Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 43:1-13

43  Ndiyeno Yeremiya atamaliza kuuza anthu onse mawu onse a Yehova Mulungu wawo, amene Yehova Mulungu anatuma Yeremiya kukawauza,+  Azariya mwana wa Hoshaya,+ Yohanani+ mwana wa Kareya ndi anthu enanso odzikuza+ anauza Yeremiya kuti: “Ukunena zabodza. Yehova Mulungu wathu sanakutume kudzatiuza+ kuti, ‘Musapite ku Iguputo kuti mukakhale kumeneko monga alendo.’+  Koma Baruki+ mwana wa Neriya ndiye akukulimbikitsa kunena zinthu zofuna kutipweteketsa ndi cholinga chotipereka m’manja mwa Akasidi kuti atiphe kapena kutitenga kupita ku ukapolo ku Babulo.”+  Chotero Yohanani mwana wa Kareya, akuluakulu onse a magulu ankhondo ndi anthu onse sanamvere mawu a Yehova+ kuti apitirize kukhala m’dziko la Yuda,+  moti Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a magulu ankhondo anatenga otsala a Yuda amene anabwerera kuchokera ku mitundu yonse ya anthu kumene anathawira kuti akhale m’dziko la Yuda kwa kanthawi kochepa.+  Anatenga amuna amphamvu, akazi awo, ana aang’ono, ana aakazi a mfumu+ ndiponso aliyense amene Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu analola kuti akhale ndi Gedaliya+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani.+ Anatenganso mneneri Yeremiya ndi Baruki+ mwana wa Neriya.  Pamapeto pake anafika ku Iguputo+ chifukwa sanamvere mawu a Yehova ndipo patapita nthawi anakafika ku Tahapanesi.+  Tsopano pamene Yeremiya anali ku Tahapanesi, Yehova anamuuza kuti:  “Tenga miyala ikuluikulu ndipo ukaibise m’dothi limene anamangira chiunda cha njerwa chimene chili pakhomo la nyumba ya Farao ku Tahapanesi. Ukachite zimenezi amuna onse achiyuda akuona.+ 10  Kenako ukawauze kuti, ‘Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Inetu ndikuitana Nebukadirezara mfumu ya Babulo+ mtumiki wanga,+ ndipo ndidzaika mpando wake wachifumu pamwamba penipeni pa miyala iyi imene ndaibisa. Iye adzamanga hema wake waulemerero pamwamba pa miyala imeneyi. 11  Nebukadirezara adzabwera kudzathira nkhondo dziko la Iguputo.+ Woyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri. Woyenera kutengedwa kupita ku ukapolo adzatengedwa kupita ku ukapolo. Woyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga.+ 12  Nyumba za milungu ya Iguputo ndidzaziyatsa moto.+ Nebukadirezara adzatentha milunguyo ndi kuitenga kupita nayo kudziko lina. Monga mmene m’busa savutikira kuvala chovala chake,+ Nebukadirezara sadzavutika kugonjetsa dziko la Iguputo ndi kuchokako atapambana. 13  Iye adzaphwanyaphwanya zipilala za ku Beti-semesi,* mzinda umene uli ku Iguputo. Ndipo nyumba za milungu ya Iguputo adzazitentha.”’”

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Nyumba ya Dzuwa.”