Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 4:1-31

4  Yehova wanena kuti: “Ngati ungabwerere, iwe Isiraeli, ubwerere kwa ine.+ Ndipo ngati ungachotse zinthu zako zonyansazo chifukwa cha ine,+ sudzakhalanso wothawathawa.  Ndipo ngati udzalumbira+ kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo, Mulungu wachoonadi+ ndi chilungamo,’+ pamenepo mitundu ya anthu idzapeza madalitso* kudzera mwa iye ndipo idzadzitama m’dzina lake.”+  Zimene Yehova wanena kwa anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu ndi izi: “Limani minda panthaka yabwino, ndipo musabzale mbewu pakati pa minga.+  Chitani mdulidwe wa mitima yanu pamaso pa Yehova,+ inu anthu a ku Yuda ndi okhala mu Yerusalemu. Chitani zimenezi kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto, pakuti ukatero udzayaka popanda munthu wozimitsa, chifukwa cha zochita zanu zoipa.”+  Nenani zimenezi mu Yuda anthu inu, ndipo zilengezeni ngakhale mu Yerusalemu.+ Fuulani ndi kuliza lipenga la nyanga ya nkhosa m’dziko lonse.+ Fuulani kuti: “Sonkhanani pamodzi, ndipo tiyeni tilowe m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+  Kwezani chizindikiro choloza njira ya ku Ziyoni. Thawirani kumalo otetezeka. Musaime chilili.” Chitani zimenezi chifukwa ndikubweretsa tsoka kuchokera kumpoto,+ ndithu ndikubweretsa tsoka lalikulu.  Wowonongayo akubwera ngati mkango umene ukutuluka paziyangoyango pamene umakhala.+ Amene akuwononga mitundu ya anthu wanyamuka.+ Wachoka m’malo ake kuti adzasandutse dziko lanu chinthu chodabwitsa. Mizinda yanu idzagwa ndi kukhala mabwinja moti sipadzapezeka wokhalamo.+  Pachifukwa chimenechi valani ziguduli,* anthu inu.+ Dzigugudeni pachifuwa ndi kulira mofuula,+ chifukwa mkwiyo woyaka moto wa Yehova sunatichokere.+  Yehova wanena kuti: “Zidzachitika pa tsikulo kuti mfumu sidzalimba mtima,+ chimodzimodzinso akalonga ake. Ansembe adzagwidwa ndi mantha ndipo aneneri adzadabwa.”+ 10  Pamenepo ndinanena kuti: “Kalanga ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Kunena zoona, mwapusitsa anthu awa+ ndiponso Yerusalemu mwa kunena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’+ koma lupanga lawabaya* mpaka mumtima.” 11  Pa nthawiyo adzauza anthu awa ndi Yerusalemu kuti: “M’njira zodutsidwadutsidwa za m’chipululu zopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga+ mukutuluka mphepo yotentha.+ Mphepo imeneyi si youluzira mankhusu* kapena yoyeretsera tirigu. 12  Mphepo yamphamvu ikuchokera m’njirazo kubwera kwa ine. Ine ndidzawauza ziweruzo zanga.+ 13  Taonani! Mdani adzabwera ngati mitambo yamvula ndipo magaleta* ake ali ngati mphepo yamkuntho.+ Mahatchi* ake ndi aliwiro kuposa ziwombankhanga.+ Tsoka ife chifukwa tafunkhidwa. 14  Tsuka mtima wako ndi kuchotsa zoipa zonse, iwe Yerusalemu, kuti upulumuke.+ Kodi maganizo ako oipawo udzakhala nawo mpaka liti?+ 15  Pakuti mawu akumveka kuchokera ku Dani+ ndipo akulengeza uthenga wopweteka kuchokera kudera lamapiri la Efuraimu.