Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 49:1-39

49  Ponena za ana a Amoni Yehova wanena kuti: “Kodi Isiraeli alibe ana aamuna, kapena kodi alibe wolandira cholowa? N’chifukwa chiyani Malikamu watenga Gadi+ kukhala cholowa chake? N’chifukwa chiyani anthu olambira Malikamu akukhala m’mizinda ya Isiraeli?”+  “‘Choncho taonani! Masiku adzafika,’ watero Yehova, ‘ndipo Raba, umene ndi mzinda wa ana a Amoni, ndidzaulizira chizindikiro chakuti kukubwera nkhondo.+ Ndipo mzindawu udzasanduka bwinja ndi mulu wadothi.+ Midzi yake yozungulira idzatenthedwa.’+ “‘Isiraeli adzatenga dziko la anthu amene analanda dziko lake,’+ watero Yehova.  “‘Fuula+ iwe Hesiboni+ pakuti mzinda wa Ai wafunkhidwa zinthu zake! Lirani inu midzi yozungulira Raba. Valani ziguduli.+ Lirani mokuwa ndi kuyendayenda m’makola amiyala chifukwa Malikamu adzatengedwa kupita ku ukapolo pamodzi ndi ansembe ndi akalonga ake onse.+  Bwanji umadzitama chifukwa cha zigwa zako, zigwa zoyenda madzi,+ iwe mwana wamkazi wosakhulupirika? Iwe ukudalira chuma chako,+ ponena kuti: “Ndani angabwere kwa ine?”’”+  “Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa+ wanena kuti, ‘Ine ndikukubweretsera chinthu chochititsa mantha+ kuchokera kwa anthu onse okuzungulira. Ndiponso anthu inu mudzabalalitsidwa, aliyense kulowera kwake,+ ndipo sipadzapezeka wosonkhanitsa pamodzi anthu othawawo.’”  “‘Pambuyo pake ndidzasonkhanitsa ana a Amoni+ amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,’ watero Yehova.”  Ponena za Edomu, Yehova wa makamu wanena kuti: “Kodi nzeru+ zinatha ku Temani? Kodi anthu ozindikira sakuperekanso malangizo anzeru? Kodi nzeru zawo zavunda?+  Thawani!+ Bwererani! Pitani kumalo otsika kuti mukakhale kumeneko, inu okhala ku Dedani!+ Pakuti Esau ndidzamugwetsera tsoka pa nthawi yomulanga.+  Kodi okolola mphesa atabwera kwa iwe sadzasiyako zina zoti ena akunkhe? Ndipotu akuba atakubwerera usiku, adzangowononga zokhazo zimene akufuna.+ 10  Koma ine ndidzawononga zinthu zonse za Esau ndi kumusiya alibiretu kalikonse.+ Ndidzavundukula malo ake obisika+ moti munthu sadzatha kubisala.+ Mbadwa zake, abale ake ndi anthu oyandikana naye adzafunkhidwa,+ ndipo Esau sadzakhalaponso.+ 11  Asiyeni ana anu amasiye.*+ Ine ndidzawasiya amoyo ndipo akazi anu amasiye adzandikhulupirira.”+ 12  Yehova wanena kuti: “Taonani! Ngakhale kuti sanazolowere kumwa za m’kapu, iwo adzamwa ndithu.+ Kodi iwe udzasiyidwa osapatsidwa chilango? Ayi, sudzasiyidwa osapatsidwa chilango pakuti udzamwa ndithu za m’kapumo.”+ 13  “Ine ndalumbira pa dzina langa kuti Bozira adzakhala chinthu chodabwitsa, chotonzedwa ndiponso malo owonongedwa.+ Iye adzakhala wotembereredwa ndipo mizinda yake yonse idzakhala mabwinja mpaka kalekale,”+ watero Yehova. 14  Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova ndipo nthumwi yatumidwa kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti: “Sonkhanani, muukireni ndi kumuthira nkhondo.”+ 15  “Taona! Ndakuchepetsa pakati pa mitundu ina, ndipo ndakupeputsa pakati pa anthu.+ 16  Iwe unachititsa anthu kunjenjemera ndiponso unali ndi mtima wodzikuza,+ koma zimenezi zakunyenga, iwe amene ukukhala m’malo obisika a m’thanthwe pamwamba pa phiri. Ngakhale kuti umamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga+ ndidzakugwetsa kuchoka pamenepo,”+ watero Yehova. 17  “Edomu adzakhala chinthu chodabwitsa.+ Aliyense wodutsa pafupi naye adzamuyang’anitsitsa modabwa ndi kumuimbira mluzu chifukwa cha miliri yonse imene idzamugwera. 18  Monga mmene Sodomu ndi Gomora pamodzi ndi midzi yapafupi inawonongedwera, Edomu adzawonongedwanso moti palibe munthu amene adzakhalanso m’dzikolo. Mwana wa munthu sadzakhalanso mmenemo ngati mlendo,”+ watero Yehova. 19  “Taona! Wina adzabwera ngati mkango+ kuchokera m’nkhalango zowirira za m’mphepete mwa Yorodano. Iye adzafika pamalo otetezeka+ odyetsera nkhosa koma m’kanthawi kochepa ndidzamuthamangitsa pamalowo.