Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 46:1-28

46  Yehova anauza mneneri Yeremiya uthenga wokhudza mitundu ya anthu.+  Uthenga umenewu unali wopita ku Iguputo+ ndipo unali kukhudza gulu lankhondo la Farao Neko, mfumu ya Iguputo, amene anali kumtsinje wa Firate ku Karikemisi.+ Nebukadirezara mfumu ya Babulo anagonjetsa mfumu imeneyi m’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda. Uthengawo unali wakuti:  “Amuna inu, tengani zishango zanu zazikulu ndi zazing’ono ndipo konzekerani kumenya nkhondo.+  Inu asilikali okwera pamahatchi, mangani mahatchi anu ndi kukwerapo, ndipo muvale zisoti zanu ndi kukhala okonzeka. Pukutani mikondo yanu ing’onoing’ono. Valani zovala zanu zamamba achitsulo.  “‘N’chifukwa chiyani akuoneka kuti agwidwa ndi mantha? Akubwerera, ndipo amuna awo amphamvu aphwanyika ndi kukhala zidutswazidutswa. Iwo athawadi ndipo sanacheuke. Zochititsa mantha zili paliponse,’+ watero Yehova.  ‘Munthu waliwiro ndi munthu wamphamvu asayese dala kuthawa.+ Iwo apunthwa ndi kugwa. Zimenezi zachitikira kumpoto+ m’mphepete mwa mtsinje wa Firate.’  “Ndani uyu amene akubwera ngati mtsinje wa Nailo, kapena ngati mitsinje ya madzi ambiri amene akuwinduka?+  Dziko la Iguputo likubwera ngati mtsinje wa Nailo,+ ndipo likubwera ngati madzi owinduka a m’mitsinje.+ Dzikolo likunena kuti, ‘Ndipita ndipo ndiphimba dziko lapansi. Ndiwononga mzinda ndi onse okhala mumzindawo.’  Inu mahatchi pitani. Inu magaleta thamangani ndi liwiro lalikulu! Lolani amuna amphamvu kuti apite. Lolani Kusi ndi Puti+ amene amadziwa kugwiritsira ntchito chishango kuti apite. Lolaninso Aludi amene amadziwa kukunga ndi kuponya uta kuti apite. 10  “Limeneli ndi tsiku la Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa ndipo ndi tsiku lobwezera chilango kwa adani ake.+ Lupanga lidzadya adaniwo ndi kukhuta ndipo lidzamwa magazi awo kufikira litathetsa ludzu lake. Lidzatero pakuti Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa,+ ali ndi nsembe imene akufuna kupereka m’dziko la kumpoto, m’mphepete mwa mtsinje wa Firate. 11  “Iwe namwali, mwana wamkazi wa Iguputo,+ pita ku Giliyadi kuti ukatenge mafuta a basamu. Wachulukitsa njira zochiritsira zosathandiza koma sudzachiritsidwa.+ 12  Mitundu ya anthu yamva zochititsa manyazi zimene zakuchitikira+ ndipo kulira kwako kwamveka m’dziko lonse.+ Amuna amphamvu apunthwitsana ndi kugwetsana.+ Onse agwera limodzi.” 13  Yehova anauza mneneri Yeremiya mawu okhudza kubwera kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo kudzaukira dziko la Iguputo.+ Iye anati: 14  “Nenani zimenezi mu Iguputo amuna inu. Lengezani zimenezi ku Migidoli,+ ku Nofi+ ndi ku Tahapanesi.+ Nenani kuti, ‘Imani chilili. Konzekani.+ Pakuti lupanga lidzawononga chilichonse chokuzungulirani.+ 15  N’chifukwa chiyani anthu anu amphamvu akokoloka? Iwo sanachirimike pakuti Yehova wawathamangitsa.+ 16  Ambiri mwa iwo akupunthwa ndi kugwa. Ndipo akuuzana kuti: “Imirira, tiye tibwerere kwa anthu a mtundu wathu ndi kudziko la abale athu chifukwa takumana ndi lupanga loopsa.”’ 17  Kumeneko asilikali anu akunena kuti, ‘Farao mfumu ya Iguputo akungoopseza ndi pakamwa chabe. Iye wathetsa nthawi ya chikondwerero.’+ 18  “‘Pali ine Mulungu wamoyo, Nebukadirezara adzabwera ndi kuonekera ngati phiri la Tabori pakati pa mapiri ena, ndiponso ngati phiri la Karimeli m’mphepete mwa nyanja,’ yatero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova wa makamu.+ 19  ‘Longedza katundu wopita naye ku ukapolo,+ iwe mwana wamkazi wokhala+ mu Iguputo. Pakuti mzinda wa Nofi+ udzakhala chinthu chodabwitsa ndipo adzautentha, moti simudzapezeka aliyense wokhalamo.+ 20  Iguputo ndi ng’ombe yaikazi yokongola kwambiri imene sinaberekepo. Udzudzu wovutitsa ndi wowononga wochokera kumpoto udzabwera kuti umuwononge.+ 21  Kuwonjezera apo, asilikali amene wawalemba ganyu ali ngati ana a ng’ombe onenepa,+ koma iwonso agonja+ ndipo onse athawa. Sanathe kulimba+ pakuti tsiku lawo la tsoka ndiponso nthawi ya kulangidwa kwawo yafika.’+ 22  “‘Mawu ake ali ngati mawu a njoka imene ikuthawa.+ Pakuti adani adzafika mwamphamvu ndipo adzabwera kwa iye ali ndi nkhwangwa ngati anthu otola nkhuni.* 23  Adaniwo ndi ochuluka kwambiri kuposa dzombe ndipo ndi osawerengeka, moti adzadula nkhalango+ yake chifukwa sangathe kudutsamo,’ watero Yehova. 24  ‘Mwana wamkazi+ wa Iguputo adzachitadi manyazi, ndipo adzaperekedwa m’manja mwa anthu a kumpoto.’+ 25  “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndilanga Amoni+ wa ku No,+ Farao, Iguputo pamodzi ndi milungu yake ndi mafumu ake. Ndilanga Farao ndi onse amene amamukhulupirira.’+ 26  “‘Ndidzapereka anthu a ku Iguputo m’manja mwa anthu amene akufuna moyo wawo, m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo+ ndi m’manja mwa atumiki ake. Kenako anthu adzakhalanso m’dzikolo monga mmene zinalili kale,’+ watero Yehova. 27  “‘Koma iwe Yakobo mtumiki wanga, usaope ndipo usagwidwe ndi mantha, iwe Isiraeli.+ Pakuti ine tsopano ndikukupulumutsa kuchokera kutali. Mbewu yako ndikuipulumutsa kuchokera m’dziko limene iwo anali akapolo.+ Yakobo adzabwerera ndi kukhala mwabata ndiponso mosatekeseka, popanda womuopsa.+ 28  Chotero, iwe Yakobo mtumiki wanga usachite mantha, pakuti ine ndili ndi iwe.+ Ine ndidzafafaniza mitundu yonse ya anthu kumene ndakubalalitsirako,+ koma iwe sindidzakufafaniza.+ Ngakhale zili choncho, ndidzakulanga pamlingo woyenera,+ ndipo ndithu sindidzakusiya osakulanga,’+ watero Yehova.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “odula nkhuni.”