+ 16  Nenani zimenezi anthu inu. Nenani zimenezi kwa anthu a mitundu ina. Lengezani zimene zidzagwera Yerusalemu.” “Alonda akubwera kuchokera kudziko lakutali+ ndipo adzalengeza uthenga wa zimene zidzagwera mizinda ya Yuda. 17  Iwo akhala ngati alonda a kunja kwa mzinda ndipo azungulira Yerusalemu kumbali zonse+ kuti amuukire chifukwa chakuti wandipandukira,”+ watero Yehova. 18  “Udzalipira chifukwa cha khalidwe lako ndi zochita zako.+ Limeneli ndilo tsoka lako chifukwa zidzakhala zowawa. Zidzatero chifukwa kupanduka kwako kwalowerera mpaka mumtima.” 19  M’mimba mwanga ine, m’mimba mwanga! Ndikumva kupweteka kwambiri mumtima mwanga.+ Mtima wanga ukuvutika.+ Sindingathe kukhala chete pakuti ndamva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, chizindikiro chochenjeza cha nkhondo.+ 20  Alengeza za kuphwanya kosakaziratu pakuti dziko lonse lafunkhidwa.+ Mwadzidzidzi, mahema anga ndi nsalu za mahema angawo zafunkhidwa+ m’kanthawi kochepa. 21  Kodi ndiona chizindikirocho ndi kumva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosako kufikira liti?+ 22  Anthu anga ndi opusa.+ Iwo sanaganizire za ine.+ Iwo ndi ana opanda nzeru ndipo sazindikira kalikonse.+ Iwo ndi anzeru pa kuchita zoipa koma sadziwa kuchita zabwino.+ 23  Ndinaliona dzikolo, ndipo linali lopanda kanthu ndi lachabechabe.+ Ndinayang’ana kumwamba ndipo sikunali kuwala.+ 24  Ndinaona mapiri ndipo anali kugwedezeka. Zitunda zonse zinali kunjenjemera.+ 25  Ndinayang’anitsitsa koma sindinaone munthu aliyense. Ndipo zolengedwa zonse zouluka zinali zitathawa.+ 26  Ndinayang’anitsitsa ndipo ndinaona kuti munda wa zipatso unali utasanduka thengo. Mizinda yake yonse inali itagwetsedwa.+ Zimenezi zinachitika ndi dzanja la Yehova chifukwa cha mkwiyo wake woyaka moto. 27  Yehova wanena kuti: “Dziko lonseli lidzakhala bwinja+ ndipo ndidzawafafaniza.+ 28  Pachifukwa chimenechi dziko lidzalira+ ndipo kumwamba kudzachita mdima.+ Izi zili choncho chifukwa ndanena, ndaganiza zimenezi mozama, sindinadziimbe mlandu ndipo sindisintha maganizo anga.+ 29  Chifukwa cha phokoso la asilikali okwera pamahatchi ndiponso oponya mivi ndi uta, mzinda wonse ukuthawa.+ Alowa paziyangoyango ndi kuthawira m’matanthwe.+ Mumzinda uliwonse anthu athawamo ndipo palibe munthu amene akukhalamo.” 30  Iwe unali kuvala zovala zamtengo wapatali,* unali kudzikongoletsa ndi zokongoletsera zagolide ndipo unali kudzikongoletsa m’maso mwako ndi utoto wakuda.+ Tsopano utani popeza wafunkhidwa? Unali kutaya nthawi ndi kudzikongoletsa.+ Amene anali kukukhumba tsopano akukukana ndipo akufunafuna moyo wako.+ 31  Ine ndamva mawu ngati a mkazi amene akumva ululu. Ndamva ngati kubuula kwa mkazi amene akubereka mwana wake woyamba,+ koma ndi mawu a mwana wamkazi wa Ziyoni amene akupuma movutikira. Iye akutambasula manja ake+ ndi kulira kuti: “Tsoka ine, chifukwa ndatopa ndi anthu amene akufuna kundipha!”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “idzadzidalitsa yokha.”
Ena amati “masaka.”
Ena amati “kugwaza.”
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”
Mawu ake enieni, “zovala zofiira,” kutanthauza zovala zofiira zamtengo wapatali.