+ Ndidzasankha ndi kuika woyang’anira malowo, pakuti ndani angafanane ndi ine, ndipo ndani angalimbane ndi ine,+ komanso ndi m’busa uti tsopano amene angatsutsane nane?+ 20  Tsopano amuna inu, tamverani zimene Yehova wasankha kuchitira Edomu+ ndiponso zimene waganiza kuti achitire anthu okhala ku Temani:+ Ndithudi, chilombo chidzakokera ana a nkhosa uku ndi uku, ndipo chidzawononga malo awo okhala chifukwa cha anthuwo.+ 21  Dziko lapansi layamba kugwedezeka chifukwa cha mkokomo wa kugwa kwawo.+ Kukumveka kulira!+ Kulirako kwamveka mpaka ku Nyanja Yofiira. 22  Taonani! Wina adzakwera kenako n’kutsika ngati chiwombankhanga chimene chikufuna kugwira chakudya chake.+ Adzatambasulira mapiko ake pa Bozira,+ ndipo pa tsikulo mtima wa amuna amphamvu a ku Edomu udzakhala ngati mtima wa mkazi amene akumva zowawa za pobereka.”+ 23  Uthenga wokhudza Damasiko+ ndi wonena kuti: “Hamati ndi Aripadi achita manyazi chifukwa chakuti amva uthenga woipa. Iwo apasuka ndipo nyanja yawinduka, moti singathe kukhala bata.+ 24  Damasiko wachita mantha. Watembenuka ndi kuthawa ndipo wapanikizika.+ Iye wagwidwa ndi nkhawa ndiponso zowawa za pobereka ngati zimene zimagwira mkazi amene akubereka.+ 25  Kodi zatheka bwanji kuti anthu asachoke mumzinda wotamandika, mudzi wobweretsa chisangalalo?+ 26  “Choncho anyamata ake adzaphedwa m’mabwalo ake, ndipo amuna ake ankhondo adzawakhalitsa chete pa tsiku limenelo,”+ watero Yehova wa makamu. 27  “Mipanda ya Damasiko ndidzaiyatsa moto, ndipo motowo udzatentha nsanja zokhalamo za Beni-hadadi.” 28  Ponena za Kedara ndi maufumu a Hazori+ amene Nebukadirezara mfumu ya Babulo anawapha,+ Yehova wanena kuti: “Nyamukani amuna inu, pitani ku Kedara ndipo mukafunkhe zinthu za ana a Kum’mawa. 29  Mahema awo,+ nkhosa zawo,+ nsalu za mahema awo ndi zinthu zawo zonse zidzatengedwa.+ Ngamila zawo zidzalandidwa. Anthu adzawalirira kuti, ‘Zochititsa mantha zili paliponse!’”+ 30  “Thawani, thawirani kutali. Tsikirani kumalo akuya kuti mukakhale kumeneko, inu okhala ku Hazori,”+ watero Yehova. “Pakuti Nebukadirezara mfumu ya Babulo+ waganiza zokuukirani ndi kukuchitirani zoipa.” 31  “Nyamukani, amuna inu. Pitani kukaukira mtundu wa anthu umene ukukhala mosatekeseka+ ndi mwamtendere!”+ watero Yehova. “Kumeneko kulibe zitseko ndi mipiringidzo. Anthu ake amakhala kwaokhaokha. 32  Ngamila zawo zidzafunkhidwa ndipo ziweto zawo zochulukazo zidzawonongedwa. Anthu amene amadulira ndevu zawo za m’mbali ndidzawabalalitsira kumbali zonse.*+ Ndidzawagwetsera tsoka kuchokera kumadera onse owazungulira,” watero Yehova. 33  “Hazori+ adzakhala malo obisalamo mimbulu+ ndipo adzakhala bwinja mpaka kalekale. Palibe munthu amene adzakhala kumeneko, moti mwana wa munthu sadzakhalanso mmenemo ngati mlendo.”+ 34  Yehova anauza Yeremiya mawu okhudza Elamu kuchiyambi kwa ufumu wa Zedekiya mfumu ya Yuda, kuti: 35  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ine ndikuthyola uta wa Aelamu,+ umene ndiwo mphamvu yawo yaikulu. 36  Anthu a ku Elamu ndidzawabweretsera mphepo zinayi kuchokera kumalekezero anayi a kumwamba.+ Ndidzawabalalitsira kumphepo zonsezi+ ndipo sipadzapezeka mtundu wa anthu kumene obalalitsidwa+ a Elamu sadzapitako.’” 37  “Aelamu ndidzawachititsa mantha pamaso pa adani awo ndi pamaso pa anthu amene akufunafuna moyo wawo. Ndidzawabweretsera tsoka, mkwiyo wanga woyaka moto,”+ watero Yehova. “Ndidzawatumizira lupanga kufikira nditawafafaniza.”+ 38  “Ndidzaika mpando wanga wachifumu ku Elamu,+ ndipo kumeneko ndidzawononga ndi kuchotsa mfumu ndi akalonga,” watero Yehova. 39  “Ndiyeno m’masiku otsiriza+ ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu a ku Elamu amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,”+ watero Yehova.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ana anu aamuna opanda abambo.”
Mawu ake enieni, “kumphepo zonse,” kutanthauza kumbali zonse kumene mphepo imapita.