichitira zonsezi?’+ Pamenepo ukawayankhe kuti, ‘Popeza mwandisiya ine Mulungu wanu ndipo mwapita kukatumikira mulungu wachilendo m’dziko lanu, mudzatumikiranso alendo m’dziko limene si lanu.’”+ 20  Mukanene izi m’nyumba ya Yakobo ndi kuzilengeza mu Yuda kuti: 21  “Tsopano tamverani izi anthu opusa inu, anthu opanda nzeru mumtima mwanu,+ amene muli ndi maso koma simukuona,+ muli ndi makutu koma simukumva.+ 22  ‘Kodi simundiopa?’+ watero Yehova. ‘Kapena kodi simukumva ululu waukulu chifukwa cha ine?+ Ine ndinaika mchenga kukhala malire a nyanja, malire okhalapo mpaka kalekale amene nyanjayo singadutse. Ngakhale kuti mafunde amawinduka sangadutse malirewo ndipo ngakhale amachita phokoso sangawapitirire.+ 23  Koma anthu awa ali ndi mtima wouma ndi wopanduka. Achoka panjira yanga ndipo akuyenda m’njira yawo.+ 24  Mumtima mwawo sananene kuti: “Tsopano tiyeni tiope Yehova Mulungu wathu,+ amene amatigwetsera mvula. Amatigwetsera mvula yoyamba ndi yomalizira pa nyengo yake,+ ndipo amaonetsetsa kuti tili ndi milungu yoikidwiratu imene timakolola.”+ 25  Zolakwa zanu ndi zimene zachititsa kuti zinthu zimenezi zithe ndipo machimo anu akutsekerezerani zabwino.+ 26  “‘Zili choncho, chifukwa pakati pa anthu anga papezeka anthu oipa.+ Iwo amawabisalira ndi kuwayang’anitsitsa ngati mmene wosaka mbalame amachitira.+ Awatchera msampha wowononga pakuti iwo amagwira anthu. 27  Nyumba zawo zadzaza chinyengo+ ngati mmene mbalame zimadzazira m’chikwere.* N’chifukwa chake iwo alemera ndipo apeza chuma chambiri.+ 28  Iwo anenepa+ ndipo matupi awo asalala. Achitanso zinthu zoipa zosawerengeka. Iwo sanaweruze mlandu wa munthu aliyense mwachilungamo,+ ngakhale mlandu wa mwana wamasiye,*+ pofuna kuti zinthu ziwayendere bwino.+ Iwo sanachitire chilungamo munthu wosauka.’” 29  “Kodi sindiyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” watero Yehova. “Kapena kodi sindiyenera kubwezera mtundu wa anthu amakhalidwe oterewa?+ 30  Chinthu chodabwitsa, chinthu choopsa, chafika m’dziko:+ 31  Aneneri akulosera monama,+ ndipo ansembe akupondereza anthu ndi mphamvu zawo.+ Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.+ Ndipo kodi anthu inu mudzachita chiyani pamapeto pake?”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.
Ena amati “nyalugwe.”
Mawu akuti “kumemesa” amatanthauza zimene nyama yamphongo imachita ikafuna kukwera.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”